M’Cheyne Bible Reading Plan
Miriamu ndi Aaroni Atsutsana ndi Mose
12 Miriamu ndi Aaroni anayamba kuyankhula motsutsana ndi Mose chifukwa cha mkazi wa ku Kusi, popeza Moseyo anakwatira Mkusi. 2 Iwowo anafunsa kuti, “Kodi Yehova anayankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanayankhule kudzeranso mwa ife?” Ndipo Yehova anamva zimenezi.
3 (Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi).
4 Nthawi yomweyo Yehova anati kwa Mose, Aaroni ndi Miriamu, “Bwerani ku tenti ya msonkhano nonse atatu.” Ndipo atatuwo anapitadi kumeneko. 5 Tsono Yehova anatsika mu mtambo, nayima pa khomo la chihema. Kenaka anayitana Aaroni ndi Miriamu. Ndipo onse awiri atapita patsogolo, 6 Mulungu anati, “Mverani mawu anga:
“Pakakhala mneneri wa Yehova pakati panu,
ndimadzionetsera kwa iyeyo mʼmasomphenya,
ndimayankhula naye mʼmaloto.
7 Koma sinditero ndi Mose mtumiki wanga;
Iyeyu ndi wokhulupirika mʼnyumba yanga yonse.
8 Ndimayankhula naye maso ndi maso,
momveka bwino osati mophiphiritsa;
ndipo amaona maonekedwe a Yehova.
Nʼchifukwa chiyani simunaope
kuyankhula motsutsana ndi Mose mtumiki wanga?”
9 Ndipo Yehova anawakwiyira, nachoka.
10 Pamene mtambo unachoka pamwamba pa Chihema, taonani, Miriamu anagwidwa ndi khate. Aaroni atachewuka anaona Miriamu ali ndi khate; 11 ndipo Aaroni anawuza Mose kuti, “Pepani mbuye wanga, musatilange chifukwa cha tchimo limene tachita mopusa. 12 Musalole kuti Miriamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa kuchoka mʼmimba mwa amayi ake, thupi lake litawonongeka.”
13 Tsono Mose anafuwulira Yehova kuti, “Chonde Inu Mulungu, muchiritseni!”
14 Yehova anayankha Mose kuti, “Abambo ake akanamulavulira malovu mʼmaso, kodi sakanakhala wonyozeka masiku asanu ndi awiri? Mutsekereni kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri, kenaka mumulowetsenso.” 15 Choncho anamutsekera Miriamu kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri ndipo anthu sanayende ulendo wawo mpaka Miriamu atamulowetsanso.
16 Pambuyo pake anthu ananyamuka ku Heziroti ndi kukamanga mʼchipululu cha Parani.
Kukazonda Kanaani
13 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”
3 Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli. 4 Mayina awo ndi awa:
kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri;
5 kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori;
6 kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune;
7 kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe;
8 kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni;
9 kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu;
10 kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi;
11 kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi;
12 kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali;
13 kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli;
14 kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi;
15 kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki.
16 Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).
17 Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri. 18 Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri. 19 Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga? 20 Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).
21 Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati. 22 Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto). 23 Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu. 24 Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko. 25 Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija.
Kufotokoza Zomwe Anakaona
26 Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo. 27 Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi. 28 Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko. 29 Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.”
30 Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”
31 Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.” 32 Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali. 33 Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
49 Imvani izi anthu a mitundu yonse;
mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
2 anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,
olemera pamodzinso ndi osauka:
3 Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;
mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
4 Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,
ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.
5 Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,
pamene achinyengo oyipa andizungulira.
6 Iwo amene adalira kulemera kwawo
ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
7 Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake
kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
8 Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,
palibe malipiro amene angakwanire,
9 kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya
ndi kusapita ku manda.
10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;
opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka
ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,
malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,
ngakhale anatchula malo mayina awo.
12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,
adzafa ngati nyama.
13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,
ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula.
Sela
14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,
ndipo imfa idzawadya.
Olungama adzawalamulira mmawa;
matupi awo adzavunda mʼmanda,
kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;
ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.
16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,
pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,
ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,
ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,
amene sadzaonanso kuwala.
20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru
adzafa ngati nyama yakuthengo.
Phiri la Yehova
2 Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
2 Mʼmasiku otsiriza,
phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
3 Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,
“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,
ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
4 Iye adzaweruza pakati pa mayiko,
ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
kapena kuphunziranso za nkhondo.
5 Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,
tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
Tsiku la Yehova
6 Inu Yehova mwawakana anthu anu,
nyumba ya Yakobo.
Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa;
amawombeza mawula ngati Afilisti,
ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
7 Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide;
ndipo chuma chawo ndi chosatha.
Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo;
ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
8 Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano;
iwo amapembedza ntchito ya manja awo,
amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
9 Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa
ndi kutsitsidwa.
Inu Yehova musawakhululukire.
10 Lowani mʼmatanthwe,
bisalani mʼmaenje,
kuthawa kuopsa kwa Yehova
ndi ulemerero wa ufumu wake!
11 Kudzikuza kwa anthu kudzatha,
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa;
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
12 Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku
limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama,
ndipo adzagonjetsa
onse amphamvu,
13 tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali,
ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
14 tsiku la mapiri onse ataliatali
ndiponso la zitunda zonse zazitali,
15 tsiku la nsanja zonse zazitali
ndiponso malinga onse olimba,
16 tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi
ndiponso la mabwato onse okongola.
17 Kudzikuza kwa munthu kudzatha
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa,
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
18 ndipo mafano onse adzatheratu.
19 Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndi mʼmaenje a nthaka,
kuthawa mkwiyo wa Yehova,
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
20 Tsiku limenelo anthu adzatayira
mfuko ndi mileme
mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide,
amene anawapanga kuti aziwapembedza.
21 Adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka
kuthawa mkwiyo wa Yehova
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
22 Lekani kudalira munthu,
amene moyo wake sukhalira kutha.
Iye angathandize bwanji wina aliyense?
Yesu Nsembe ya Anthu Onse
10 Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. 2 Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. 3 Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. 4 Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.
5 Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,
“Simunafune nsembe kapena zopereka,
koma thupi munandikonzera.
6 Simunakondwere nazo nsembe zopsereza
ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.
7 Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,
Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”
8 Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. 9 Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.
11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
17 Ndipo akutinso:
“Sindidzakumbukiranso konse
machimo awo ndi zolakwa zawo.”
18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro
19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
26 Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27 Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28 Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29 Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30 Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31 Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
32 Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33 Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34 Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.
35 Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36 Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37 Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,
Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,
Ine sindidzakondwera naye.
39 Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.