Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 1

Kalembera

Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti, “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi. Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali. Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi. Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa:

Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,

Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,

Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,

Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,

Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,

10 Mwa ana a Yosefe:

kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi;

kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;

11 Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,

12 Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,

13 Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,

14 Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,

15 Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”

16 Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.

17 Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa, 18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi 19 monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:

20 Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 21 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.

22 Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 23 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.

24 Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 25 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.

26 Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 27 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.

28 Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 29 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.

30 Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 31 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.

32 Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe:

Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 33 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.

34 Kuchokera mwa zidzukulu za Manase:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 35 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.

36 Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 37 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.

38 Kuchokera mwa zidzukulu za Dani:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 39 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.

40 Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 41 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.

42 Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali:

Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 43 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.

44 Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake. 45 Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo. 46 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.

47 Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena. 48 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, 49 “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli. 50 Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo. 51 Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa. 52 Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake. 53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”

54 Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.

Masalimo 35

Salimo la Davide.

35 Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;
    mumenyane nawo amene akumenyana nane.
Tengani chishango ndi lihawo;
    dzukani ndipo bwerani mundithandize.
Tengani mkondo ndi nthungo,
    kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.
Uzani moyo wanga kuti,
    “Ine ndine chipulumutso chako.”

Iwo amene akufunafuna moyo wanga
    anyozedwe ndi kuchita manyazi;
iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke
    abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo
    pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera
    pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa
    ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa
    ukonde umene iwo abisa uwakole,
    agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova
    ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera,
    “Ndani angafanane nanu Yehova?
Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,
    osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”

11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
    zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
    ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
    ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14     ndinayendayenda ndi kulira maliro,
    kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
    kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
    ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
    Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
    anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
    Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
    moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
    pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.

19 Musalole adani anga onyenga
    akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
    andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
    koma amaganizira zonamizira
    iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
    Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”

22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
    Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
    Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
    Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”

26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
    achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
    avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
    afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
    Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
    ndi za matamando anu tsiku lonse.

Mlaliki 11

Kuponya Chakudya pa Madzi

11 Ponya chakudya chako pa madzi,
    udzachipezanso patapita masiku ambiri.
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
    pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.

Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,
    imagwetsa mvula pa dziko lapansi.
Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,
    ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
Amene amayangʼana mphepo sadzadzala;
    amene amayangʼana mitambo sadzakolola.

Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,
    kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,
momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,
    Mlengi wa zinthu zonse.

Dzala mbewu zako mmawa
    ndipo madzulo usamangoti manja lobodo,
pakuti sudziwa chimene chidzapindula,
    mwina ichi kapena icho,
    kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.

Kumbukira Mlengi Wako

Kuwala nʼkwabwino,
    ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
Munthu akakhala wa zaka zambiri,
    mulekeni akondwerere zaka zonsezo,
koma iye azikumbukira masiku a mdima,
    pakuti adzakhala ochuluka.
    Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.

Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,
    ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.
Tsatira zimene mtima wako ukufuna,
    ndiponso zimene maso ako akuona,
koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo
    Mulungu adzakuweruza.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,
    upewe zokupweteka mʼthupi mwako,
    pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.

Tito 3

Kuchita Ntchito Zabwino

Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino. Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera, Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu, kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.

Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake. 10 Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe. 11 Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.

Mawu Otsiriza

12 Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira. 13 Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. 14 Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.

15 Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro.

Chisomo chikhale ndi inu nonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.