M’Cheyne Bible Reading Plan
Kuwombola Zomwe ndi za Yehova
27 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati munthu anachita lumbiro lapadera loti adzapereka munthu mnzake kwa Yehova ndipo akufuna kuti amuwombole, 3 mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. 4 Ndipo ngati ndi wamkazi, mtengo wake ukhale masekeli makumi atatu. 5 Mtengo wa munthu wamwamuna wa zaka zapakati pa zisanu ndi makumi awiri ukhale masekeli makumi awiri ndipo munthu wamkazi ukhale masekeli khumi. 6 Ngati ndi munthu wamwamuna wa pakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, mtengo wa munthu wamwamuna ukhale masekeli asanu a siliva ndipo ngati ndi wamkazi, ukhale masekeli atatu a siliva. 7 Ngati ndi munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi kapena kuposerapo, mtengo wa wamwamuna ukhale masekeli khumi ndi asanu, ndipo wamkazi ukhale masekeli khumi. 8 Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira.
9 “ ‘Ngati chimene anachitira lumbiro kuti apereke ndi nyama imene amapereka kukhala nsembe kwa Yehova, zonse zimene amapereka kwa Yehova nʼzopatulika. 10 Munthu asasinthanitse ndi ina kapena kupereka ina yabwino mʼmalo mwa yoyipa, kapena yoyipa mʼmalo mwa yabwino. Ngati asinthitsa nyama ina mʼmalo mwa ina, nyamayo pamodzi ndi inzake wasinthitsayo zikhala zopatulika. 11 Ngati chimene anachitira lumbiro ndi nyama yodetsedwa, nyama imene siloledwa kuyipereka kukhala nsembe kwa Yehova, nyamayo abwere nayo kwa wansembe, 12 ndipo wansembeyo atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 13 Ngati mwini wakeyo akufuna kuwombola nyamayo, awonjezere pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu zamtengowo.
14 “ ‘Ngati munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 15 Ngati munthu amene wapereka nyumbayo afuna kuyiwombola nyumbayo, awonjezere pamtengo wake wa nyumbayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ndipo nyumbayo idzakhalanso yake.
16 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova mbali ina ya malo a makolo ake, mtengo umene awuyike ukhale wolingana ndi mtengo wa mbewu zimene zimadzabzalidwamo. Zikhale mbewu za barele za makilogalamu makumi awiri ndipo mtengo wake ukhale masekeli makumi asanu. 17 Ngati munthu apereka munda wake kuyambira chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mtengo wake ukhale umene unakhazikitsidwa. 18 Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo. 19 Ngati munthu amene wapereka munda afuna kuwuwombola, ayenera kuwonjezera pa mtengo wake wa mundawo, limodzi mwa magawo asanu a mtengowo. Ndipo mundawo udzakhalanso wake. 20 Koma ngati sawuwombola mundawo, kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzawomboledwanso. 21 Mwini mundawo akawusiya mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu ndiye kuti mundawo udzakhala wopatulika monga woperekedwa kwa Yehova: udzakhala munda wa ansembe.
22 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova munda umene anagula, umene si malo a makolo ake, 23 wansembe atchule mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo monga ndalama zopatulika kwa Yehova. 24 Pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene anawugulitsayo, amene malowo anali ake. 25 Potchula mtengo uliwonse wansembe awerengere molingana ndi mtengo wa sekeli wa ku Nyumba ya Mulungu: magera makumi awiri pa sekeli imodzi.
26 “ ‘Koma pasapezeke munthu wopereka mwana woyamba kubadwa wa nyama, popeza mwana woyamba kubadwa ali kale wa Yehova, kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, zimenezi ndi za Yehova. 27 Ngati ili nyama yodetsedwa, ayiwombole pa mtengo umene wansembe wawuyika, ndi kuwonjezeranso pa mtengo wake wa nyamayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ngati sayiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe awuyike.
28 “ ‘Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu, nyama, kaya ndi malo a makolo, chimenechi chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Choperekedwa kwa Yehova motere nʼchopatulika kwambiri.
29 “ ‘Munthu amene waperekedwa kotheratu sangawomboledwe. Munthuyo ayenera kuphedwa.
30 “ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova. 31 Ngati munthu afuna kuwombola chakhumi chilichonse, awonjezere pamtengo wake chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo. 32 Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova. 33 Palibe amene adzaloledwa kusankha nyama yomwe ili yabwino kapena kusinthitsa. Ngati asinthitsa, nyamayo pamodzi ndi inzakeyo zidzakhala zopatulika ndipo sangaziwombole.’ ”
34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anamupatsa Mose pa Phiri la Sinai kuti awuze Aisraeli.
Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka.
34 Ndidzayamika Yehova nthawi zonse;
matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
2 Moyo wanga udzanyadira Yehova;
anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine;
tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.
4 Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha;
anandilanditsa ku mantha anga onse.
5 Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira;
nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.
6 Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva;
Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
7 Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye
ndi kuwalanditsa.
8 Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;
wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
9 Wopani Yehova inu oyera mtima ake,
pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.
10 Mikango itha kulefuka ndi kumva njala
koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.
11 Bwerani ana anga, mundimvere;
ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.
12 Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake
ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,
13 asunge lilime lake ku zoyipa
ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
14 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
funafuna mtendere ndi kuwulondola.
15 Maso a Yehova ali pa olungama
ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;
16 nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa,
kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.
17 Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;
Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
18 Yehova ali pafupi kwa osweka mtima
ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
19 Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri,
Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
20 Iye amateteza mafupa ake onse,
palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.
21 Choyipa chidzapha anthu oyipa;
adani a olungama adzapezeka olakwa.
22 Yehova amawombola atumiki ake;
aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.
10 Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira,
choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
2 Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino,
koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
3 Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu,
zochita zake ndi zopanda nzeru
ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
4 Ngati wolamulira akukwiyira,
usachoke pa ntchito yako;
kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.
5 Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano,
kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
6 Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba,
pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
7 Ndaona akapolo atakwera pa akavalo,
pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
8 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha;
amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
9 Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo;
amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.
10 Ngati nkhwangwa ili yobuntha
yosanoledwa,
pamafunika mphamvu zambiri potema,
koma luso limabweretsa chipambano.
11 Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka
ngati njokayo yakuluma kale.
12 Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa,
koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
13 Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa;
potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
14 ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu.
Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo,
ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?
15 Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa;
ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.
16 Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana,
ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
17 Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka
ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake,
kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
18 Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka;
ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.
19 Phwando ndi lokondweretsa anthu,
ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo,
koma ndalama ndi yankho la chilichonse.
20 Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako,
kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako,
pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako
nʼkukafotokoza zomwe wanena.
Malangizo Osiyanasiyana
2 Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. 2 Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.
3 Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. 4 Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. 5 Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
6 Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. 7 Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako. 8 Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.
9 Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10 kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.
11 Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. 12 Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, 13 pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu, 14 amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
15 Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.