M’Cheyne Bible Reading Plan
Zilango za Tchimo
20 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala. 3 Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera. 4 Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha, 5 Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”
6 “ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.
7 “ ‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8 Ndipo sungani malangizo anga ndi kuwatsata. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani.
9 “ ‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake.
10 “ ‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa.
11 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake.
12 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
13 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
14 “ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu.
15 “ ‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo.
16 “ ‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
17 “ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango.
18 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo.
19 “ ‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu.
20 “ ‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana.
21 “ ‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana.
22 “ ‘Nʼchifukwa chake muzisunga malangizo anga onse ndi malamulo anga ndipo muwatsatire kuti ku dziko limene Ine ndikupita nanu kuti mukakhalemo lisakakusanzeni. 23 Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo. 24 Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25 “ ‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu. 26 Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga.
27 “ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”
Salimo la Davide.
25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
2 Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
kapena kuti adani anga andipambane.
3 Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
4 Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
phunzitseni mayendedwe anu;
5 tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
6 Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
pakuti ndi zakalekale.
7 Musakumbukire machimo a ubwana wanga
ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
9 Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,
khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?
Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,
ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;
amawulula pangano lake kwa iwowo.
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,
pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,
pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;
masuleni ku zowawa zanga.
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga
ndipo mufafanize machimo anga onse.
19 Onani mmene adani anga achulukira
ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
musalole kuti ndichite manyazi,
pakuti ndimathawira kwa Inu.
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.
22 Wombolani Israeli Inu Mulungu,
ku mavuto ake onse!
Chilichonse Chili ndi Nthawi
3 Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,
ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
2 Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,
nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
3 Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,
nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
4 Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,
nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,
nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
6 Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,
nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
7 Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,
nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
8 Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,
nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.
9 Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? 10 Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu. 11 Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro. 12 Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo. 13 Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa. 14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
15 Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,
ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba;
Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.
16 Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano:
ku malo achiweruzo, kuyipa mtima kuli komweko,
ku malo achilungamo, kuyipa mtima kuli komweko.
17 Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti;
“Mulungu adzaweruza
olungama pamodzi ndi oyipa omwe,
pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse,
nthawi ya ntchito iliyonse.”
18 Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama. 19 Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake. 20 Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko. 21 Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”
22 Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?
Malangizo kwa Amayi Amasiye, Akulu Ampingo ndi Akapolo
5 Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako. 2 Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.
3 Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha. 4 Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu. 5 Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza. 6 Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo. 7 Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa. 8 Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.
9 Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha. 10 Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.
11 Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso. 12 Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba. 13 Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba. 14 Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza 15 Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana.
16 Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha.
17 Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. 18 Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” 19 Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu. 20 Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo.
21 Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.
22 Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako.
23 Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.
24 Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo. 25 Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingatheke kubisika.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.