Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 17

Za Kusadya Magazi

17 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza Aaroni ndi ana ake, pamodzi ndi Aisraeli onse kuti, ‘Chimene Yehova walamula ndi ichi: Mwisraeli aliyense amene apha ngʼombe, mwana wankhosa kapena mbuzi mu msasa kapena kunja kwa msasa, mʼmalo mobwera nayo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova ndi kuyipereka kuti ikhale nsembe ya Yehova, ameneyo wapalamula mlandu wa magazi, wakhetsa magazi ndipo ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake. Izi zili choncho kuti Aisraeli azibwera ndi nyama zawo za nsembe zimene akanaphera ku malo kwina kulikonse. Aisraeli azibwera nazo nyamazo kwa Yehova, kwa wansembe wokhala pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo aziphere pomwepo kuti zikhale nsembe za chiyanjano. Wansembe awaze magazi ake pa guwa la Yehova limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo atenthe mafuta ake kuti atulutse fungo lokomera Yehova. Motero asadzapherenso nsembe fano la mbuzi limene amachita nalo zadama. Limeneli ndi lamulo la muyaya kwa iwo ndi mibado ya mʼtsogolo.’ ”

“Uwawuze kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo amene amakhala pakati pawo akapereka nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse popanda kubwera nayo pa khomo la tenti ya msonkhano kudzayipereka pamaso pa Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’ ”

10 “Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene adya magazi, ndidzamufulatira ndipo ndidzamuchotsa pakati pa anthu anzake. 11 Pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi, ndipo ndawupereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amachotsa machimo chifukwa moyo uli mʼmenemo. 12 Choncho ndikuwawuza Aisraeli kuti, ‘Pasapezeke aliyense wa inu wodya magazi, ngakhale mlendo wokhala pakati panu.’ ”

13 “Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala pakati panu amene amasaka ndi kupha nyama zakuthengo kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuwakwirira ndi dothi, 14 chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi ake. Nʼchifukwa chake ndinawawuza Aisraeli kuti, ‘Musamadye magazi a cholengedwa chilichonse, chifukwa moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.

15 “ ‘Munthu aliyense, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, amene amadya chilichonse chofa chokha, kapena chojiwa ndi zirombo, achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Kenaka adzakhala woyeretsedwa. 16 Koma ngati sachapa zovala zake ndi kusamba, adzasenzabe machimo ake.’ ”

Masalimo 20-21

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
    dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
    akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Iye akumbukire nsembe zako zonse
    ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
            Sela
Akupatse chokhumba cha mtima wako
    ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
    ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
    Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
    ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
    koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
    koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
    Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
    chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
    ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
            Sela
Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
    ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
    masiku ochuluka kwamuyaya.
Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
    Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
    Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
Pakuti mfumu imadalira Yehova;
    kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
    iyo sidzagwedezeka.

Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
    dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
Pa nthawi ya kuonekera kwanu
    mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
    ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
    zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
    sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
    pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
    ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

Miyambo 31

Mawu a Mfumu Lemueli

31 Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:

Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga?
    Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?
Usapereke mphamvu yako kwa akazi.
    Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.

Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu,
    mafumu sayenera kumwa vinyo.
    Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa
kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko,
    nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.
Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa,
    vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
amwe kuti ayiwale umphawi wawo
    asakumbukirenso kuvutika kwawo.

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha.
    Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.
Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo.
    Uwateteze amphawi ndi osauka.

Mathero: Mkazi Wangwiro

10 Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani?
    Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
11 Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira
    ndipo mwamunayo sasowa phindu.
12 Masiku onse a moyo wake
    mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
13 Iye amafunafuna ubweya ndi thonje;
    amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda,
    amakatenga chakudya chake kutali.
15 Iye amadzuka kusanache kwenikweni;
    ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya
    ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
16 Iye amalingalira za munda ndi kuwugula;
    ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
17 Iye amavala zilimbe
    nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
18 Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu,
    choncho nyale yake sizima usiku wonse.
19 Iye amadzilukira thonje
    ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
20 Iye amachitira chifundo anthu osauka
    ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
21 Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu;
    pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
22 Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake;
    amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
23 Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda,
    ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
24 Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa;
    amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
25 Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake;
    ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
26 Iye amayankhula mwanzeru,
    amaphunzitsa anthu mwachikondi.
27 Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake
    ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
28 Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;
    ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
29 “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana
    koma iwe umawaposa onsewa.”
30 Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa;
    koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
31 Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita
    ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.

1 Timoteyo 2

Malangizo Achipembedzo

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi. Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu. Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera. Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.

Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.

Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. 10 Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.

11 Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu. 12 Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete. 13 Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava. 14 Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa. 15 Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.