Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 15

Zonyansa Zotuluka Mʼthupi

15 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, “Yankhulani ndi Aisraeli ndipo muwawuze kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zotulukazo ndi zonyansa ndithu. Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa:

“ ‘Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonapo, ndiponso chinthu chilichonse chimene akhalepo chidzakhala chodetsedwa. Aliyense wokhudza bedi la munthuyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense wokhala pa chinthu chimene munthu wotulutsa mafinyayo anakhalapo, achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

“ ‘Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akutulutsa mafinyayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

“ ‘Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu munthu wina amene ndi woyeretsedwa, munthu ameneyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

“ ‘Chilichonse chimene munthuyo akhalira akakwera pa kavalo chidzakhala chodetsedwa. 10 Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

11 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

12 “ ‘Mʼphika wadothi umene munthu wotulutsa mafinyayo wakhudza awuphwanye, ndipo chiwiya chilichonse chamtengo achitsuke ndi madzi.

13 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa. 14 Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe. 15 Wansembe apereke zimenezo: imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wotulutsa mafinya uja pamaso pa Yehova.

16 “ ‘Mwamuna akataya pansi mbewu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 17 Chovala chilichonse kapena chikopa chilichonse pomwe pagwera mbewu yaumunayo achichape, komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo. 18 Mwamuna akagona ndi mkazi wake nataya mbewu yake yaumuna, onse awiriwo asambe. Komabe adzakhala odetsedwa mpaka madzulo.

19 “ ‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

20 “ ‘Chilichonse chimene mkaziyo agonera pa nthawi yake yosamba chidzakhala chodetsedwa, ndipo chilichonse chimene adzakhalira chidzakhalanso chodetsedwa. 21 Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Aliyense wokhudza chimene wakhalapo achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23 Kaya ndi bedi kapena chinthu china chilichonse chimene anakhalapo, ngati munthu wina akhudza chinthucho, munthuyo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

24 “ ‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa.

25 “ ‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. 26 Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba. 27 Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

28 “ ‘Nthawi yosamba ikatha, mkaziyo awerenge masiku asanu ndi awiri, ndipo masikuwo akatha adzakhala woyeretsedwa. 29 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano. 30 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja.

31 “ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ”

32 Amenewa ndi malamulo a munthu amene akutuluka mafinya kumaliseche kwake, komanso a munthu aliyense amene wadetsedwa ndi mbewu yaumuna, 33 mkazi wodwala chifukwa cha msambo komanso a mwamuna kapena mkazi amene akutulutsa mafinya kumaliseche kwake ndi mwamuna wogona ndi mkazi amene akusamba.

Masalimo 18

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.

18 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.

Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;
    Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.
    Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
    ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

Zingwe za imfa zinandizinga;
    mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
    misampha ya imfa inalimbana nane.
Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
    ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.
Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;
    kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,
    ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;
    ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;
    moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,
    makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
Iye anangʼamba thambo natsika pansi;
    pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
10 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;
    nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
11 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,
    chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.
12 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala,
    makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.
13 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,
    mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
14 Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,
    ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
15 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera;
    maziko a dziko lapansi anakhala poyera,
Yehova atabangula mwaukali,
    pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.

16 Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;
    anandivuwula mʼmadzi ozama.
17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
    adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.
18 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,
    koma Yehova anali thandizo langa.
19 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;
    anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
    molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
    ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
    sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
    ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
    molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.

25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
    kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
    koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
    koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
    Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
    ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
    mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
    kwa onse amene amathawira kwa Iye.
31 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
    Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
32 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu
    ndi kulungamitsa njira yanga.
33 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;
    Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
34 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
    manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
35 Inu mumandipatsa chishango chachipambano,
    ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;
    mumawerama pansi kundikuza.
36 Munakulitsa njira yoyendamo ine,
    kuti mapazi anga asaguluke.

37 Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira;
    sindinabwerere mpaka atawonongedwa.
38 Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka;
    anagwera pa mapazi anga.
39 Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo,
    munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.
40 Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa,
    ndipo ine ndinawononga adani angawo.
41 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.
    Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
42 Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.
    Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;
    mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
    Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
    akangomva za ine amandigonjera.
45 Iwo onse anataya mtima;
    anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!
    Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
    amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
48     amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
    munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;
    ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;
    amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,
    kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.

Miyambo 29

29 Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri,
    adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.

Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa,
    koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.

Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake,
    koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo,
    koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.

Munthu woshashalika mnzake,
    akudziyalira ukonde mapazi ake.

Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake,
    koma wochita chilungamo amayimba lokoma.

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka,
    koma woyipa salabadira zimenezi.

Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda,
    koma anthu anzeru amaletsa ukali.

Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru,
    chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.

10 Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro
    koma anthu olungama amasamalira moyo wake.

11 Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake,
    koma munthu wanzeru amadzigwira.

12 Ngati wolamulira amvera zabodza,
    akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.

13 Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti:
    Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.

14 Ngati mfumu iweruza osauka moyenera,
    mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.

15 Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru
    koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

16 Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka,
    koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.

17 Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere
    ndi kusangalatsa mtima wako.

18 Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo;
    koma wodala ndi amene amasunga malamulo.

19 Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi;
    ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.

20 Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo
    kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.

21 Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana,
    potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.

22 Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano,
    ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

23 Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,
    koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

24 Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe;
    amalumbira koma osawulula kanthu.

25 Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha,
    koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima,
    koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.

27 Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo;
    koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.

2 Atesalonika 3

Tipempherereni

Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.

Awachenjeza za Kusagwira Ntchito

Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”

11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.

14 Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15 Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.

Malonje Otsiriza

16 Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

17 Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.

18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.