M’Cheyne Bible Reading Plan
Kuyeretsedwa ku Nthenda ya Khate
14 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe. 3 Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira, 4 wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope. 5 Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino. 6 Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino. 7 Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
8 “Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri. 9 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
10 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. 11 Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
12 “Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula. 13 Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana. 14 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 15 Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere, 16 aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 17 Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja. 18 Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.
19 “Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza 20 ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.
21 “Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. 22 Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
23 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe. 24 Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25 Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 26 Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere, 27 ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 28 Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula. 29 Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova. 30 Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, 31 imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.
32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.
Za Ndere za Mʼnyumba
33 “Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 34 Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo, 35 mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’ 36 Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo. 37 Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma, 38 wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri. 39 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo, 40 wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda. 41 Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi. 42 Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.
43 “Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso, 44 wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa. 45 Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.
46 “Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 47 Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.
48 “Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha. 49 Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope. 50 Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi. 51 Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri 52 Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira. 53 Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
54 Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa, 55 nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba, 56 khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga 57 kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa.
Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.
Pemphero la Davide.
17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
2 Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
maso anu aone chimene ndi cholungama.
3 Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
4 Kunena za ntchito za anthu,
monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
posatsata njira zachiwawa.
5 Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
mapazi anga sanaterereke.
6 Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
7 Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
8 Mundisunge ine ngati mwanadiso;
mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
9 kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.
Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.
28 Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,
koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.
2 Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,
koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.
3 Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake
ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.
4 Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,
koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.
5 Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,
koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.
6 Munthu wosauka wa makhalidwe abwino
aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.
7 Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,
koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.
8 Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka
amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.
9 Wokana kumvera malamulo
ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.
10 Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa
adzagwera mu msampha wake womwe,
koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.
11 Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru,
koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.
12 Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu;
koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.
13 Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,
koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.
14 Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse,
koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.
15 Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa
ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.
16 Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza
koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.
17 Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu
adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake;
wina aliyense asamuthandize.
18 Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa
koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.
19 Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka,
koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.
20 Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri,
koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
21 Kukondera si kwabwino,
ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.
22 Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera
koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.
23 Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake
mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.
24 Amene amabera abambo ake kapena amayi ake
namanena kuti “kumeneko sikulakwa,”
ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.
25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,
koma amene amadalira Yehova adzalemera.
26 Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru,
koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.
27 Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu,
koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.
28 Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala,
koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.
Kubwera kwa Munthu Woyipitsitsa
2 Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani 2 kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale. 3 Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo. 4 Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi? 6 Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera. 7 Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe. 8 Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake. 9 Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo. 10 Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe. 11 Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza. 12 Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.
Imani Mwamphamvu
13 Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi. 14 Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. 15 Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.
16 Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, 17 akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.