M’Cheyne Bible Reading Plan
Chakudya Choyeretsedwa ndi Chodetsedwa
11 Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, 2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: 3 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.
4 “ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 5 Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 6 Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye. 7 Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 8 Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa.
9 “ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu. 11 Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu.
13 “ ‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 14 nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, 15 akhungubwi a mitundu yonse, 16 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi 17 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, dembo, 19 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
20 “ ‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. 21 Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira. 22 Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. 23 Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu.
24 “ ‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 25 Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
26 “ ‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa. 27 Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28 Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.
29 “ ‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse, 30 gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe. 31 Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 32 Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa. 33 Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo. 34 Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa. 35 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa. 36 Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa. 37 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino. 38 Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu.
39 “ ‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 40 Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
41 “ ‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya. 42 Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa. 43 Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa. 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.
46 “ ‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa. 47 Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’ ”
Kudziyeretsa kwa Mkazi Atabala Mwana
12 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba. 3 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe. 4 Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha. 5 Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.
6 “ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 7 Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake.
“ ‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi. 8 Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
13 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga
ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
Mpaka liti adani anga adzandipambana?
3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
Walitsani maso anga kuti ndingafe;
4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
6 Ine ndidzayimbira Yehova
pakuti wandichitira zokoma.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
14 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
“Kulibe Mulungu.”
Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa;
palibe amene amachita zabwino.
2 Yehova kumwamba wayangʼana pansi,
kuyangʼana anthu onse
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
amene amafunafuna Mulungu.
3 Onse atembenukira kumbali,
onse pamodzi asanduka oyipa;
palibe amene amachita zabwino,
palibiretu ndi mmodzi yemwe.
4 Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse?
Akudya anthu anga ngati chakudya chawo
ndipo satamanda Yehova?
5 Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu,
pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.
6 Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka,
koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.
7 Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni!
Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake,
Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!
26 Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola,
ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.
2 Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira,
ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.
3 Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu,
choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.
4 Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.
5 Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.
6 Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga
kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.
7 Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
8 Kupereka ulemu kwa chitsiru
zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.
9 Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
10 Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda,
ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.
11 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake
chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.
12 Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo
kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.
13 Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango,
mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”
14 Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake,
momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.
15 Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale;
zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.
16 Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru
kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.
17 Munthu wongolowera mikangano imene si yake
ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.
18 Monga munthu wamisala amene
akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
19 ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake,
amene amati, “Ndimangoseka chabe!”
20 Pakasowa nkhuni, moto umazima;
chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.
21 Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto,
ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.
22 Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma;
chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.
23 Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi
ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
24 Munthu wachidani amayankhula zabwino
pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
25 Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire,
pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
26 Ngakhale amabisa chidani mochenjera,
koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.
27 Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha;
ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.
28 Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,
ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.
Tsiku la Ambuye
5 Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, 2 chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. 3 Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
4 Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. 5 Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. 6 Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. 7 Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. 8 Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. 9 Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 10 Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. 11 Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
Malangizo Otsiriza
12 Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. 13 Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. 14 Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20 Musanyoze mawu a uneneri. 21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.
23 Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. 24 Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.
25 Abale, mutipempherere. 26 Perekani moni wachikondi kwa onse. 27 Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.
28 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.