M’Cheyne Bible Reading Plan
6 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, 3 kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, 4 ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo 5 kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. 6 Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo. 7 Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.”
Nsembe Yopsereza
8 Yehova anawuza Mose kuti, 9 “Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. 11 Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando. 12 Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo. 13 Moto uzikhala ukuyaka pa guwa nthawi zonse ndipo usazimepo.
Nsembe Zachakudya
14 “ ‘Lamulo la nsembe yachakudya ndi ili: ana a Aaroni azibwera nayo nsembeyo pamaso pa Yehova, patsogolo pa guwa. 15 Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova. 16 Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano. 17 Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo. 18 Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ”
19 Yehova anawuzanso Mose kuti, 20 “Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo. 21 Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova. 22 Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera. 23 Nsembe iliyonse yachakudya ya wansembe izitenthedwa kwathunthu, isamadyedwe.”
Nsembe Yopepesera Tchimo
24 Yehova anawuza Mose kuti 25 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika. 26 Wansembe amene apereke nsembeyi adyere ku malo wopatulika ndiye kuti mʼbwalo la tenti ya msonkhano. 27 Chilichonse chimene chidzakhudza nsembeyo chidzakhala chopatulika, ndipo ngati magazi ake agwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo opatulika. 28 Mʼphika wadothi umene aphikira nyamayo auphwanye. Koma ngati yaphikidwa mu mʼphika wa mkuwa, awukweche ndi kuwutsukuluza ndi madzi. 29 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kuyidya popeza nsembeyi ndi yopatulika kwambiri. 30 Koma nsembe yopepesera tchimo imene magazi ake amabwera nawo mu tenti ya msonkhano kudzachita mwambo wopepesera tchimo ku malo opatulika isadyedwe, mʼmalo mwake itenthedwe.’ ”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide.
5 Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova,
ganizirani za kusisima kwanga
2 Mverani kulira kwanga kofuna thandizo,
Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
3 Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;
Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu
ndi kudikira mwachiyembekezo.
4 Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa;
choyipa sichikhala pamaso panu.
5 Onyada sangathe kuyima pamaso panu;
Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
6 Mumawononga iwo amene amanena mabodza;
anthu akupha ndi achinyengo,
Yehova amanyansidwa nawo.
7 Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu,
ndidzalowa mʼNyumba yanu;
mwa ulemu ndidzaweramira pansi
kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
8 Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu
chifukwa cha adani anga ndipo
wongolani njira yanu pamaso panga.
9 Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike;
mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko.
Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;
ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
10 Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu!
Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo.
Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri,
pakuti awukira Inu.
11 Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere;
lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe.
Aphimbeni ndi chitetezo chanu,
iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
12 Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama;
mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
kapena kundilanga mu ukali wanu.
2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;
Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.
Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;
Amakutamandani ndani ali ku manda?
6 Ine ndatopa ndi kubuwula;
usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;
ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;
akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,
pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;
Yehova walandira pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;
adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
21 Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova;
Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
2 Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo,
koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
3 Za chilungamo ndi zolondola
ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
4 Maso odzikuza ndi mtima wonyada,
zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
5 Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake;
koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
6 Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa
ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7 Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga,
pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
8 Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota,
koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
9 Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba,
kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10 Munthu woyipa amalakalaka zoyipa;
sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
11 Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru;
koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
12 Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova,
ndipo Iye adzawononga woyipayo.
13 Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira,
nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
14 Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo,
ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
15 Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala,
koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
16 Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru
adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
17 Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi,
ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama
ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
19 Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu
kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
20 Munthu wanzeru samwaza chuma chake,
koma wopusa amachiwononga.
21 Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika,
amapeza moyo ndi ulemerero.
22 Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu
ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
23 Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake
sapeza mavuto.
24 Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,”
iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
25 Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha
chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
26 Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri,
koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
27 Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova,
nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
28 Mboni yonama idzawonongeka,
koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
29 Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima,
koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
30 Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu,
zimene zingapambane Yehova.
31 Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo,
koma ndi Yehova amene amapambanitsa.
4 Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.
Malangizo Ena
2 Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. 3 Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. 4 Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. 5 Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. 6 Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.
Mawu Otsiriza
7 Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. 8 Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. 9 Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.
10 Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). 11 Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. 12 Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. 13 Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. 14 Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. 15 Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.
16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.
17 Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”
18 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.