Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 39

Zovala za Ansembe

39 Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.

Chovala cha Efodi

Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa. Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo. Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose.

Chovala Chapachifuwa

Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. 10 Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili; 11 mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; 12 mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti; 13 mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide. 14 Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

15 Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. 16 Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa. 17 Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. 18 Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. 19 Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. 20 Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. 21 Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose.

Zovala zina za Unsembe

22 Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso. 23 Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. 24 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo. 25 Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo. 26 Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose.

27 Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso, 28 nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino. 29 Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose.

30 Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, wopatulikira Yehova. 31 Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Mose Ayendera Chihema

32 Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 33 Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 34 chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba; 35 bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake; 36 tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 37 choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo; 38 guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti; 39 guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake; 40 nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano; 41 ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.

42 Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 43 Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.

Yohane 18

Amugwira Yesu

18 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.

Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.

Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.”

Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo). Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.

Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?”

Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”

Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.” Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”

10 Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).

11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”

Amutengera Yesu kwa Anasi

12 Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. 13 Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho. 14 Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu.

Petro Akana Yesu Koyamba

15 Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe 16 koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro.

17 Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?”

Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”

18 Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.

Mkulu wa Ansembe Amufunsa Yesu

19 Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake.

20 Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri. 21 Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.”

22 Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?”

23 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?” 24 Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.

Petro Akana Yesu Kachiwiri ndi Kachitatu

25 Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?”

Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”

26 Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?” 27 Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira.

Yesu ku Bwalo la Pilato

28 Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska. 29 Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?”

30 Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.”

31 Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.”

Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.” 32 Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe.

33 Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?”

34 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?”

35 Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”

36 Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”

37 Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!”

Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”

38 Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye. 39 Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’ ”

40 Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.

Miyambo 15

15 Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo,
    koma mawu ozaza amautsa ukali.

Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru,
    koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.

Maso a Yehova ali ponseponse,
    amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.

Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo,
    koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.

Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake,
    koma wochenjera amasamala chidzudzulo.

Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri,
    zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.

Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru;
    koma mitima ya zitsiru sitero.

Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova,
    koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.

Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova
    koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.

10 Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa.
    Odana ndi chidzudzulo adzafa.

11 Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova,
    nanji mitima ya anthu!

12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa;
    iye sapita kwa anthu anzeru.

13 Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe,
    koma mtima wosweka umawawitsa moyo.

14 Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru,
    koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.

15 Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa,
    koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.

16 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova,
    kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.

17 Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi,
    kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.

18 Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano,
    koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.

19 Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga,
    koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.

20 Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
    koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.

21 Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru,
    koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.

22 Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka,
    koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.

23 Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera,
    ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.

24 Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo
    kuti apewe malo okhala anthu akufa.

25 Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada
    koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.

26 Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova,
    koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.

27 Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake,
    koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.

28 Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire,
    koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.

29 Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa,
    koma amamva pemphero la anthu olungama.

30 Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima
    ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.

31 Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo
    adzakhala pakati pa anthu anzeru.

32 Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha,
    koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.

33 Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,
    ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.

Afilipi 2

Kutsanzira Kudzichepetsa kwa Khristu

Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:

Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,
    sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
Koma anadzichepetsa kotheratu
    nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo
    ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
Ndipo pokhala munthu choncho
    anadzichepetsa yekha
    ndipo anamvera mpaka imfa yake,
        imfa yake ya pamtanda!
Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,
    ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,
    kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye
    kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Kuwala monga Nyenyezi

12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera, 13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.

14 Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo, 15 kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba 16 powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe. 17 Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse. 18 Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi.

Timoteyo ndi Epafrodito

19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu. 20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu. 21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake. 23 Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere. 24 Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa.

25 Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga. 26 Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala. 27 Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke. 28 Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe. 29 Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu. 30 Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.