M’Cheyne Bible Reading Plan
36 1 Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.”
2 Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito. 3 Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse. 4 Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo 5 ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.”
6 Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, 7 chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse.
Chihema
8 Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi. 9 Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. 10 Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. 11 Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. 12 Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. 13 Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi.
14 Iwo anapanga nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zinalipo khumi ndi imodzi. 15 Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri. 16 Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso. 17 Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 18 Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 19 Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
20 Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 21 Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69. 22 Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri. Iwo anapanga maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 23 Anapanga maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho, 24 ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 25 Iwo anapanganso maferemu makumi awiri a mbali yakumpoto ya chihemacho, 26 ndiponso matsinde makumi anayi asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 27 Anapanganso maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo, 28 ndiponso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 29 Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana. 30 Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse.
31 Iwo anapanganso mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha. Mitanda isanu inali ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 32 mitanda isanu inanso inali ya maferemu a mbali inayo ndipo mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 33 Anapanga mtanda wapakati omwe umachokera pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 34 Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide.
35 Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi. 36 Iwo anapanga nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide. Anapanganso ngowe zagolide za nsanamirazo ndi matsinde asiliva anayi. 37 Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 38 Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa.
Mpesa ndi Nthambi
15 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2 Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4 Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
5 “Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6 Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7 Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8 Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
9 “Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’
Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu
18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’
Ntchito ya Mzimu Woyera
26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”
12 Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu,
koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
2 Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova,
koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
3 Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa,
koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
4 Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake,
koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
5 Maganizo a anthu olungama ndi owongoka,
koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
6 Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa,
koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
7 Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika,
koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
8 Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake,
koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
9 Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika,
kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
10 Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake,
koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
11 Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka,
koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
12 Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa,
koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
13 Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa;
koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
14 Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake
ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
15 Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino,
koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
16 Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo,
koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
17 Woyankhula zoona amapereka umboni woona,
koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
18 Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga,
koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
19 Mawu woona amakhala mpaka muyaya
koma mawu abodza sakhalitsa.
20 Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo;
koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
21 Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama,
koma munthu woyipa mavuto samuthera.
22 Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova,
koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
23 Munthu wochenjera amabisa nzeru zake,
koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
24 Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira,
koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
25 Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu,
koma mawu abwino amamusangalatsa.
26 Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake,
koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
27 Munthu waulesi sapeza chimene akufuna,
koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
28 Mʼnjira yachilungamo muli moyo;
koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.
5 Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. 2 Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.
3 Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. 4 Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. 5 Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. 6 Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. 7 Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.
8 Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika 9 (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti,
“Dzuka, wamtulo iwe,
uka kwa akufa,
ndipo Khristu adzakuwalira.”
15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. 17 Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. 18 Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. 19 Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. 20 Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Malangizo kwa Akazi ndi Amuna Mʼbanja
21 Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.
22 Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. 23 Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. 24 Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.
25 Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo 26 kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. 27 Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. 28 Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. 29 Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake 30 pakuti ndife ziwalo za thupi lake. 31 “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 32 Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. 33 Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.