M’Cheyne Bible Reading Plan
Miyala ina Yatsopano
34 Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. 2 Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. 3 Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”
4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. 5 Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. 6 Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, 7 waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.”
8 Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. 9 Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.”
10 Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni. 11 Mverani zimene ndikukulamulirani lero. Ine ndidzathamangitsa pamaso panu Aamori, Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi. 12 Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu. 13 Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. 14 Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.
15 “Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. 16 Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi.
17 “Musadzipangire milungu yosungunula.
18 “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto.
19 “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. 20 Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna.
“Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake.
21 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma.
22 “Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka. 23 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. 24 Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse.
25 “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa.
26 “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu.
“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.”
27 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” 28 Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.
Nkhope ya Mose Inyezimira
29 Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. 30 Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. 31 Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. 32 Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai.
33 Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. 34 Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, 35 iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.
Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake
13 Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.
2 Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. 3 Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; 4 anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. 5 Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
6 Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”
7 Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”
8 Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”
9 Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”
10 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” 11 Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.
12 Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13 Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14 Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15 Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17 Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
18 “Ine sindikunena za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndinawasankha. Koma izi zikukwaniritsa malemba: ‘Iye amene akudya nawo chakudya changa, ndiye amene anandiwukira.’
19 “Ine ndikukuwuzani tsopano zisanachitike zimenezi, kuti pamene zachitika, mudzakhulupirire kuti Ine Ndine. 20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene alandira amene Ine ndamutuma, alandiranso Ine. Aliyense amene alandira Ine, alandiranso amene anandituma.”
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
21 Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”
22 Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. 23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. 24 Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”
25 Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”
26 Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. 27 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.
Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” 28 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. 29 Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. 30 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32 Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.
33 “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.
34 “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35 Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”
36 Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?”
Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”
37 Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”
38 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”
Miyambo ya Solomoni
10 Miyambo ya Solomoni:
Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
2 Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa,
koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3 Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala;
koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
4 Wochita zinthu mwaulesi amasauka,
koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
5 Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru,
koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
6 Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama,
koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
7 Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso,
koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
8 Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo,
koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
9 Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;
koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
10 Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto,
koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
11 Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo,
koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
12 Udani umawutsa mikangano,
koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13 Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu,
koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
14 Anzeru amasunga chidziwitso
koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
15 Chuma cha munthu wolemera
ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
16 Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama,
koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
17 Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,
koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
18 Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama,
ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
19 Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,
koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
20 Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri,
koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
21 Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri;
koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
22 Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma,
ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23 Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa,
koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
24 Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira;
chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
25 Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa,
koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
26 Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso,
ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo;
koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
28 Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe,
koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
29 Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino,
koma wochita zoyipa adzawonongeka.
30 Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake
koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
31 Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru,
koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula,
koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.
Paulo Mlaliki wa Anthu a Mitundu Ina
3 Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.
2 Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu, 3 ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule. 4 Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu, 5 chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri. 6 Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.
7 Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu. 8 Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu. 9 Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. 10 Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. 11 Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 12 Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima. 13 Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu.
Paulo Apempherera Aefeso
14 Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate, 15 amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo. 16 Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, 17 kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi 18 kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. 19 Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.
20 Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, 21 Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.