M’Cheyne Bible Reading Plan
Mwambo Wopatula Ansembe
29 “Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema. 2 Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu. 3 Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija. 4 Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. 5 Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. 6 Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. 7 Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza. 8 Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro 9 ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha.
“Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.
10 “Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake. 11 Uphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 12 Utenge magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chako pa nyanga zaguwa lansembe ndipo magazi otsalawo uwakhutulire pa tsinde laguwalo. 13 Kenaka utenge mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake. Zonsezi uzitenthe pa guwapo. 14 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake uziwotche kunja kwa msasa. Iyi ndi nsembe yopepesera machimo.
15 “Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 16 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo. 17 Uyidule nkhosayo nthulinthuli, kutsuka matumbo ake ndi miyendo yake. Ukatero, pamodzi ndi mutu wake, uziyike pamwamba pa nthulizo. 18 Ndipo uwotche nkhosa yonseyo pa guwa lansembe. Iyi ndi nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ili ndi fungo lokoma, loperekedwa pa moto kwa Yehova.
19 “Utenge nkhosa yayimuna ina ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 20 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 21 Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo.
22 “Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza. 23 Utengenso mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene lili pamaso pa Yehova, buledi mmodzi, buledi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. 24 Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 25 Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova. 26 Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.
27 “Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija. 28 Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo.
29 “Zovala zopatulika za Aaroni zidzakhala za ana ake aamuna iye atafa kuti adzavale podzozedwa ndi polandira udindo wawo. 30 Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.
31 “Utenge nkhosa yayimuna ya pamwambo wodzoza ansembe ndipo uyiphike pamalo opatulika. 32 Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano. 33 Adye zonse zimene anazipereka kwa Yehova pamwambo wopepesera machimo powadzoza ndi kuwapatula. Munthu wamba asadye chifukwa ndi zopatulika. 34 Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.
35 “Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri. 36 Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika. 37 Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa.
38 “Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri. 39 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. 40 Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa. 41 Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova.
42 “Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthawi zonse, pa mibado yonse. Muzidzazipereka pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Pa guwa lansembe, Yehova adzakumana nanu ndi kuyankhula nanu. 43 Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga.
44 “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira. 45 Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo. 46 Adzadziwa kuti ine ndine Mulungu wawo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova, Mulungu wawo.”
8 1 Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. 2 Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. 3 Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo 4 anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. 5 Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” 6 Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.
Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. 7 Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” 8 Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
9 Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”
11 Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”
“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
Za Umboni wa Yesu
12 Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
13 Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”
14 Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16 Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17 Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”
19 Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”
Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” 20 Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.
Mkangano Woti Yesu Ndani
21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”
22 Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”
23 Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. 24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”
25 Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”
Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, 26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
27 Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. 28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” 30 Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.
Ana a Abrahamu
31 Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. 32 Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
33 Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”
34 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. 35 Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. 36 Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu. 37 Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38 Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”
39 Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.”
Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita. 40 Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi. 41 Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.”
Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”
Ana a Mdierekezi
42 Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha. 43 Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. 44 Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. 45 Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine! 46 Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira? 47 Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”
Zomwe Yesu Ananena za lye Mwini
48 Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”
49 Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza. 50 Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza. 51 Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”
52 Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’ 53 Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”
54 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine. 55 Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake. 56 Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”
57 Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”
58 Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!” 59 Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.
Chenjezo kwa Mkazi Wachigololo
5 Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi,
tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,
2 kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru
ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.
3 Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.
Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,
4 koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;
ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5 Mapazi ake amatsikira ku imfa;
akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.
6 Iye saganizirapo za njira ya moyo;
njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.
7 Tsopano ana inu, mundimvere;
musawasiye mawu anga.
8 Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,
usayandikire khomo la nyumba yake,
9 kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;
ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,
10 kapenanso alendo angadyerere chuma chako
ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.
11 Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,
thupi lako lonse litatheratu.
12 Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!
Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13 Sindinamvere aphunzitsi anga
kapena alangizi anga.
14 Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke
pakati pa msonkhano wonse.”
15 Imwa madzi a mʼchitsime chakochako,
madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
16 Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu?
Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
17 Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha,
osati uyigawireko alendo.
18 Yehova adalitse kasupe wako,
ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
19 Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.
Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,
ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
20 Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?
Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
21 Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona,
ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.
22 Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha;
zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.
23 Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo,
adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
4 Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake. 2 Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa. 3 Chomwechonso, ife pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo ya dziko lapansi. 4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo, 5 kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana. 6 Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.” 7 Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.
Nkhawa ya Paulo chifukwa cha Agalatiya
8 Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu. 9 Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo? 10 Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka. 11 Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe.
12 Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire. 13 Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka. 14 Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini. 15 Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa. 16 Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?
17 Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo. 18 Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu. 19 Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu, 20 ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru.
Hagara ndi Sara
21 Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena? 22 Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu. 23 Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.
24 Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25 Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. 27 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Sangalala, iwe mayi wosabala,
amene sunabalepo mwana;
imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,
iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
kuposa mkazi wokwatiwa.”
28 Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29 Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero. 30 Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.” 31 Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.