Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 28

Zovala za Ansembe

28 “Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe. Umusokere mʼbale wako, Aaroni, zovala zopatulika kuti azioneka mwaulemerero ndi molemekezeka. Uwawuze anthu onse aluso amene Ine ndawapatsa nzeru pa ntchito yosoka kuti apange zovala za Aaroni za pa mwambo womupatula, kuti iye anditumikire monga wansembe. Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe. Iwo agwiritse ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira ndi yosalala yofewa.

Efodi

“Apange efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yolukidwa mwaluso. Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala.

“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli. 10 Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo. 11 Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide. 12 Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. 13 Upange zoyikamo za maluwa agolide, 14 ndiponso maunyolo awiri a golide wabwino kwambiri, wopetedwa ngati zingwe ndipo uwalumikize ku zoyikamozo.

Chovala Chapachifuwa

15 “Upange chovala chapachifuwa chogwiritsa ntchito poweruza mlandu ndipo uchipange mwaluso kwambiri. Uchipange ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. 16 Kutalika kwake kukhale kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, ndipo chikhale chopinda pawiri. 17 Uyikepo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rubi, topazi ndi berili. 18 Mzere wachiwiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; 19 mzere wachitatu pakhale miyala ya opera, agate ndi ametisiti. 20 Mzere wachinayi pakhale miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi uyiike mu zoyikamo zagolide. 21 Miyalayo ikhalepo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse uzokotedwe ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

22 “Upange timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. 23 Upangenso mphete ziwiri zagolide ndipo uzimangirire pa ngodya ziwiri za pa chovala chapachifuwa. 24 Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. 25 Ndipo mbali ina ya timaunyoloto umangirire pa zoyikapo zake ziwiri zija ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. 26 Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. 27 Upangenso mphete zina ziwiri zagolide ndipo uzilumikize kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. 28 Tsono umangirire mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi.

29 “Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse. 30 Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova.

Zovala Zina za Ansembe

31 “Uyipangire efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo. 32 Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. 33 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake. 34 Choncho pazikhala mphonje imodzi kenaka belu limodzi, kuzungulira mpendero wa mkanjo wonse. 35 Aaroni azivala mkanjowo pamene akutumikira ngati wansembe. Kulira kwa maberu kuzimveka pamene akulowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova ndiponso pamene akutuluka, kuti asafe.

36 “Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, choperekedwa kwa Yehova. 37 Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo. 38 Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.

39 “Uluke mwinjiro wa nsalu yofewa yosalala ndiponso upange nduwira ya nsalu yofewa yosalala. Lamba wake akhale wolukidwa bwino ndi munthu waluso. 40 Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka. 41 Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga.

42 “Uwapangire akabudula a nsalu yofewa oyambira mʼchiwuno kulekeza mʼntchafu kuti asamaonetse maliseche. 43 Aaroni ndi ana ake ayenera kuvala akabudulawo pamene akulowa mu tenti ya msonkhano kapena pamene akupita ku guwa lansembe kukatumikira malo oyera kuopa kuti angachimwe ndi kufa.

“Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aaroni ndi zidzukulu zake.”

Yohane 7

Yesu Apita Kuphwando Lamisasa

Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe. Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita. Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.” Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.

Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa. Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.” Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.

10 Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri. 11 Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?”

12 Pakuti pa chigulu cha anthu panali kunongʼona ponseponse za Iye. Ena ankanena kuti, “Iye ndi munthu wabwino.”

Ena ankayankha kuti, “Ayi, Iye amanamiza anthu.” 13 Koma panalibe amene ankanena kalikonse poyera za Iye chifukwa choopa Ayuda.

Yesu Aphunzitsa pa Phwando

14 Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”

16 Yesu anayankha kuti, “Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. 17 Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. 18 Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse. 19 Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”

20 Gulu la anthu linayankha kuti, “Iwe ndiye wagwidwa ndi ziwanda. Ndani akufuna kukupha?”

21 Yesu anawawuza kuti, “Ine ndinachita chodabwitsa chimodzi ndipo inu mwadabwa. 22 Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata. 23 Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata? 24 Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.”

Kodi Yesu ndi Khristu?

25 Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu? 26 Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? 27 Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”

28 Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa, 29 koma Ine ndikumudziwa chifukwa ndichokera kwa Iyeyo ndipo ndiye amene anandituma Ine.”

30 Chifukwa cha izi iwo anayesa kumugwira Iye, koma palibe aliyense amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa nthawi yake inali isanafike. 31 Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”

32 Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.

33 Yesu anati, “Ine ndili ndi inu kwa kanthawi kochepa chabe, ndipo kenaka ndizipita kwa Iye amene anandituma Ine. 34 Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”

35 Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki? 36 Kodi Iye amatanthauza chiyani pamene anati, ‘Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndi ‘Kumene Ine ndili, inu simungathe kubwera?’ ”

Mitsinje ya Madzi Opatsa Moyo

37 Pa tsiku lomaliza ndi lalikulu kwambiri laphwando, Yesu anayimirira nafuwula nati, “Ngati munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe. 38 Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ” 39 Ponena izi Iye amatanthauza Mzimu Woyera, amene adzalandire amene amakhulupirira Iye. Pa nthawiyi nʼkuti Mzimu Woyera asanaperekedwe, pakuti Yesu anali asanalemekezedwe.

40 Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”

41 Ena anati, “Iye ndiye Khristu.”

Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? 42 Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?” 43 Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. 44 Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.

Kusakhulupirira kwa Atsogoleri a Ayuda

45 Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”

46 Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”

47 Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” 48 “Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye? 49 Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”

50 Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti, 51 “Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”

52 Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”

[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe 7:53 mpaka 8:11]

Za Mkazi Wachigololo

53 Kenaka onse anachoka, napita kwawo.

Miyambo 4

Nzeru Iposa Zonse

Ananu, mverani malangizo a abambo anu;
    tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.
    Choncho musasiye malangizo anga.
Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga;
    mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.
Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,
    “Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,
    usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.
Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;
    usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.
    Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru.
    Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza;
    ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako;
    idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”

10 Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena,
    ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.
11 Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru.
    Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.
12 Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana;
    ukamadzathamanga, sudzapunthwa.
13 Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi.
    Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
14 Usayende mʼnjira za anthu oyipa
    kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
15 Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo;
    uzilambalala nʼkumangopita.
16 Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa;
    tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.
17 Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi
    ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.

18 Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha
    kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
19 Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani;
    iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.

20 Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena;
    tchera khutu ku mawu anga.
21 Usayiwale malangizo angawa,
    koma uwasunge mu mtima mwako.
22 Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza
    ndipo amachiritsa thupi lake lonse.
23 Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu
    pakuti ndiwo magwero a moyo.
24 Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota;
    ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
25 Maso ako ayangʼane patsogolo;
    uziyangʼana kutsogolo molunjika.
26 Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako
    ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
27 Usapatukire kumanja kapena kumanzere;
    usapite kumene kuli zoyipa.

Agalatiya 3

Chikhulupiriro Kapena Ntchito za Lamulo

Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda. Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva? Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi? Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi? Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva? Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”

Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu. Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.” Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.

10 Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.” 11 Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.” 12 Koma chikhulupiriro si Malamulo, chifukwa Malemba akuti, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” 13 Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.” 14 Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.

Lamulo ndi Lonjezo

15 Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi. 16 Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu. 17 Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo. 18 Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.

19 Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati. 20 Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.

21 Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama. 22 Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.

23 Chikhulupiriro ichi chisanabwere, ife tinali mʼndende ya lamulo, otsekeredwa mpaka pamene chikhulupiriro chikanavumbulutsidwa. 24 Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro. 25 Tsopano pakuti chikhulupiriro chabwera, ife sitilinso mu ulamuliro wa lamulo.

Ana a Mulungu

26 Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu, 27 pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu. 28 Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. 29 Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.