M’Cheyne Bible Reading Plan
Yetero Abwera Kudzaona Mose
18 Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.
2 Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira 3 mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” 4 Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”
5 Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa. 6 Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”
7 Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti 8 Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.
9 Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. 10 Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. 11 Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.” 12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
13 Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. 14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”
15 Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. 16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”
17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.”
24 Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. 25 Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. 26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.
27 Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.
Chopereka cha Mayi Wamasiye
21 Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. 2 Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. 3 Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. 4 Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”
Zizindikiro za Masiku Otsiriza
5 Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati, 6 “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
7 Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”
8 Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. 9 Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”
10 Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina. 11 Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.
12 “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. 13 Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni. 14 Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. 15 Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa. 16 Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. 17 Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine. 18 Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke. 19 Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.
Kuwonongedwa kwa Yerusalemu
20 “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi. 21 Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda. 22 Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa. 23 Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira. 24 Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.
25 “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. 26 Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka. 27 Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28 Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
Fanizo la Mtengo Wamkuyu
29 Iye anawawuza fanizo ili, “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse. 30 Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi. 31 Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
32 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Za Kukhala Tcheru
34 “Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. 35 Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. 36 Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37 Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse. 38 Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.
36 Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:
2 “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani
kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.
3 Nzeru zanga ndimazitenga kutali;
ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
4 Ndithudi mawu anga si abodza;
wanzeru zangwiro ali ndi inu.
5 “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu;
Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.
6 Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo
koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.
7 Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama;
amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu
ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.
8 Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo,
ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,
9 Iye amawafotokozera zomwe anachita,
kuti iwo anachimwa modzikuza.
10 Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake
ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.
11 Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira,
adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere,
adzatsiriza zaka zawo mosangalala.
12 Koma ngati samvera,
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo adzafa osadziwa kanthu.
13 “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo;
akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.
14 Amafa akanali achinyamata,
pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.
15 Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo;
Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.
16 “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso,
kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani,
kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.
17 Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu;
chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.
18 Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma;
musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.
19 Kodi chuma chanu
kapena mphamvu zanu zonse
zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?
20 Musalakalake kuti usiku ubwere,
pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.
21 Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,
chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.
22 “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.
Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
23 Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite,
kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’
24 Kumbukirani kutamanda ntchito zake
zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.
25 Anthu onse amaziona ntchitozo;
anthuwo amaziona ali kutali.
26 Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe!
Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.
27 “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo,
timene timasungunuka nʼkukhala mvula;
28 mitambo imagwetsa mvulayo
ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.
29 Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera,
momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?
30 Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse,
zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
31 Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu
ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.
32 Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani,
ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.
33 Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho;
ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.
6 Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe. 2 Pakuti akunena kuti,
“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,
ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.
Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”
Masautso a Paulo
3 Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. 4 Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. 5 Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; 6 pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi 7 ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. 8 Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. 9 Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. 10 Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.
11 Tayankhula momasuka kwa inu, Akorinto, ndipo tanena zonse za kumtima kwathu. 12 Ife sitikukubisirani chikondi chathu pa inu, koma inu mukubisa chikondi chanu pa ife. 13 Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu.
Kukhala Pamodzi ndi Osakhulupirira
14 Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima? 15 Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira? 16 Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti,
“Ndidzakhala mwa iwo
ndipo ndidzayendayenda pakati pawo,
ndipo ndidzakhala Mulungu wawo,
ndipo adzakhala anthu anga.”
17 Nʼchifukwa chake
“Tulukani pakati pawo
ndi kudzipatula,
akutero Ambuye.
Musakhudze chodetsedwa chilichonse,
ndipo ndidzakulandirani.”
18 Ndipo
“Ndidzakhala Atate anu,
ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,
akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.