Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 17

Madzi Otuluka Mʼthanthwe

17 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.”

Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”

Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”

Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”

Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”

Aisraeli Agonjetsa Aamaleki

Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli. Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”

10 Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri. 11 Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana. 12 Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa. 13 Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga.

14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”

15 Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi). 16 Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.”

Luka 20

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

20 Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”

Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe, ‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’ ”

Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’ Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”

Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”

Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”

Fanizo la Olima Mʼmunda Wamphesa

Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali. 10 Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu. 11 Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu. 12 Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.

13 “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’

14 “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’ 15 Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha.

“Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa? 16 Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.”

Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”

17 Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti,

“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana
    wasanduka mwala wa pa ngodya.

18 Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’ ”

19 Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.

Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara

20 Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza. 21 Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi. 22 Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”

23 Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti, 24 “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”

25 Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”

Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”

26 Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.

Za Kuuka kwa Akufa ndi Ukwati

27 Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso. 28 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 29 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana. 30 Wachiwiri 31 ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana. 32 Pa mapeto pake mkaziyo anafanso. 33 Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”

34 Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa. 35 Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. 36 Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa. 37 Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’ 38 Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”

39 Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!” 40 Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.

Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41 Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide? 42 Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti,

“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
    ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,
43 mpaka Ine nditasandutsa adani anu
    chopondapo mapazi anu?’

44 Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”

Achenjeza za Aphunzitsi Amalamulo

45 Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake, 46 “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando. 47 Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”

Yobu 35

35 Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,

“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza?
    Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’
Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani,
    ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’

“Ine ndikufuna ndikuyankheni inu
    pamodzi ndi abwenzi anu omwe.
Yangʼanani kumwamba ndipo muone
    mitambo imene ili kutali ndi inuyo.
Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani?
    Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?
Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani?
    Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?
Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo,
    ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.

“Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa;
    akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.
10 Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga,
    amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,
11 amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi
    ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’
12 Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye
    chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.
13 Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake;
    Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.
14 Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti
    Iye saona zimene zikuchitika.
Iye adzaweruza molungama ngati
    inu mutamudikira
15 ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango,
    zoyipa zambiri zimene anthu amachita,
16 abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake,
    mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”

2 Akorinto 5

Matupi Atsopano

Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.

Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. 10 Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.

Ntchito Yoyanjanitsa

11 Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. 12 Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. 13 Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. 14 Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. 15 Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.

16 Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.