M’Cheyne Bible Reading Plan
Mana ndi Zinziri
16 Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai. 2 Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni 3 kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. 5 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”
6 Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. 7 Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?” 8 Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”
9 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”
10 Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.
11 Yehova anati kwa Mose, 12 “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
13 Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. 14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. 15 Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe.
Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye. 16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ”
17 Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa. 18 Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya.
19 Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.”
20 Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.
21 Mmawa uliwonse aliyense amatola zimene amazifuna, ndipo dzuwa likatentha zimasungunuka. 22 Tsiku lachisanu ndi chimodzi anatuta malita anayi munthu aliyense, ndipo atsogoleri a mpingo wonse anabwera kudzawuza Mose za zimenezi. 23 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ”
24 Choncho anasunga mpaka mmawa monga Mose anawalamulira, ndipo sananunkhe kapena kuchita mphutsi. 25 Mose anati, “Idyani lero chifukwa lero ndi Sabata la Yehova. Lero simukapeza chilichonse kunjaku. 26 Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.”
27 Komabe anthu ena anapita kuti akatole chakudya tsiku lachisanu ndi chiwiri, koma sanapeze kanthu. 28 Ndipo Yehova anafunsa Mose nati, “Kodi inu muzipitirira kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti? 29 Taonani, popeza Yehova wakupatsani Sabata nʼchifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi amakupatsani chakudya cha masiku awiri. Aliyense azikhala pamene ali pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, pasapezeke wotuluka kunja.” 30 Kotero anthu anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri.
31 Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi. 32 Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”
33 Choncho Mose anati kwa Aaroni, “Tenga mtsuko ndipo uyikemo malita awiri a mana. Ndipo uyike manawo pamaso pa Yehova kusungira mibado imene ikubwera.”
34 Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike. 35 Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani.
36 (Malita awiri amafanana ndi gawo lakhumi la efa).
Zakeyu Apulumutsidwa
19 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. 2 Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. 3 Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. 4 Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.
5 Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” 6 Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.
7 Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”
8 Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”
9 Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10 Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”
Antchito Opindula Mosiyana
11 Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. 12 Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. 13 Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’
14 “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’
15 “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.
16 “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’
17 “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’
18 “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’
19 “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’
20 “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. 21 Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’
22 “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? 23 Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’
24 “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”
25 Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”
26 Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 27 Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”
Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero
28 Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu. 29 Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo, 30 “Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno. 31 Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”
32 Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira. 33 Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?”
34 Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.”
35 Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu. 36 Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.
37 Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.
38 “Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!”
“Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”
39 Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!”
40 Iye anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”
41 Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira 42 nati, “Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako. 43 Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse. 44 Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”
Yesu mʼNyumba ya Mulungu
45 Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. 46 Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”
47 Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe. 48 Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake.
34 Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
2 “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru;
tcherani khutu inu anthu ophunzira.
3 Pakuti khutu limayesa mawu
monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
4 Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera;
tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
5 “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa,
koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
6 Ngakhale ndine wolungama mtima,
akundiyesa wabodza;
ngakhale ndine wosachimwa,
mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
7 Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani,
amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
8 Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa;
amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
9 Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu
poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
10 “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu.
Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe,
Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
11 Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake;
Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
12 Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa,
kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
13 Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani?
Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
14 Mulungu akanakhala ndi maganizo
oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
15 zamoyo zonse zikanawonongekeratu
ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
16 “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi;
mvetserani zimene ndikunena.
17 Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira?
Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
18 Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’
ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
19 Iye sakondera akalonga
ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka,
pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
20 Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku;
anthu amachita mantha ndipo amamwalira;
munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
21 “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu;
amaona mayendedwe ake onse.
22 Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani
kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
23 Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu,
kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
24 Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu
ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
25 Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo
amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
26 Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo,
pamalo pamene aliyense akuwaona;
27 Chifukwa anasiya kumutsata
ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
28 Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake,
kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
29 Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa?
Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe?
Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
30 kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza,
kuti asatchere anthu misampha.
31 “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti,
‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
32 ndiphunzitseni zimene sindikuziona
ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
33 Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira,
pamene inu mukukana kulapa?
Chisankho nʼchanu, osati changa;
tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
34 “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana,
anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
35 ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru;
mawu ake ndi opanda fundo.’
36 Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto
chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
37 Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira;
amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu,
ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”
Chuma Chosungidwa Mʼmbiya Zadothi
4 Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima. 2 Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake. 3 Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika. 4 Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. 5 Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu. 6 Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
7 Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife. 8 Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; 9 tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka. 10 Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu. 11 Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa. 12 Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.
13 Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula, 14 chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake. 15 Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
16 Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. 17 Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. 18 Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.