M’Cheyne Bible Reading Plan
Mwambo Wopatula Ana Oyamba Kubadwa
13 Yehova anati kwa Mose, 2 “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”
3 Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti. 4 Pa tsiku la lero mwezi uno wa Abibu, mukutuluka mʼdziko la Igupto. 5 Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno. 6 Muzidzadya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri ndipo tsiku lachisanu ndi chiwirilo muzichita chikondwerero cha Yehova. 7 Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu. 8 Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’ 9 Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu. 10 Muzichita mwambo uwu pa nthawi yake chaka ndi chaka.
11 “Yehova akadzakulowetsani ndi kukupatsani dziko la Kanaani monga analonjezera kwa inu ndi makolo anu, 12 muzikapereka kwa Ambuye ana onse oyamba kubadwa. Ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa ndi za Ambuye. 13 Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola.
14 “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu. 15 Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’ 16 Ndipo chidzakhala kwa inu ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi pamphumi panu kuonetsa kuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.”
Kuwoloka Nyanja
17 Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” 18 Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.
19 Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.”
20 Atachoka ku Sukoti anakagona ku Etamu mʼmphepete mwa chipululu. 21 Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku. 22 Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja.
Fanizo la Kapitawo Wosakhulupirika
16 Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. 2 Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’
3 “Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha. 4 Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’
5 “Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’
6 “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’
“Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’
7 “Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’
“Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000.
“Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’
8 “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. 9 Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.
10 “Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri. 11 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni? 12 Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?
13 “Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”
14 Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu. 15 Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.
Ziphunzitso Zina
16 “Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo. 17 Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.
18 “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”
Za Munthu Wachuma ndi Lazaro
19 “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. 20 Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse 21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.
22 “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. 24 Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’
25 “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. 26 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’
27 “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, 28 pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’
29 “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’
30 “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’
31 “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”
31 “Ndinachita pangano ndi maso anga
kuti sindidzapenya namwali momusirira.
2 Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani?
Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?
3 Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa,
tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?
4 Kodi Mulungu saona zochita zanga,
ndi kudziwa mayendedwe anga?
5 “Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso,
kapena kufulumira kukachita zachinyengo,
6 Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama
ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,
7 ngati mayendedwe anga asempha njira,
ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona,
kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.
8 Pamenepo ena adye zimene ndinadzala,
ndipo zomera zanga zizulidwe.
9 “Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi,
ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,
10 pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya,
ndipo amuna ena azigona naye.
11 Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi,
tchimo loyenera kulangidwa nalo.
12 Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko;
ukanapsereza zokolola zanga.
13 “Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi,
pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,
14 ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa?
Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?
15 Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo?
Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?
16 “Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba,
kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,
17 ngati chakudya changa ndinadya ndekha,
wosagawirako mwana wamasiye,
18 chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake,
ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,
19 ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa,
kapena munthu wosauka alibe chofunda,
20 ndipo ngati iyeyo sananditamandepo
chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,
21 ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye,
poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,
22 pamenepo phewa langa lipokonyeke,
mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.
23 Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu,
ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.
24 “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma
kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’
25 ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri,
zinthu zimene manja anga anazipeza,
26 ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala,
kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,
27 ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo
nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,
28 pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo,
chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.
29 “Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga,
kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,
30 ine sindinachimwe ndi pakamwa panga
potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,
31 ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti,
‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’
32 Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse,
pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,
33 ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena,
kubisa kulakwa mu mtima mwanga
34 chifukwa choopa gulu la anthu,
ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko
kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.
35 “Aa, pakanakhala wina wondimva!
Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe;
mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
36 Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa,
ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.
37 Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita;
ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.
38 “Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine
ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,
39 ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama
kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,
40 pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu
ndi udzu mʼmalo mwa barele.”
Mawu a Yobu athera pano.
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo,
Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.
2 Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Mulungu Mwini Chitonthozo
3 Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. 4 Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. 5 Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri. 6 Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife. 7 Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo. 9 Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa. 10 Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe. 11 Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.
Paulo Afotokoza za Kusintha kwa Ulendo Wake
12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. 13 Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa. 14 Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
15 Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri. 16 Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. 17 Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
18 Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.” 19 Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.” 20 Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu. 21 Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife, 22 nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
23 Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni. 24 Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.