M’Cheyne Bible Reading Plan
50 Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. 2 Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. 3 Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
4 Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, 5 ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”
6 Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”
7 Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. 8 Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni 9 Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.
10 Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.
12 Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14 Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.
Yosefe Abwereza Kutsimikizira Abale Ake
15 Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?” 16 Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: 17 ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
18 Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”
19 Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu? 20 Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri. 21 Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.
Kumwalira kwa Yosefe
22 Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 23 ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.
24 Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.” 25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
26 Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.
Yohane Mʼbatizi Akonza Njira
3 Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. 2 Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. 3 Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. 4 Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.
5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa
ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa,
misewu yokhotakhota idzawongoledwa,
ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
6 Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”
7 Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera? 8 Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana. 9 Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”
10 Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”
11 Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”
12 Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”
13 Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” 14 Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?”
Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”
15 Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. 16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 17 Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.” 18 Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.
19 Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, 20 Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.
Ubatizo wa Yesu
21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”
Makolo a Yesu
23 Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe,
mwana wa Heli, 24 mwana wa Matate,
mwana wa Levi, mwana wa Meliki,
mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe
25 mwana wa Matati, mwana wa Amosi,
mwana wa Naomi, mwana wa Esli,
mwana wa Nagai, 26 mwana wa Maati,
mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni,
mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda
27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa,
mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli,
mwana wa Neri, 28 mwana wa Meliki,
mwana wa Adi, mwana wa Kosamu,
mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,
29 mwana wa Jose, mwana wa Eliezara,
mwana wa Yorimu, mwana wa Matati,
mwana wa Levi, 30 mwana wa Simeoni,
mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe,
mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,
31 mwana wa Meleya, mwana wa Mena,
mwana wa Matata, mwana wa Natani,
mwana wa Davide, 32 mwana wa Yese,
mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi,
mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,
33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni,
mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi,
mwana wa Yuda, 34 mwana wa Yakobo,
mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu,
mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,
35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu,
mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi,
mwana wa Sela, 36 mwana wa Kainane,
mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu,
mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,
37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki,
mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli,
mwana wa Kainane, 38 mwana wa Enosi,
mwana wa Seti,
mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.
Mawu a Yobu
16 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Ndinamvapo zambiri monga zimenezi;
nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
3 Kodi mawu anu ochulukawo adzatha?
Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
4 Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu,
inuyo mukanakhala monga ndilili inemu;
Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu
ndi kukupukusirani mutu wanga.
5 Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani;
chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.
6 “Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa;
ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
7 Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu;
mwawononga banja langa lonse.
8 Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni;
kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
9 Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane,
amachita kulumira mano;
mdani wanga amandituzulira maso.
10 Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza;
amandimenya pa tsaya mwachipongwe
ndipo amagwirizana polimbana nane.
11 Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa
ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
12 Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya;
anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya.
Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
13 anthu ake oponya mauta andizungulira.
Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga
ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
14 Akundivulaza kawirikawiri,
akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.
15 “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa
ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
16 Maso anga afiira ndi kulira,
ndipo zikope zanga zatupa;
17 komatu manja anga sanachite zachiwawa
ndipo pemphero langa ndi lolungama.
18 “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga;
kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
19 Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba;
wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
20 Wondipembedzera ndi bwenzi langa,
pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
21 iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu
monga munthu amadandaulira bwenzi lake.
22 “Pakuti sipapita zaka zambiri
ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”
17 “Mtima wanga wasweka,
masiku anga atha,
manda akundidikira.
2 Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira;
maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.
3 “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna.
Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?
4 Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu;
choncho simudzawalola kuti apambane.
5 Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma,
ana ake sadzaona mwayi.
6 “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense,
munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.
7 Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni;
ndawonda ndi mutu womwe.
8 Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi;
anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.
9 Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo,
ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.
10 “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo,
sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.
11 Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka,
pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.
12 Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana,
nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’
13 Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda,
ngati ndiyala bedi langa mu mdima,
14 ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’
ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’
15 tsono chiyembekezo changa chili kuti?
Ndani angaone populumukira panga?
16 Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse,
polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.”
Atumiki a Khristu
4 Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu. 2 Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika. 3 Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha. 4 Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye. 5 Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.
6 Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake. 7 Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire?
8 Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. 9 Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. 10 Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa! 11 Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. 12 Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. 13 Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.
Pempho ndi Chenjezo
14 Sindikulemba izi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kukuchenjezani monga ana anga okondedwa. 15 Ngakhale muli ndi anthu 10,000 okutsogolerani mwa Khristu, mulibe abambo ambiri, popeza mwa Khristu Yesu, ine ndakhala abambo anu kudzera mu Uthenga Wabwino. 16 Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine. 17 Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo, mwana wanga amene ndimamukonda, amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu, umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse.
18 Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu. 19 Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani. 20 Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu. 21 Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.