M’Cheyne Bible Reading Plan
Pangano la Mulungu ndi Abramu
15 Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati:
“Usaope Abramu.
Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza.
Mphotho yako idzakhala yayikulu.”
2 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko? 3 Inu simunandipatse ana kotero kuti wantchito wa ku nyumba kwanga ndiye amene adzalowe mʼmalo mwanga.”
4 Yehova anayankhula naye nati: “Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.” 5 Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
6 Abramu anakhulupirira Yehova, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.
7 Ndipo anamuwuza kuti, “Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.”
8 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”
9 Kotero Yehova anati kwa iye, “Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.”
10 Abramu anabweretsadi zonsezi nadula chilichonse pakati nʼkuzindandalika, chidutswa chilichonse kuyangʼanana ndi chinzake; koma njiwa ndi nkhunda sanazidule pakati. 11 Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa.
12 Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba. 13 Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. 14 Koma ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo ndipo pambuyo pake iwo adzatulukamo ndi chuma chambiri. 15 Komabe iweyo udzamwalira mu mtendere ndi kuyikidwa mʼmanda utakalamba bwino. 16 Patapita mibado inayi, adzukulu ako adzabwereranso kuno popeza tchimo la Aamori silinafike pachimake kuti alangidwe.”
17 Dzuwa litalowa ndipo mdima utagwa, panaoneka mʼphika wofuka nthunzi ya moto ndi sakali yoyaka ndipo zinadutsa pakati pa zidutswa za nyama zija. 18 Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 19 Ndidzakupatsani dziko la Akeni, Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti, Aperezi, Arefaimu, 21 Aamori, Akanaani, Agirigasi ndi Ayebusi.”
Kuphedwa kwa Yohane Mʼbatizi
14 Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu. 2 Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”
3 Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo. 4 Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” 5 Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.
6 Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. 7 Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe. 8 Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” 9 Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; 10 ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. 11 Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. 12 Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
13 Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. 14 Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.
15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”
16 Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”
17 Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”
18 Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” 19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
Yesu Ayenda pa Nyanja
22 Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. 23 Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. 24 Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
25 Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. 26 Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.
27 Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”
28 Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”
29 Iye anati, “Bwera.”
Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. 30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”
31 Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”
32 Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. 33 Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
34 Atawoloka, anafika ku Genesareti. 35 Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye. 36 Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.
Adani a Nehemiya pa Ntchito Yake
4 Sanibalati atamva kuti tikumanganso khoma anapsa mtima nayamba kuseka ndi kunyogodola Ayuda kwambiri. 2 Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?”
3 Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, “Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!”
4 Tsono ndinayamba kupemphera kuti, “Timvereni, Inu Mulungu wathu, mmene akutinyozera. Mulole kuti mawu awo onyoza awabwerere, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo. 5 Musawakhululukire mphulupulu zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu popeza aputa ukali wanu pamaso pa anthu omanga khoma.”
6 Choncho ife tinamangabe khomalo kufikira lonse litafika theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu anagwira ntchitoyo ndi mtima wawo wonse.
7 Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri. 8 Tsono onse anapangana za chiwembu kuti abwere ndi kudzathira nkhondo anthu a ku Yerusalemu ndi kuyambitsa mapokoso pakati pawo. 9 Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinayika alonda otiteteza kwa adaniwo usiku ndi usana.
10 Pa nthawi yomweyi anthu a ku Yuda anati, “Mphamvu za anthu onyamula zinyalala zikutha ndipo pali zinyalala zambiri. Choncho ife sititha kumanga khomali.”
11 Adani athunso anati, “Iwo asanadziwe izi, kapena kutiona, tidzakhala tili pakati pawo ndipo tidzawapha ndi kuyimitsa ntchitoyo.”
12 Ndipo Ayuda amene ankhala pafupi ndi adani athuwo anabwera kakhumi konse kuchokera konse kumene ankakhala kudzatiwuza kuti tibwereko ku ntchito.
13 Choncho kumbuyo kwa khoma, cha mʼmunsi mwake komanso malo amene anali asanathe ndinayikamo anthu mʼmabanja atatenga malupanga, mikondo ndi mauta awo. 14 Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”
15 Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma.
16 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse 17 amene ankamanga khoma. Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, dzanja linali atanyamula chida chankhondo. 18 Mʼmisiri aliyense ankamangirira lupanga lake mʼchiwuno mwake akamagwira ntchito. Koma munthu woyimba lipenga anali pambali panga nthawi zonse.
19 Ndipo ine ndinati kwa anthu olemekezeka ndi anthu ena onse, “Ntchitoyi ndi yayikulu ndipo ili padera lalikulu ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma. 20 Tsono kulikonse kumene muliko, mukamva kulira kwa lipenga bwerani mudzasonkhane kumene kuli ine kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”
21 Choncho enafe tinapitiriza kugwira ntchito, pamene theka lina linkanyamula mikondo kuyambira mʼbandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka. 22 Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.” 23 Choncho ine, anzanga, antchito anga, ndi anthu otiteteza amene ankanditsata panalibe ndi mmodzi yemwe anavula zovala zake pogona. Aliyense anasunga chida chake chankhondo pambali pake.
Ku Ikoniya
14 Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira. 2 Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale. 3 Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo. 4 Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi. 5 Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala. 6 Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo, 7 kumene anapitiriza kulalikira Uthenga Wabwino.
Ku Lusitra ndi ku Derbe
8 Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake. 9 Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho. 10 Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.
11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!” 12 Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula. 13 Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.
14 Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, 15 “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 16 Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo. 17 Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” 18 Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa. 20 Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.
Paulo ndi Barnaba Abwerera ku Antiokeya wa ku Siriya
21 Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya. 22 Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” 23 Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira. 24 Atadutsa Pisidiya, anafika ku Pamfiliya. 25 Atalalikira Mawu ku Perga, anapita ku Ataliya.
26 Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza. 27 Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro. 28 Ndipo anakhala kumeneko ndi ophunzira nthawi yayitali.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.