Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 13

Abramu Asiyana ndi Loti

13 Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide.

Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, ndiponso kumene Abramu anamangira Yehova guwa lansembe kwa nthawi yoyamba ndi kupemphera mʼdzina la Yehova.

Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi. Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo.

Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.”

10 Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). 11 Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. 12 Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. 13 Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri.

14 Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. 15 Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya. 16 Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako. 17 Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.”

18 Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.

Mateyu 12

Yesu Mbuye wa Sabata

12 Pa nthawi imeneyo Yesu anadutsa pakati pa minda ya tirigu pa tsiku la Sabata. Ophunzira ake anamva njala nayamba kuthyola ngala za tirigu nʼkumadya. Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.”

Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene anachita Davide pamene iye ndi anzake anamva njala? Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha. Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa? Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano. Ngati mukanadziwa zomwe mawu awa atanthauza, ‘Ine ndifuna chifundo osati nsembe,’ inu simukanatsutsa osalakwa. Pakuti Mwana wa Munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”

Yesu Achiritsa Munthu Wolumala Dzanja

Atachoka kumeneko anakalowa mʼsunagoge mwawo. 10 Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, “Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?”

11 Iye anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu ali ndi nkhosa nigwera mʼdzenje tsiku la Sabata, kodi simudzayigwira ndi kuyitulutsa kunja? 12 Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata.”

13 Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale. 14 Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.

Mtumiki Wosankhidwa ndi Mulungu

15 Podziwa zimenezi, Yesu anachoka kumalo amenewo. Ambiri anamutsata Iye ndipo anachiritsira odwala awo onse 16 nawachenjeza kuti asamuwulule kuti yani. 17 Uku kunali kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,

18 “Taonani mnyamata wanga amene ndinamusankha,
    Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye.
Pa Iye ndidzayika Mzimu wanga,
    ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
19 Sadzalimbana, sadzafuwula,
    ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake mʼmakwalala.
20 Bango lophwanyika sadzalithyola,
    ndi nyale yofuka sadzayizimitsa,
kufikira Iye adzatumiza chiweruziro chikagonjetse.
21     Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”

Mwano wa Afarisi

22 Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona. 23 Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?”

24 Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”

25 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse ukagawanika mwa iwo udzawonongeka ndi mzinda uliwonse kapena banja likagawanika, mwa izo zokha sizidzayima. 26 Ngati Satana atulutsa Satana, iye adzigawa yekha. Nanga ufumu wake ungayime bwanji? 27 Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu. 28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.

29 “Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.

30 “Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amamwaza. 31 Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa. 32 Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo.

Mtengo ndi Zipatso Zake

33 “Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake. 34 Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima. 35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye. 36 Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. 37 Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”

Chizindikiro cha Yona

38 Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”

39 Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona. 40 Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka. 41 Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano. 42 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.

Za Mzimu Woyipa

43 “Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza. 44 Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino. 45 Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”

Amayi ndi Abale Ake a Yesu

46 Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye. 47 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunjaku akufuna kuyankhulana nanu.”

48 Iye anayankha kuti, “Amayi anga ndani ndipo abale anga ndi ndani?” 49 Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, “Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga. 50 Pakuti aliyense amene achita chifuniro cha Atate anga akumwamba ndiye mʼbale wanga, mlongo wanga ndi amayi anga.”

Nehemiya 2

Aritasasita Atumiza Nehemiya ku Yerusalemu

Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.”

Ine ndinachita mantha kwambiri. Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”

Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?”

Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”

Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.

Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane.

10 Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.

Nehemiya Ayendera Makoma a Yerusalemu

11 Ndinafika ku Yerusalemu, ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.

13 Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto. 14 Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse. 15 Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa. 16 Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi.

17 Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.” 18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza.

Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.

19 Koma Sanibalati wa ku Horoni, Tobiya wa ku Amoni ndi Gesemu Mwarabu atamva zimenezi, anatiseka ndi kutinyoza. Iwo anafunsa kuti, “Kodi muti ndi chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mufuna kuwukira mfumu?”

20 Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”

Machitidwe a Atumwi 12

Petro Apulumuka Mʼndende

12 Inali nthawi yomweyi imene mfumu Herode anamanga ena a mu mpingo ndi cholinga chakuti awazunze. Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. Ataona kuti zimenezi zinakondweretsa Ayuda, anawonjeza ndi kugwiranso Petro. Izi zinachitika pa nthawi ya Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.

Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.

Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.

Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. 10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.

11 Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”

12 Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. 13 Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. 14 Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!”

15 Anthuwo anati kwa iye, “Wopenga iwe!” Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, “Ameneyo ndi mngelo wake.”

16 Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri. 17 Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.

18 Pamene kunacha kunali phokoso lalikulu pakati pa asilikali, iwo anafunsa kuti, “Kodi chamuchitikira Petro ndi chiyani?” 19 Herode atamufunafuna ndipo wosamupeza, anawafunsa asilikali ndipo analamulira kuti asilikaliwo aphedwe.

Imfa ya Herode

Kenaka Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi 20 Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo.

21 Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo. 22 Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.

24 Koma Mawu a Mulungu anapitirirabe kufalikirafalikira.

25 Barnaba ndi Saulo atamaliza ntchito yawo anachoka ku Yerusalemu, atatenga Yohane wotchedwanso Marko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.