M’Cheyne Bible Reading Plan
Nsanja ya Babeli
11 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. 2 Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.
3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. 4 Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”
5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6 Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”
8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu
10 Nayi mibado yochokera kwa Semu.
Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.
26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.
Mibado Yochokera mwa Tera
27 Nayi mibado yochokera mwa Tera.
Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.
31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.
32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.
Yesu Atuma Ophunzira Ake
10 Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.
2 Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane, 3 Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; 4 Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
5 Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. 6 Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. 7 Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ 8 Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.
9 “Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.
16 “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17 Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18 Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19 Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20 pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.
21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.
24 “Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!
26 “Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27 Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29 Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31 Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.
32 “Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33 Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.
34 “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35 Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa
“ ‘Munthu ndi abambo ake,
mwana wamkazi ndi amayi ake,
mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,
36 adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’
37 “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38 Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39 Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.
40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
Anthu Avomereza Tchimo Lawo
10 Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri. 2 Ndipo Sekaniya, mwana wa Yehieli, wa fuko la Elamu, anawuza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mayiko akunowa. Koma ngakhale zili chomwechi, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraeli. 3 Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo. 4 Tsono dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu. Ife tikuthandizani. Limbani mtima ndipo gwirani ntchitoyi.”
5 Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira. 6 Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.
7 Tsono anthu analengeza mʼdziko lonse la Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Yerusalemu kwa onse ochokera ku ukapolo aja kuti asonkhane ku Yerusalemu. 8 Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.
9 Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa. 10 Ndipo wansembe Ezara anayimirira nawuza anthuwo kuti, “Inu mwachimwa pomakwatira akazi achikunja ndi kumawonjezera pa tchimo la Aisraeli. 11 Tsopano lapani kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu ndi kuchita zimene akufuna. Dzipatuleni kwa anthu a mayiko enawa ndi kwa akazi achikunjawa.”
12 Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu. 13 Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi. 14 Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.” 15 Koma Yonatani yekha mwana wa Asaheli ndi Yahazieli mwana wa Tikiva ndiwo anatsutsapo pa zimenezi. Tsono Mesulamu ndi Mlevi Sebetai anawayikira kumbuyo.
16 Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi. 17 Ndipo pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba anali atathana nawo anthu amene anakwatira akazi achilendo aja.
Okwatira Akazi Achilendo
18 Nawu mʼndandanda wa ansembe amene anakwatira akazi achikunja:
Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali awa: Maaseiya, Eliezara, Yaribu ndi Gedaliya. 19 Iwo anatsimikiza zochotsa akazi awo ndipo chifukwa cha kulakwa kwawo aliyense anapereka nkhosa yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.
20 Pa banja la Imeri panali awa:
Hanani ndi Zebadiya.
21 Pa banja la Harimu panali awa:
Maseya, Eliya, Semaya, Yehieli ndi Uziya.
22 Pa banja la Pasuri panali awa:
Eliyoenai, Maseya, Ismaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa.
23 Pakati pa Alevi panali:
Yozabadi, Simei, Kelaya (ndiye kuti, Kelita). Petaya, Yuda ndi Eliezara.
24 Pakati pa oyimba nyimbo panali
Eliyasibu.
Ochokera kwa alonda a zipata:
Salumu, Telemu ndi Uri.
25 Ochokera pakati pa Aisraeli ena:
a fuko la Parosi anali
Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, ndi Benaya.
26 A fuko la Elamu anali
Mataniya, Zekariya, Yehieli, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.
27 A fuko la Zatu anali
Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza.
28 A fuko la Bebai anali
Yehohanani, Hananiya, Zabayi ndi Atilayi.
29 A fuko la Bani anali
Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubu, Seali ndi Yeremoti.
30 A fuko la Pahati-Mowabu anali
Adina, Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, Binuyi ndi Manase.
31 A fuko la Harimu anali
Eliezara, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, 32 Benjamini, Maluki ndi Semariya.
33 A fuko la Hasumu anali
Mataneyi, Matata, Zabadi, Elifeleti, Yeremayi, Manase ndi Simei.
34 A fuko la Bani anali
Madai, Amramu, Uweli, 35 Benaya, Bediya, Keluhi, 36 Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37 Mataniya, Matenayi ndi Yasu.
38 A fuko la Binuyi anali
Simei, 39 Selemiya, Natani, Adaya, 40 Makinadebayi, Sasai, Sarai, 41 Azaleli, Selemiya, Semariya, 42 Salumu, Amariya ndi Yosefe.
43 A fuko la Nebo anali
Yeiyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya.
44 Onsewa anakwatira akazi achilendo. Tsono anawasudzula akaziwo ndi kuwatumiza kwawo pamodzi ndi ana awo.
Kenturiyo Korneliyo Ayitana Petro
10 Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya. 2 Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse. 3 Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”
4 Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?”
Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso. 5 Tsopano tuma anthu apite ku Yopa kuti akayitane munthu dzina lake Simoni Petro. 6 Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”
7 Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu. 8 Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa.
Masomphenya a Petro
9 Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera. 10 Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka. 11 Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi. 12 Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga. 13 Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”
14 Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”
15 Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”
16 Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.
17 Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata. 18 Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.
19 Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna. 20 Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”
21 Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”
22 Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.” 23 Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.
Petro ku Nyumba ya Korneliyo
24 Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima. 25 Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira. 26 Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”
27 Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana. 28 Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa. 29 Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?
30 Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira. 31 Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. 32 Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’ 33 Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”
34 Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera. 35 Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo. 36 Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse. 37 Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira, 38 kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.
39 “Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo, 40 koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera. 41 Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa. 42 Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa. 43 Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”
44 Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo. 45 Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina. 46 Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati, 47 “Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.” 48 Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.