Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 8

Nowa Atuluka Mʼchombo

Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera.

Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. 10 Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. 11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. 12 Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.

13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. 14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.

15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”

18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.

20 Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza. 21 Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.

22 “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire,
nthawi yodzala ndi nthawi yokolola
yozizira ndi yotentha,
dzinja ndi chilimwe,
usana ndi usiku,
sizidzatha.”

Mateyu 8

Yesu Achiritsa Wakhate

Iye atatsika ku phiri kuja, anthu ambirimbiri anamutsata. Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, “Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake. Ndipo Yesu anati kwa iye, “Taona, usawuze wina aliyense. Koma upite kwa mkulu wa ansembe ukadzionetse wekha ndi kupereka mphatso imene Mose analamulira, kuti ukhale umboni kwa iwo.”

Chikhulupiriro cha Kenturiyo

Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”

Ndipo Yesu anati kwa iye, “Ine ndibwera kudzamuchiritsa.”

Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”

10 Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere. 11 Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. 12 Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

13 Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, “Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira.” Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

14 Ndipo Yesu atalowa mʼnyumba ya Petro, anaona mpongozi wake wa Petro ali gone akudwala malungo. 15 Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.

16 Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. 17 Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,

“Iye anatenga zofowoka zathu,
    nanyamula nthenda zathu.”

Za Kutsatira Yesu

18 Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. 19 Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”

20 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”

21 Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”

22 Koma Yesu anamuwuza kuti, “Nditsate Ine ndipo uwaleke akufa ayikane akufa okhaokha.”

Yesu Aletsa Namondwe

23 Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24 Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25 Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”

26 Iye anawayankha kuti, “Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?” Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.

27 Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”

Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara

28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29 Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”

30 Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31 Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”

32 Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. 33 Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.

Ezara 8

Mʼndandanda wa Akuluakulu a Mabanja Amene Anabwera ndi Ezara

Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:

Geresomu wa fuko la Finehasi;

Danieli wa fuko la Itamara;

Hatusi mwana wa Sekaniya wa fuko la Davide;

Zekariya wa fuko la Parosi. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwa anthu ena 150;

Elihunai mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahati-Mowabu. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu ena 400.

Sekaniya, mwana wa Yahazieli wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwanso anthu 300.

Ebedi, mwana wa Yonatani wa fuko la Adini. Pamodzi naye analembedwanso anthu ena makumi asanu.

Yesaiya, mwana wa Ataliya wa fuko la Elamu. Pamodzi naye panali anthu ena 70.

Zebadiya, mwana wa Mikayeli wa fuko la Sefatiya. Pamodzi naye panalinso anthu 80.

Obadiya, mwana wa Yehieli wa fuko la Yowabu. Pamodzi naye panalinso anthu 218.

10 Selomiti mwana wa Yosifiya wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu 160.

11 Zekariya, mwana wa Bebai wa fuko la Babai. Pamodzi naye analembedwanso anthu 28.

12 Yohanani, mwana wa Hakatani wa fuko la Azigadi. Pamodzi naye panalinso anthu 110.

13 Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene anabwera pambuyo pake mayina awo anali Elifeleti, Yeiyeli ndi Semaya. Pamodzi ndi iwowa panalinso anthu 60.

14 Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri. Pamodzi ndi iwowa panali anthu 70.

Kubwerera ku Yerusalemu

15 Anthu onse ndinawasonkhanitsa ku mtsinje umene umapita mpaka ku Ahava, ndipo kumeneko tinagona mʼmisasa masiku atatu. Nditayangʼana pakati pa anthu ndi ansembe, ndinapeza kuti panalibe Alevi. 16 Choncho ndinayitana atsogoleri awa: Eliezara, Arieli, Semaiya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi awiri, Yoyaribu ndi Elinatani, 17 ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu. 18 Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18. 19 Anatitumiziranso Hasabiya ndi Yesaiya wa fuko la Merari pamodzi ndi abale ake ndi adzukulu ake, anthu makumi awiri. 20 Panalinso anthu ena 220 mwa anthu ogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amene Davide ndi nduna zake anawasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onsewa analembedwa potsata mayina awo.

21 Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense. 22 Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.” 23 Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.

24 Tsono ndinasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi awiri awa, Serebiya, Hasabiya ndi abale awo khumi 25 ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka. 26 Nditayeza zonse, ndinapereka mʼmanja mwawo, matani 22 asiliva, ziwiya zasiliva zolemera makilogalamu 70, ndiponso makilogalamu 3,400 a golide, 27 mbale zagolide makumi awiri zolemera makilogalamu asanu ndi atatu ndi theka ndiponso ziwiya ziwiri zamkuwa wosalala, wonyezimira bwino ngati golide wamtengowapatali.

28 Kenaka ndinawawuza kuti, “Inu ndi opatulika a Yehova, ndiponso mphatso zonsezi ndi zopatulika. Siliva ndi golideyu ndi zopereka zaufulu kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu. 29 Muzisamale bwino mpaka mutaziyeza pamaso pa atsogoleri a ansembe ndi Alevi ndi akulu a mabanja a Israeli mʼzipinda za mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu.” 30 Choncho ansembe ndi Alevi analandira zonse zoyezedwa zija, siliva, golide pamodzi ndi ziwiya kuti apite nazo ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.

31 Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira. 32 Tinafika ku Yerusalemu, komwe tinapumula masiku atatu.

33 Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi. 34 Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse.

35 Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova. 36 Iwo anaperekanso chidziwitso cha mfumu chija kwa akuluakulu a mfumu ndi kwa akazembe a mʼdera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwo anathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.

Machitidwe a Atumwi 8

Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano.

Kuzunzika kwa Mpingo

Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri. Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.

Filipo ku Samariya

Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita. Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko. Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena. Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.

Simoni Wamatsenga

Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana, 10 ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.” 11 Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo. 12 Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi. 13 Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.

14 Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane. 15 Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera, 16 chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 17 Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19 “Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”

20 Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama! 21 Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22 Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako. 23 Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”

24 Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”

25 Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.

Filipo ndi Nduna ya Zachuma ya ku Etiopia

26 Mngelo wa Ambuye anati kwa Filipo, “Nyamuka pita chakummwera, ku msewu wa ku chipululu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu.” 27 Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu, 28 ndipo akubwerera kwawo atakwera pa galeta lake amawerenga buku la mneneri Yesaya. 29 Mzimu anamuwuza Filipo kuti, “Pita pa galeta ilo ndipo ukakhale pafupi nalo.”

30 Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?”

31 Iye anayankha kuti, “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.

32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:

“Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
    kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
    momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
33 Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake.
    Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake
    poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”

34 Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, “Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?” 35 Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.

36 Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?” 37 Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.” 38 Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza. 39 Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.