M’Cheyne Bible Reading Plan
14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, 2 “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. 3 Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ 4 Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.
5 Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?” 6 Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake. 7 Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. 8 Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika. 9 Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.
10 Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova. 11 Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto? 12 Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”
13 Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso. 14 Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.”
15 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda. 16 Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma. 17 Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero. 18 Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”
19 Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo. 20 Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse.
21 Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika. 22 Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.
23 Aigupto onse, Farao, ndi onse okwera pa magaleta ndi akavalo anawalondola ndipo analowa mʼmadzi. 24 Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo. 25 Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.”
26 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.” 27 Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo. 28 Madzi anabwerera ndi kumiza magaleta ndi okwera akavalo, asilikali ankhondo onse amene anatsatira Aisraeli mʼnyanja, palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka.
29 Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. 30 Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa 31 Choncho Aisraeli anaona dzanja lamphamvu la Yehova limene linagonjetsa Aigupto aja, ndipo iwo anaopa Yehova ndi kumukhulupirira pamodzi ndi mtumiki wake Mose.
Za Uchimo, Chikhulupiriro ndi Ntchito
17 Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. 2 Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa. 3 Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha.
“Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni. 4 Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”
5 Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”
6 Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.
7 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’ 8 Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’ 9 Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita? 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ”
Yesu Achiritsa Akhate Khumi
11 Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. 12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!”
14 Iye atawaona, anati, “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.
15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.
17 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18 Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” 19 Pamenepo anati kwa iye, “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”
Za Ufumu wa Mulungu
20 Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso, 21 kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”
22 Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. 23 Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo. 24 Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake. 25 Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.
26 “Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu. 27 Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.
28 “Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga. 29 Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo.
30 “Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera. 31 Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti! 33 Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga. 34 Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 35 Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa. 36 Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.”
37 Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?”
Iye anayankha kuti, “Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”
Mawu a Elihu
32 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. 2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. 3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. 4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. 5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:
“Ine ndine wamngʼono,
inuyo ndinu akuluakulu,
nʼchifukwa chake ndimaopa,
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru,
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 Ndadikira nthawi yonseyi,
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12 ineyo ndinakumvetseranidi.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;
mawu awathera.
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,
pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;
nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,
ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,
kapena kuyankhula zoshashalika,
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”
2 Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko. 2 Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni? 3 Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe. 4 Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.
Za Kukhululukira Wolakwa
5 Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera. 6 Chilango chimene ambiri a inu mwamupatsa munthu ameneyu nʼchokwanira. 7 Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima. 8 Choncho ndikukupemphani kuti mutsimikizire chikondi chanu pa iye. 9 Cholinga china chimene ndinakulemberani kalata ija chinali chofuna kukuonani ngati mudzandimvera pa zonse. 10 Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu, 11 kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.
Atumiki a Pangano Latsopano
12 Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo, 13 ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.
14 Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. 15 Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. 16 Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi? 17 Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.