Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 13

Munthu wa Mulungu Wochokera ku Yuda

13 Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani. Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ” Tsiku lomwelo munthu wa Mulungu uja anapereka chizindikiro ichi: “Chizindikiro chimene Yehova wanena ndi ichi: Taonani guwali lidzangʼambika pakati ndipo phulusa lili pamenepo lidzamwazika.”

Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza. Nthawi yomweyo guwa lija linangʼambika pakati ndipo phulusa lake linamwazika molingana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapereka potsata mawu a Yehova.

Pamenepo mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Undipempherere kwa Yehova Mulungu wako kuti andikomere mtima ndipo undipempherere kuti dzanja langa lichire.” Choncho munthu wa Mulungu anapempha kwa Yehova, ndipo dzanja la mfumu linachiritsidwa nʼkukhala ngati momwe linalili kale.

Mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya, ndipo ndidzakupatsa mphatso.”

Koma munthu wa Mulunguyo anayankha mfumu kuti, “Ngakhale mutandipatsa theka la chuma chanu, sindingapite nanu, kapena kudya chakudya, kapenanso kumwa madzi kuno. Pakuti Yehova anandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kapena kubwerera podzera njira imene unayendamo kale.’ ” 10 Choncho munthu wa Mulunguyo anadzera njira ina ndipo sanatsate njira imene anayendamo pobwera ku Beteliko.

11 Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu. 12 Abambo awo aja anawafunsa kuti, “Kodi wadzera njira iti?” Ana akewo anamufotokozera njira imene munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo anadzera. 13 Ndipo abambo aja anati kwa ana akewo, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo atamangirira chishalo pa bulu, nkhalambayo inakwera buluyo 14 ndipo inalondola munthu wa Mulunguyo. Inamupeza atakhala pansi pa mtengo wa thundu ndipo inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene anabwera kuchokera ku Yuda?”

Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndineyo.”

15 Choncho mneneri wokalambayo anati kwa iye, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya.”

16 Munthu wa Mulungu uja anati, “Sindingabwerere nanu kapena kudya chakudya kapenanso kumwa madzi kuno. 17 Pakuti ndawuzidwa ndi Yehova kuti, ‘Usadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko kapenanso kubwerera poyenda njira imene unayendamo popita.’ ”

18 Mneneri wokalambayo anayankha kuti, “Inenso ndine mneneri ngati iwe. Ndipo mngelo wa Yehova anayankhula nane mawu a Yehova kuti, ‘Kamubweze abwere ku nyumba yako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’ ” Koma anamunamiza. 19 Choncho munthu wa Mulungu uja anabwerera naye ndipo anakadya ndi kumwa madzi mʼnyumba mwake.

20 Ali pa tebulo, Yehova anayankhula ndi mneneri wokalambayo amene anamubweza munthu wa Mulunguyo. 21 Iye anafuwulira munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo kuti, “Yehova akuti, ‘Iwe wanyoza mawu a Yehova ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa. 22 Iwe wabwerera ndi kudya chakudya ndiponso kumwa madzi ku malo amene Iye anakuwuza kuti usadye chakudya kapena kumwa madzi. Choncho mtembo wako sadzawuyika mʼmanda a makolo ako.’ ”

23 Munthu wa Mulungu atatha kudya ndi kumwa, mneneri amene anamubweza uja anamangirira chishalo pa bulu wa munthu wa Mulunguyo. 24 Akupita, anakumana ndi mkango pa msewu ndipo unamupha, mtembo wake unagwera pansi pa msewu, bulu uja anayima pambali pake ndipo mkango unayima pafupi ndi mtembowo. 25 Ndipo taonani, anthu ena amene ankapita mu msewumo anaona mtembowo uli pansi potero, mkango utayima pa mbali pa mtembo uja ndipo anapita nakafotokozera anthu mu mzinda umene mumakhala mneneri wokalamba uja.

26 Mneneri amene anamubweza mnzake ku njira uja atamva zimenezi, anati, “Ameneyo ndi munthu wa Mulungu amene wanyoza mawu a Yehova. Yehova wamupereka kwa mkango umene wamukhadzula ndi kumupha, monga momwe Yehova anamuchenjezera.”

27 Mneneri wokalambayo anati kwa ana ake, “Mundimangire chishalo pa bulu,” ndipo anaterodi. 28 Ndipo anapita, nakapezadi mtembo utagwera pansi mu msewu, bulu pamodzi ndi mkango atayima pambali pake. Koma mkangowo sunadye mtembowo kapena kukhadzula buluyo. 29 Choncho mneneri wokalambayo anatenga mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nawuyika pa bulu, ndipo anabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuyika mtembowo mʼmanda. 30 Tsono anayika mtembowo mʼmanda amene mneneri wokalamba uja anadzikonzera, ndipo anamulira pomanena kuti, “Mʼbale wanga ine! Mʼbale wanga ine!”

31 Atamuyika mʼmanda, iye anati kwa ana ake, “Ine ndikafa, mudzandiyike mʼmanda amene munthu wa Mulungu wayikidwa. Mudzayike mafupa anga pambali pa mafupa ake. 32 Pakuti uthenga umene Yehova anamuyankhulitsa, wotsutsana ndi guwa lansembe la ku Beteli ndi nyumba zonse za chipembedzo za mʼmizinda ya ku Samariya, zidzachitika ndithu.”

33 Ngakhale izi zinachitika, Yeroboamu sanasiye njira zake zoyipa, koma anasankhanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo ake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna kukhala wansembe iye anamupatula kukhala wansembe. 34 Limeneli ndiye linali tchimo la nyumba ya Yeroboamu limene linabweretsa kugwa kwake ndiponso chiwonongeko mʼdzikomo.

Afilipi 4

Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.

Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.

Malangizo Otsiriza

Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa! Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi. Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka. Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

Kuthokoza Chifukwa cha Mphatso

10 Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi. 11 Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. 12 Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. 13 Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

14 Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. 15 Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. 16 Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. 17 Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. 18 Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. 19 Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

20 Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Malonje Otsiriza

21 Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo. 22 Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara.

23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.

Ezekieli 43

Ulemerero Ubwerera Mʼnyumba ya Mulungu

43 Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku chipinda choyangʼana kummawa, ndipo ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ukubwera kuchokera kummawa. Liwu lake linali ngati mkokomo wamadzi, ndipo dziko linawala ndi ulemerero wake. Masomphenya amene ndinawaonawa anali ngati masomphenya amene ndinawaona pamene Yehova anabwera kudzawononga mzinda ndiponso ngati masomphenya amene ndinawaona ku mtsinje wa Kebara. Ndipo ndinadzigwetsa chafufumimba. Ulemerero wa Yehova unalowa mʼNyumba ya Mulungu kudzera pa chipata choyangʼana kummawa. Tsono Mzimu unandinyamula nundilowetsa mʼbwalo lamʼkati, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.

Munthuyo ali chiyimire pambali panga, ndinamva wina akundiyankhula kuchokera mʼNyumba ya Mulungu. Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo. Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya. Tsopano alekeretu kupembedza milungu ina ndipo achotseretu mitembo ya mafumu awo, isakhale pafupi ndi Ine, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo mpaka muyaya.

10 “Iwe mwana wa munthu, awuze Aisraeliwa za Nyumba ya Mulunguyi, mamangidwe ake ndipo achite manyazi ndi machimo awo, 11 akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.

12 “Limeneli ndi lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwe pamwamba pa phiri. Malo ake onse ozungulira adzakhala oyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.

Guwa la Nsembe

13 “Miyeso ya guwa lansembe ndi iyi: Pa tsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake ndi mulifupi mwake. Mʼphepete mwa ngalandeyo kuzungulira guwa lonse, mudzakhala mkombero wa masentimita 25. 14 Kuchokera mʼngalande ya pansi padzakhala mpaka pa phaka lapansi mita imodzi, mulifupi mwake theka la mita. Kuchokera pa phaka lalingʼono mpaka pa phaka lalikulu, msinkhu wake ndi mamita awiri, mulifupi mwake ndi masentimita makumi asanu. 15 Malo osonkhapo moto pa guwa, msinkhu wake udzakhala mamita awiri. Pa ngodya iliyonse ya malo osonkhapo motowo panatuluka nyanga imodzi. 16 Malo osankhalapo moto pa guwa lansembe miyeso yake ndi yofanana mbali zonse. Mulitali mwake mudzakhala mamita asanu ndi limodzi ndipo mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi limodzi. 17 Phaka lapamwamba muyeso wake udzakhala wofanana mbali zonse. Mulitali mudzakhala mamita asanu ndi awiri ndiponso mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi awiri. Mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 ndiponso ngalande yake yozungulira idzakhala ya masentimita 25. Makwerero a guwa lansembe adzayangʼana kummawa.”

18 Kenaka munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ambuye Yehova akuti: Guwalo litamangidwa, tsono malamulo awa azidzatsatidwa popereka nsembe zopsereza ndiponso powaza magazi pa guwapo. 19 Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 20 Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula. 21 Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.

22 “Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija. 23 Utatha kuyeretsa guwa lansembelo, udzatenge mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndiponso nkhosa yayimuna yopanda chilema. 24 Udzapereke zonsezi pamaso pa Yehova, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.

25 “Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema. 26 Kwa masiku asanu ndi awiriwo ansembe adzachite mwambo woyeretsa ndi kupatula guwa lansembelo. 27 Masiku amenewa atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu, ansembe azipereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe. Apo ndidzakulandirani. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Masalimo 95-96

95 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,
    tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko
    ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.

Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,
    mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,
    ndipo msonga za mapiri ndi zake.
Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,
    ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,
    tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
pakuti Iye ndiye Mulungu wathu
    ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,
    ndi nkhosa za mʼdzanja lake.

Lero ngati inu mumva mawu ake,
    musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,
    monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,
    ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;
    ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera
    ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,
    “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”
96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;
    Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;
    lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,
    ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
    ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,
    koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,
    mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;
    bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;
    njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”
    Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;
    Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;
    nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
12     minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
13     idzayimba pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo
    ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.