Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mateyu 19

Za Kuthetsa Ukwati

19 Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo.

Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, “Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?”

Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”

Ndipo iwo anamufunsa nati, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?”

Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”

10 Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”

11 Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. 12 Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”

Yesu Adalitsa Ana

13 Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.

14 Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.” 15 Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.

Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu

16 Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”

17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”

18 Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”

Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19 lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”

20 Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?”

21 Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”

22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

23 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”

25 Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?”

26 Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

27 Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”

28 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. 30 Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”

Marko 10

Za Kusudzula

10 Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.

Afarisi ena anabwera kudzamuyesa pomufunsa kuti, “Kodi malamulo amalola kuti mwamuna asiye mkazi wake?”

Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”

Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”

Yesu anayankha kuti, “Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu. Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”

10 Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi. 11 Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. 12 Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”

Yesu Adalitsa Ana

13 Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. 14 Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. 15 Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.” 16 Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.

Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu

17 Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”

18 Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. 19 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

20 Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.”

21 Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.”

22 Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

23 Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”

24 Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! 25 Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.”

26 Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?”

27 Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”

28 Petro anati kwa Iye, “Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!”

29 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino 30 adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo. 31 Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira.”

Yesu Aneneratunso za Imfa Yake

32 Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye. 33 Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina, 34 amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”

Pempho la Yakobo ndi Yohane

35 Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”

36 Iye anafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?”

37 Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”

38 Yesu anati, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwere chikho chimene ndidzamwera kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwe nawo?”

39 Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo, 40 koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”

41 Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane. 42 Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo. 43 Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, 44 ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. 45 Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”

Bartumeyu Wosaona

46 Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. 47 Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

48 Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

49 Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.” 50 Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.

51 Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?”

Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”

52 Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.