Chronological
Afarisi ndi Asaduki Afuna Chizindikiro
16 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.
2 Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira. 3 Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi. 4 Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.
Yisiti wa Afarisi ndi Asaduki
5 Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. 6 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”
7 Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.”
8 Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa. 9 Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? 10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? 11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.” 12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.
Petro Avomereza za Yesu
13 Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?”
14 Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”
15 Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?”
16 Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”
17 Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba. 18 Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa. 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.” 20 Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.
22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.”
23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”
Za Kusenza Mtanda
24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. 25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.
28 “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”
Yesu Adyetsa Anthu 4,000
8 Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, 2 “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. 3 Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”
4 Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”
5 Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
6 Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. 7 Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. 8 Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. 9 Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, 10 analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.
11 Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. 12 Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” 13 Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.
Yisiti wa Afarisi ndi Herode
14 Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15 Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”
16 Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”
17 Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18 Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19 Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”
Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”
20 “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
21 Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida
22 Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”
24 Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”
25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26 Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”
Petro Avomereza Khristu
27 Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”
28 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”
29 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”
30 Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
Njira ya Mtanda
34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
Petro Avomereza Khristu
18 Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
19 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
20 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
Yesu Aneneratu za Imfa yake
21 Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. 22 Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
23 Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. 24 Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. 25 Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? 26 Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera. 27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.