Chronological
Chiphunzitso cha pa Phiri
5 Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye, 2 ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,
3 “Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,
chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
4 Odala ndi amene ali achisoni,
chifukwa adzatonthozedwa.
5 Odala ndi amene ali ofatsa,
chifukwa adzalandira dziko lapansi.
6 Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,
chifukwa adzakhutitsidwa.
7 Odala ndi amene ali ndi chifundo,
chifukwa adzawachitira chifundo.
8 Odala ndi amene ali oyera mtima,
chifukwa adzaona Mulungu.
9 Ndi odala amene amabweretsa mtendere,
chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,
pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
11 “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. 12 Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.
Mchere ndi Kuwunika
13 “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.
14 “Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika. 15 Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo. 16 Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.
Kukwaniritsa Malamulo
17 “Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa. 18 Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa. 19 Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. 20 Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.
Zokhudza Kupha
21 “Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’ 22 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.
23 “Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, 24 usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.
25 “Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende. 26 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti sudzatuluka mʼndende mpaka utalipira zonse.
Zokhudza Chigololo
27 “Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’ 28 Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake. 29 Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. 30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.
Zokhudza Kusudzula Mkazi
31 “Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’ 32 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.
Malonjezo
33 “Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’ 34 Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu. 35 Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu. 36 Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi. 37 Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.
Za Kubwezera Choyipa
38 “Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’ 39 Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo. 40 Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. 41 Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. 42 Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.
Kukonda Adani
43 “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’ 44 Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani 45 kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’ 46 Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi? 47 Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi? 48 Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”
Zopereka Zachifundo
6 “Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.
2 “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. 3 Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, 4 kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.
Za Kupemphera
5 “Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho. 7 Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu. 8 Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.
9 “Chifukwa chake pempherani motere:
“ ‘Atate athu akumwamba,
dzina lanu lilemekezedwe,
10 Ufumu wanu ubwere,
chifuniro chanu chichitike
pansi pano monga kumwamba.
11 Mutipatse chakudya chathu chalero.
12 Mutikhululukire mangawa athu,
monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.
13 Ndipo musatitengere kokatiyesa;
koma mutipulumutse kwa woyipayo.’
14 Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani. 15 Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Kusala Kudya
16 “Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 17 Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.
Za Chuma cha Kumwamba
19 “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.
Diso Nyale ya Thupi
22 “Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala. 23 Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji!
24 “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.
Musade Nkhawa
25 “Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? 26 Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? 27 Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?
28 “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. 29 Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. 30 Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! 31 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ 32 Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. 33 Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. 34 Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Za Kuweruza Ena
7 “Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. 2 Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.
3 “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? 4 Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako? 5 Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako.
6 “Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.
Pemphani, Funafunani, Gogodani
7 “Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. 8 Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
9 “Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? 10 Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? 11 Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha? 12 Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.
Zipata Ziwiri ndi Njira Ziwiri
13 “Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. 14 Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.
Aneneri Owona ndi Onyenga
15 “Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? 17 Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa. 18 Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino. 19 Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. 20 Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.
Ophunzira Owona ndi Onyenga
21 “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. 22 Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ 23 Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’
Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa
24 “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26 Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. 27 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”
28 Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29 chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.