Chronological
8 1 Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.
2 Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. 3 Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.
4 Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.
5 Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. 6 Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.
7 Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo. 8 Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.
9 Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija.
10 Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”
11 Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”
12 Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.
13 Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo. 14 Tsono anapeza kuti zinalembedwa mʼbuku la malamulo kuti Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti Aisraeli azikhala mʼzithando pa nthawi yonse ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri. 15 Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.”
16 Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu. 17 Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu.
18 Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.
Aisraeli Avomereza Kuchimwa Kwawo
9 Pa tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraeli anasonkhana pamodzi ndi kusala chakudya, kuvala ziguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. 2 Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo. 3 Anthuwo anayimirira pomwepo, ndipo anamva mawu a mʼbuku la malamulo a Yehova akuwerengedwa kwa maora enanso atatu ndipo anakhala maora ena atatu akuwulula machimo awo ndi kupembedza Yehova Mulungu wawo. 4 Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo. 5 Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.”
“Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse. 6 Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.
7 “Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumutulutsa mʼdziko la Uri wa ku Kaldeya ndi kumutcha dzina lake Abrahamu. 8 Inu munaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa inu, ndipo munapangana naye pangano lakuti mudzapereka kwa zidzukulu zake dziko la Akanaani Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Inu mwasunga lonjezo lanu chifukwa ndinu wolungama.
9 “Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira. 10 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. 11 Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. 12 Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo.
13 “Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino. 14 Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso. 15 Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.”
16 “Koma makolo athu anadzikuza ndi kuwumitsa khosi, ndipo iwo sanamvere malamulo anu. 17 Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye. 18 Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa.
19 “Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku. 20 Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa. 21 Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”
22 “Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo. 23 Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga. 24 Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire. 25 Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana.
26 “Komabe iwo anakhala osamvera ndipo anakuwukirani nafulatira malamulo anu. Anapha aneneri anu, amene anakawadandaulira kuti abwerere kwa Inu. Anachita chipongwe choopsa. 27 Pamene anazunzidwa anafuwulira kwa Inu, ndipo Inu munawamvera muli kumwambako. Ndipo mwa chifundo chanu chachikulu munkawapatsa atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo.”
28 “Koma akangokhala pa mtendere ankayambanso kuchita zoyipa pamaso panu. Choncho munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira kwa Inu, Inu munkawamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chochuluka, nthawi zonse munkawapulumutsa.
29 “Inu munkawachenjeza kuti abwerere ndi kuyamba kutsata malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula ndipo sankamvera malamulo anu. Iwo anachimwira malangizo anu amene munati ‘Amapatsa moyo kwa munthu wowamvera.’ Iwo ankakufulatirani, nawumitsa makosi awo osafuna kukumverani. 30 Munapirira nawo kwa zaka zambiri. Munkawachenjeza ndi Mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, koma iwo sankakumverani. Choncho munawapereka mʼmanja mwa anthu a mayiko ena. 31 Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.
32 “Nʼchifukwa chake, tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa kwambiri mumasunga pangano ndi chikondi chosasinthika. Musalole kuti mavuto onse amene atigwera ife, mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu ena onse kuyambira nthawi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero aoneke ochepa pamaso panu. 33 Koma Inu mwakhala wolungama pa zonse zimene zakhala zikutichitikira. Mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa. 34 Ndipotu mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire mawu anu. Iwo sanalabadire za malamulo anu ngakhale mawu anu owachenjeza amene munawapatsa. 35 Ngakhale ankadzilamulira okha, nʼkumalandira zabwino zochuluka mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, koma iwo sanakutumikireni kapena kusiya ntchito zawo zoyipa.
36 “Tsono, taonani! Ife lero ndife akapolo, ndife akapolo mʼdziko limene munapereka kwa makolo athu kuti azidya zipatso zake ndi zabwino zake zonse. 37 Tsono chifukwa cha machimo athu, mafumu amene munawayika kuti azitilamulira angodzilemeretsa ndi chuma chambiri cha dzikoli. Iwo ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndi ngʼombe zathu momwe afunira. Zedi, ife tili mʼmavuto aakulu.”
Mgwirizano wa Anthu
38 “Chifukwa cha zonsezi, ife tikuchita mgwirizano wokhazikika, pochita kulemba, ndipo atsogoleri athu, Alevi athu ndi ansembe athu asindikiza chidindo chawo pa mgwirizanowo.”
10 Amene anasindikiza chidindo anali awa:
Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya.
Zedekiya, 2 Seraya, Azariya, Yeremiya
3 Pasuri, Amariya, Malikiya,
4 Hatusi, Sebaniya, Maluki,
5 Harimu, Meremoti, Obadiya,
6 Danieli, Ginetoni, Baruki,
7 Mesulamu, Abiya, Miyamini
8 Maziya, Biligai ndi Semaya
Awa anali ansembe.
9 Alevi anali awa:
Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli,
10 ndi abale awo awa: Sebaniya,
Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,
11 Mika, Rehobu, Hasabiya,
12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya,
13 Hodiya, Bani ndi Beninu.
14 Atsogoleri a anthu anali awa:
Parosi, Pahati-Mowabu, Elamu, Zatu, Bani,
15 Buni, Azigadi, Bebai,
16 Adoniya, Bigivai, Adini,
17 Ateri, Hezekiya, Azuri,
18 Hodiya, Hasumu, Bezayi
19 Harifu, Anatoti, Nebayi,
20 Magipiyasi, Mesulamu, Heziri
21 Mesezabeli, Zadoki, Yaduwa
22 Pelatiya, Hanani, Ananiya,
23 Hoseya, Hananiya, Hasubu
24 Halohesi, Piliha, Sobeki,
25 Rehumu, Hasabiya, Maaseya,
26 Ahiya, Hanani, Anani,
27 Maluki, Harimu ndi Baana.
28 Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru, 29 tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.
30 “Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna.
31 “Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
32 “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu. 33 Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
34 “Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.”
35 “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.”
36 “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”
37 “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. 38 Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” 39 Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo.
“Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.