Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 42-43

Zipinda za Ansembe

42 Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto ndipo anafika nane ku zipinda zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto. Nyumba yakumpotoyi mulitali mwake munali mamita makumi asanu, mulifupi mwake munali mamita 25. Panali midadada iwiri, umodzi umayangʼanana ndi bwalo lamʼkati la mamita khumi, winawo umayangʼanana ndi bwalo lakunja. Midadada iwiriyi inali ya nyumba zitatu zosanjikana ndipo imayangʼanana. Kumaso kwa zipindazo kunali njira yamʼkati, mulifupi mwake munali mamita asanu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Makomo ake analoza chakumpoto. Zipinda zammwamba zinali zazifupi mʼmimbamu kupambana zipinda zamʼmunsi ndi zipinda zapakati chifukwa njira zake zinatenga malo ambiri. Popeza zipinda zinali zosanjikizana katatu ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo, motero zipinda zamʼmwamba zinali zochepa kuyerekeza ndi zipinda zapansi ndi zipinda zapakati. Panali khoma lakunja lomwe limatsatana ndi zipindazo kutsogolo kwake pambali pabwalo lakunja, kutalika kwake kunali mamita 25. Zipinda za mʼmbali mwa bwalo lakunja mulitali mwake munali mamita 25. Koma zomwe zinali mʼmbali mwa Nyumba ya Mulungu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Pansi pa zipinda zimenezi panali khomo chakummawa kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma lake linkayambira.

10 Mbali yakummwera kuyangʼanana ndi bwalo ndi nyumbayo kunali zipinda zina. 11 Kumaso kwa zipindazi kunali njira. Zipindazi mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zofanana ndi zipinda zoyangʼana zakumpoto zija. Makomo ndi zitseko zake zinalinso zofanana 12 ndi makomo a zipinda zakummwera. Kunali khomo mʼmbali ya kummawa kumene ankalowerako. Kunalinso khoma logawa zipinda.

13 Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika. 14 Pamene ansembe alowa ku malo opatulikawa, asatuluke kupita ku bwalo lakunja popanda kusiya momwemo zovala zimene anavala potumikira zija, pakuti zovalazi ndi zopatulika. Avale kaye zovala zina ndipo akhoza kufika kwa anthu.”

15 Munthuyo atamaliza kuyeza zimene zinali mʼkati mwa Nyumba ya Mulungu, anatuluka nane pa chipata chakummawa ndi kuyeza bwalo lonse. 16 Anayeza mbali yakummawa ndi ndodo yake yoyezera; kutalika kwake kunali mamita 250. 17 Anayeza mbali ya kumpoto ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250. 18 Munthuyo anayeza mbali yakummwera; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. 19 Kenaka anatembenukira ku mbali ya kumadzulo ndi kuyeza ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. 20 Motero anayeza mbali zonse zinayi. Panali khoma lozungulira bwalolo mulitali mwake munali mamita 250 ndipo mulifupi mwake munalinso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.

Ulemerero Ubwerera Mʼnyumba ya Mulungu

43 Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku chipinda choyangʼana kummawa, ndipo ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ukubwera kuchokera kummawa. Liwu lake linali ngati mkokomo wamadzi, ndipo dziko linawala ndi ulemerero wake. Masomphenya amene ndinawaonawa anali ngati masomphenya amene ndinawaona pamene Yehova anabwera kudzawononga mzinda ndiponso ngati masomphenya amene ndinawaona ku mtsinje wa Kebara. Ndipo ndinadzigwetsa chafufumimba. Ulemerero wa Yehova unalowa mʼNyumba ya Mulungu kudzera pa chipata choyangʼana kummawa. Tsono Mzimu unandinyamula nundilowetsa mʼbwalo lamʼkati, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.

Munthuyo ali chiyimire pambali panga, ndinamva wina akundiyankhula kuchokera mʼNyumba ya Mulungu. Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo. Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya. Tsopano alekeretu kupembedza milungu ina ndipo achotseretu mitembo ya mafumu awo, isakhale pafupi ndi Ine, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo mpaka muyaya.

10 “Iwe mwana wa munthu, awuze Aisraeliwa za Nyumba ya Mulunguyi, mamangidwe ake ndipo achite manyazi ndi machimo awo, 11 akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.

12 “Limeneli ndi lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwe pamwamba pa phiri. Malo ake onse ozungulira adzakhala oyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.

Guwa la Nsembe

13 “Miyeso ya guwa lansembe ndi iyi: Pa tsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake ndi mulifupi mwake. Mʼphepete mwa ngalandeyo kuzungulira guwa lonse, mudzakhala mkombero wa masentimita 25. 14 Kuchokera mʼngalande ya pansi padzakhala mpaka pa phaka lapansi mita imodzi, mulifupi mwake theka la mita. Kuchokera pa phaka lalingʼono mpaka pa phaka lalikulu, msinkhu wake ndi mamita awiri, mulifupi mwake ndi masentimita makumi asanu. 15 Malo osonkhapo moto pa guwa, msinkhu wake udzakhala mamita awiri. Pa ngodya iliyonse ya malo osonkhapo motowo panatuluka nyanga imodzi. 16 Malo osankhalapo moto pa guwa lansembe miyeso yake ndi yofanana mbali zonse. Mulitali mwake mudzakhala mamita asanu ndi limodzi ndipo mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi limodzi. 17 Phaka lapamwamba muyeso wake udzakhala wofanana mbali zonse. Mulitali mudzakhala mamita asanu ndi awiri ndiponso mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi awiri. Mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 ndiponso ngalande yake yozungulira idzakhala ya masentimita 25. Makwerero a guwa lansembe adzayangʼana kummawa.”

18 Kenaka munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ambuye Yehova akuti: Guwalo litamangidwa, tsono malamulo awa azidzatsatidwa popereka nsembe zopsereza ndiponso powaza magazi pa guwapo. 19 Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 20 Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula. 21 Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.

22 “Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija. 23 Utatha kuyeretsa guwa lansembelo, udzatenge mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndiponso nkhosa yayimuna yopanda chilema. 24 Udzapereke zonsezi pamaso pa Yehova, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.

25 “Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema. 26 Kwa masiku asanu ndi awiriwo ansembe adzachite mwambo woyeretsa ndi kupatula guwa lansembelo. 27 Masiku amenewa atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu, ansembe azipereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe. Apo ndidzakulandirani. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.