Chronological
Kuwukira kwa Israeli
20 Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.
2 Tsono Yehova anandiyankhula nati: 3 “Iwe mwana wa munthu, ayankhule akuluakulu a Israeli ndi kuwawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, Ine sindidzakulolani kupempha nzeru kwa Ine, akutero Ambuye Yehova.’
4 “Kodi uwaweruza? Iwe mwana wa munthu, kodi ugamula mlandu wawo? Uwadziwitse tsono zonyansa zimene anachita makolo awo, uwawuze kuti, 5 ‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 6 Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena. 7 Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
8 “ ‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo. 9 Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto. 10 Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu. 11 Ndinawapatsa malangizo anga ndi kuwadziwitsa malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. 12 Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.
13 “ ‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu. 14 Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto. 15 Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu muja, nditakweza dzanja, kuti sindidzawalowetsanso mʼdziko limene ndinawapatsa, dziko la mwana alirenji, lokoma kwambiri kuposa mayiko ena onse. 16 Paja anakana malamulo anga, sanatsatire malangizo anga ndipo anayipitsa masabata anga. Mitima yawo inakonda mafano. 17 Komabe ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge kapena kuwatheratu mʼchipululu. 18 Tsono kwa ana awo mʼchipululu ndinati, ‘Musatsatire malangizo a makolo anu kapena kusunga malamulo awo kapena kudziyipitsa ndi mafano awo. 19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsatirani malangizo anga ndipo sungani malamulo anga. 20 Masabata anga muziwasunga ngati opatulika kuti akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Mukatero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
21 “ ‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo. 22 Koma sindinatero chifukwa cha dzina langa kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Iguptomo. 23 Choncho ndinalumbira mʼchipululu, nditakweza dzanja langa, kuti ndidzawabalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwamwazira ku mayiko akutali, 24 chifukwa sanamvere malamulo anga, anakana malangizo anga, nayipitsa masabata anga, ndi kupembedza mafano a makolo awo. 25 Ine ndinawapatsanso malangizo amene sanali abwino ndi malamulo amene sakanatha kupeza nawo moyo. 26 Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’
27 “Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika. 28 Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa. 29 Tsono ndinawafunsa kuti: Kodi chitunda chimene mukupitako nʼchotani? Chitundachi chakhala chikutchedwa mpaka lero kuti ‘Chitunda cha Chipembedzo.’
Chiweruzo ndi Kubwezeretsa
30 “Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa? 31 Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.
32 “ ‘Inu munanena kuti, ‘Tikufuna tikhale ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu adziko lapansi, amene amapembedza mtengo ndi mwala.’ Koma zimene mukuganizazo sizidzachitika. 33 Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani. 34 Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndikukusonkhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munamwazikirako, ndi dzanja langa lamphamvu ndi lotambasuka ndili wokwiya kwambiri. 35 Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha anthu a mitundu ina ndipo kumeneko, moonana maso ndi maso, ndidzakuzengani mlandu. 36 Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova. 37 Ndidzakuwerengani ndi ndodo ya mʼbusa, kukulowetsani mʼchimango cha pangano langa. 38 Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
39 “ ‘Koma inu Aisraeli, zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Pitani katumikireni mafano anu onse, aliyense wa inu! Koma mʼtsogolo mwake mudzandimvera ndithu ndipo simudzayipitsa dzina langa lopatulika popereka mphatso zanu kwa mafano. 40 Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika. 41 Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona. 42 Tsono mudzadziwa kuti ndine Yehova ndikadzabwera nanu ku dziko la Israeli, dziko limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa makolo anu. 43 Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu ndi machitidwe anu onse amene munadziyipitsa nawo, ndipo mudzanyansidwa nokha chifukwa cha zoyipa zimene munachita. 44 Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Uneneri Wotsutsa Kummwera
45 Yehova anandiyankhula nati: 46 “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane kummwera; ndipo lalika mawu odzudzula anthu akummwera ndipo unenere zodzudzula dziko la nkhalango ya kummwera. 47 Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo. 48 Aliyense adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndayatsa motowo, ndipo sudzazimitsidwa.’ ”
49 Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ”
Babuloni, Lupanga la Mulungu
21 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu. 3 Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. 4 Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto. 5 Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’
6 “Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu. 7 Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”
8 Yehova anandiyankhulanso kuti, 9 “Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,
“Izi ndi zimene Yehova akunena:
Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.
10 Lanoledwa kuti likaphe,
lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi!
“ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.
11 “ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,
ndi kuti linyamulidwe,
lanoledwa ndi kupukutidwa,
kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.
12 Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,
pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga;
zidzagweranso akalonga onse a Israeli.
Adzaphedwa ndi lupanga
pamodzi ndi anthu anga.
Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.
13 “ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’
14 “Tsono mwana wa munthu, nenera
ndipo uwombe mʼmanja.
Lupanga likanthe kawiri
ngakhale katatu.
Limenelo ndilo lupanga lophera anthu.
Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa
limene likuwazungulira.
15 Ndawayikira pa zipata zawo zonse
lupanga laphuliphuli
kuti ataye mtima
ndiponso kuti anthu ambiri agwe.
Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi
ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
16 Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,
kenaka kumanzere,
kulikonse kumene msonga yako yaloza.
17 Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,
ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga
Ine Yehova ndayankhula.”
18 Yehova anandiyankhulanso kuti, 19 “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda. 20 Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa. 21 Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe. 22 Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo. 23 Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.
24 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
25 “ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni, 26 Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. 27 Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’
28 “Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Lupanga, lupanga,
alisolola kuti liphe anthu,
alipukuta kuti liwononge
ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
29 Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.
Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso.
Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa
amene tsiku lawo lafika,
ndiye kuti nthawi
ya kulangidwa kwawo komaliza.
30 “ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.
Ku malo kumene inu munabadwira,
mʼdziko la makolo anu,
ndidzakuweruzani.
31 Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,
ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani.
Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza;
anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.
32 Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.
Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe.
Simudzakumbukiridwanso
pakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.