Chronological
Yeremiya Aponyedwa Mʼchitsime cha Matope
38 Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti, 2 “Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. 3 Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ”
4 Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”
5 Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.”
6 Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.
7 Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini. 8 Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti, 9 “Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”
10 Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”
11 Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya. 12 Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi, 13 ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.
Zedekiya Afunsanso Yeremiya
14 Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”
15 Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.”
16 Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.”
17 Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. 18 Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”
19 Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”
20 Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa. 21 Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi: 22 Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti,
“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa,
ndipo anakugonjetsa.
Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope;
abwenzi ako aja akusiya.’
23 “Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.”
24 Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa. 25 Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ 26 udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’ ”
27 Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.
28 Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.
Kugonjetsedwa kwa Yerusalemu
39 Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo. 2 Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa. 3 Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni. 4 Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.
5 Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake. 6 Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda. 7 Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni.
8 Ababuloni anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu, ndiponso anagwetsa malinga a Yerusalemu. 9 Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye. 10 Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.
11 Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati: 12 “Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.” 13 Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni 14 anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake.
15 Yeremiya ali mʼndende ku bwalo la alonda, Yehova anayankhula naye: 16 “Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona. 17 Koma ndidzakupulumutsa pa tsiku limenelo, akutero Yehova; sudzaperekedwa kwa anthu amene umawaopa. 18 Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’ ”
Amasula Yeremiya
40 Yehova anayankhula ndi Yeremiya pamene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anamasula Yeremiyayo ku Rama. Anamupeza Yeremiya ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi amʼndende ena onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene ankapita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 2 Mtsogoleriyu anamupeza Yeremiya, anamuwuza kuti, “Yehova Mulungu wako analengeza kale zakuti malo ano adzawonongedwa. 3 Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere. 4 Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.” 5 Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.”
Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite. 6 Motero Yeremiya anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa ndipo anakakhala naye kumeneko pakati pa anthu amene anatsala mʼdzikomo.
Kuphedwa kwa Gedaliya
7 Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni. 8 Iwowa anapita ku Mizipa kwa Gedaliya. Amene anapitawo ndi awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana a Efai a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu awo. 9 Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 10 Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.”
11 Nawonso Ayuda onse a ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu ndi a ku mayiko ena onse anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasiyako anthu ena ku Yuda ndipo kuti inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala bwanamkubwa wawo. 12 Tsono Ayuda onsewo anabwerera ku Yuda, ku Mizipa kwa Gedaliya, kuchokera ku mayiko onse kumene anabalalikira. Ndipo anakolola zipatso zochuluka ndi vinyo wambiri.
13 Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a ankhondo onse amene sanadzipereke aja anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya 14 ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire.
15 Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwamseri anawuza Gedaliya ku Mizipa kuti, “Loleni ndipite ndikaphe Ismaeli mwana wa Netaniya, ndipo palibe amene ati adziwe. Akuphereninji ndi kuchititsa Ayuda onse, amene akuzungulirani kuti abalalike ndi kuti otsala a ku Yuda awonongeke?”
16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anawuza Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Usachite zimenezo! Zimene ukunena za Ismaeli ndi zabodza.”
Ndakatulo ya Asafu.
74 Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu?
Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
2 Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale,
fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola,
phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
3 Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya
chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
4 Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe;
anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
5 Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo
kuti adule mitengo mʼnkhalango.
6 Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo
zonse zimene tinapachika.
7 Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;
anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
8 Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.”
Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
9 Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa;
palibe aneneri amene atsala
ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
10 Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu?
Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
11 Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja?
Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
12 Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale;
Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
13 Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
14 Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani
ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
15 Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje,
munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
16 Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso;
Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
17 Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi;
munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova,
momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
19 Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo;
nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko
asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
21 Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi;
osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
22 Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu;
kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
23 Musalekerere phokoso la otsutsana nanu,
chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.
Salimo la Asafu.
79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu;
ayipitsa Nyumba yanu yoyera,
asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.
2 Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu
kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya,
matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.
3 Akhetsa magazi monga madzi
kuzungulira Yerusalemu yense,
ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.
4 Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu,
choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.
5 Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya?
Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?
6 Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina
amene sakudziwani Inu,
pa maufumu
amene sayitana pa dzina lanu;
7 pakuti iwo ameza Yakobo
ndi kuwononga dziko lawo.
8 Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu
chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe,
pakuti tili ndi chosowa chachikulu.
9 Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;
tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu
chifukwa cha dzina lanu.
10 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti,
“Ali kuti Mulungu wawo?”
Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina
kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.
11 Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu;
ndi mphamvu ya dzanja lanu
muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.
12 Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri
kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.
13 Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu,
tidzakutamandani kwamuyaya,
kuchokera mʼbado ndi mʼbado
tidzafotokoza za matamando anu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.