Chronological
Hezekiya Apempha Thandizo kwa Yehova
37 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2 Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’ 4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”
5 Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8 Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka? 12 Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi? 13 Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova: 16 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 17 Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.
18 “Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo. 19 Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu. 20 Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
Yehova Ayankha Pemphero la Hezekiya
21 Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya. 22 Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa:
“Mwana wamkazi wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu,
akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
23 Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani?
Kodi iwe wafuwulira
ndi kumuyangʼana monyada ndani?
Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
24 Kudzera mwa amithenga ako
iwe wanyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta anga ochuluka
ndafika pamwamba pa mapiri,
pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni.
Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri,
ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini.
Ndafika pa msonga pake penipeni,
nkhalango yake yowirira kwambiri.
25 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndi kumva madzi akumeneko
ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’
26 “Kodi sunamvepo
kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale?
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndazichitadi,
kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
27 Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu,
ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi.
Anali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu omera pa denga,
umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
28 “Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe;
ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa,
ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
29 Chifukwa umandikwiyira Ine
ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa
njira yomwe unadzera pobwera.
30 “Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi:
“Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha,
ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha,
koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola,
mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
31 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire
adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
32 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka.
Changu cha Yehova Wamphamvuzonse
chidzachita zimenezi.
33 “Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya:
“Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi uliwonse.
Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango
kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
34 Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,”
akutero Yehova.
35 “Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”
36 Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse! 37 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.
38 Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.
Kudwala kwa Hezekiya
38 Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
2 Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti, 3 “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
4 Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti: 5 “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako. 6 Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
7 “ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza: 8 Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
9 Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
10 Ine ndinaganiza kuti
ndidzapita ku dziko la akufa
pamene moyo ukukoma.
11 Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,
mʼdziko la anthu amoyo,
sindidzaonanso mtundu wa anthu
kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
12 Nyumba yanga yasasuka
ndipo yachotsedwa.
Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga,
ngati munthu wowomba nsalu;
kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
13 Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa;
koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango,
ndipo mwakhala mukundisiya.
14 Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba,
ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula.
Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga.
Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”
15 Koma ine ndinganene chiyani?
Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi.
Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga,
ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
16 Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.
Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu.
Munandichiritsa ndi
kundikhalitsa ndi moyo.
17 Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere
kuti ndikhale ndi moyo;
Inu munandisunga
kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko
chifukwa mwakhululukira
machimo anga onse.
18 Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,
akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani.
Iwo amene akutsikira ku dzenje
sangakukhulupirireni.
19 Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,
monga mmene ndikuchitira ine lero lino;
abambo amawuza ana awo za
kukhulupirika kwanu.
20 Yehova watipulumutsa.
Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe
masiku onse a moyo wathu
mʼNyumba ya Yehova.
21 Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”
22 Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”
Nthumwi Zochokera ku Babuloni
39 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira. 2 Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
3 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
4 Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?”
Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
5 Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse: 6 Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. 7 Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
8 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu.
76 Mulungu amadziwika mu Yuda;
dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
2 Tenti yake ili mu Salemu,
malo ake okhalamo mu Ziyoni.
3 Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka,
zishango ndi malupanga, zida zankhondo.
Sela
4 Wolemekezeka ndinu,
wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
5 Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma,
Iwowo amagona tulo tawo totsiriza;
palibe mmodzi wamphamvu
amene angatukule manja ake.
6 Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo,
kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
7 Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa.
Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
8 Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo,
ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
9 pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze,
kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko.
Sela
10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando
ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.
11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse;
anthu onse omuzungulira abweretse mphatso
kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
12 Iye amaswa mzimu wa olamulira;
amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.