Chronological
Yehova Alanga Ahaziya
1 Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli. 2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake chammwamba ku Samariya, ndipo anavulala kwambiri. Choncho iye anatuma amithenga nawawuza kuti, “Pitani mukafunse kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, ngati ndichire matendawa.”
3 Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’ 4 Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka.
5 Amithenga aja atabwerera kwa mfumu, mfumuyo inawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?”
6 Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ”
7 Mfumu inafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo ndi kukuwuzani zimenezi amaoneka bwanji?”
8 Iwo anayankha kuti, “Munthuyo anavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake.”
Mfumu inati, “Munthu ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”
9 Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ”
10 Eliya anayankha mtsogoleriyo kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu makumi asanu akowo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
11 Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’ ”
12 Eliya anayankha kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu ako makumi asanuwo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
13 Ndipo mfumu inatumanso mtsogoleri wachitatu pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleri wachitatuyu anakwera pa phiripo ndi kugwada pamaso pa Eliya. Iye anayankhula mopemba kuti, “Munthu wa Mulungu, chonde musandiwononge ineyo pamodzi ndi atumiki makumi asanu anuwa! 14 Taonani, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kupsereza atsogoleri awiri pamodzi ndi anthu awo onse. Koma tsopano musawononge moyo wanga!”
15 Mngelo wa Yehova anati kwa Eliya, “Pita naye, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka natsika naye limodzi kupita kwa mfumu.
16 Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ” 17 Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula.
Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda. 18 Ntchito zina zonse zimene Ahaziya anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
Eliya Atengedwa Kupita Kumwamba
2 Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala. 2 Eliya anawuza Elisa kuti, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Beteli.”
Koma Elisa anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Beteli.
3 Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.”
4 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.”
Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko.
5 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.”
6 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.”
Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.
7 Anthu makumi asanu mwa ana a aneneri anawatsatira nayima chapatali moyangʼanana nawo ndipo Eliya ndi Elisa anayima mʼmphepete mwa Yorodani. 8 Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma.
9 Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”
Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.”
10 Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.”
11 Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. 12 Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.
13 Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani. 14 Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka.
15 Ndipo ana a aneneri ochokera ku Yeriko atamuona anati, “Mzimu wa Eliya wakhazikika pa Elisa.” Ndipo anapita kukakumana naye nagwada ndi kuweramitsa mitu yawo pansi pamaso pake. 16 Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.”
Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.”
17 Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze. 18 Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?”
Kuchiritsidwa kwa Madzi
19 Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.”
20 Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye.
21 Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ” 22 Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula.
Kusekedwa kwa Elisa
23 Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi” 24 Iye anatembenuka nawayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Nthawi yomweyo panatulukira zimbalangondo ziwiri kuchokera kuthengo, ndi kuphapo anyamata 42. 25 Ndipo iye anapita ku phiri la Karimeli. Pochoka kumeneko anabwerera ku Samariya.
Kuwukira kwa Mowabu
3 Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga. 3 Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.
4 Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna. 5 Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli. 6 Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse. 7 Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
8 Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?”
Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
9 Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
10 Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
11 Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?”
Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
12 Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
13 Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.”
Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
14 Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe. 15 Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.”
Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa, 16 ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’ 17 Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’ 18 Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu. 19 Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
20 Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
21 Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo. 22 Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo. 23 Ndipo iwo anati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha ndipo aphana. Amowabu, tsopano ndi nthawi yofunkha!”
24 Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu. 25 Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
26 Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera. 27 Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.
Mafuta a Mkazi Wamasiye
4 Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”
2 Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?”
Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.”
3 Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. 4 Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.”
5 Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta. 6 Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.”
Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.
7 Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”
Elisa Aukitsa Mwana wa Mayi wa ku Sunemu
8 Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya. 9 Mayiyo anawuza mwamuna wake kuti, “Taonani, ine ndikudziwa kuti munthu amene amadutsa pano nthawi zambiriyu ndi munthu woyera wa Mulungu. 10 Tiyeni timumangire kachipinda kakangʼono pa denga la nyumbayi ndi kumuyikiramo bedi ndi tebulo, mpando ndi nyale. Akabwera kuno azikhala mʼmenemo.”
11 Tsiku lina pamene Elisa anafika ku Sunemu, iye anakalowa mʼchipinda chake chija nagona mʼmenemo. 12 Iye anati kwa mtumiki wake Gehazi, “Muyitane Msunemuyu.” Ndipo anapita kukamuyitana mayiyo, ndipo anabwera nayima pamaso pa Elisa. 13 Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’ ”
Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.”
14 Elisa anafunsanso Gehazi kuti, “Kodi tingamuchitire chiyani?”
Gehazi anati, “Ndithu, mayiyu alibe mwana ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.”
15 Pamenepo Elisa anati, “Muyitane.” Choncho Gehazi anamuyitana, ndipo iye anabwera nayima pa khomo. 16 Elisa anati kwa mayiyo, “Nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, udzakhala utanyamula mwana wamwamuna mʼmanja mwako.”
Mayiyo anatsutsa zimenezi nanena kuti, “Ayi mbuye wanga. Inu munthu wa Mulungu, musanamize mdzakazi wanu!”
17 Koma mayi uja anakhala woyembekezera, ndipo chaka chotsatiracho, nthawi ngati yomweyo anabereka mwana wamwamuna monga momwe Elisa anamuwuzira.
18 Mwana uja anakula, ndipo tsiku lina anapita kwa abambo ake amene anali ndi anthu odula tirigu. 19 Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!”
Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.” 20 Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira. 21 Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.
22 Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”
23 Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.”
Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
24 Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.” 25 Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli.
Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo! 26 Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’ ”
Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
27 Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”
28 Tsono mayiyo anati, “Mbuye wanga, kodi ine ndinakupemphani mwana? Kodi sindinakuwuzeni kuti musandinamize?”
29 Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”
30 Koma mayi wake wa mwana uja anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Choncho Elisa ananyamuka natsatira mayiyo.
31 Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”
32 Ndipo Elisa atafika ku nyumbako, taonani, mwanayo anali wakufa atamugoneka pa bedi lake. 33 Elisa analowa mʼnyumbamo natseka chitseko. Anali awiri okha mʼchipindamo ndipo iye anapemphera kwa Yehova. 34 Kenaka anakwera pa bedi ndi kumugonera mwanayo, pakamwa pake panakhudzana ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, ndipo manja ake anakhudzana ndi manja a mwanayo. Pamene ankadzitambalitsa yekha pa mwanayo, thupi la mwanayo linayamba kufunda. 35 Elisa anatembenuka nayenda uku ndi uku kamodzi mʼchipindamo ndipo kenaka anakweranso pa bedi nagoneranso mwanayo. Mwanayo anayetsemula kasanu ndi kawiri ndipo anatsekula maso ake.
36 Elisa anayitana Gehazi ndipo anati, “Muyitane Msunemuyo.” Ndipo anaterodi. Mayiyo atabwera, Elisa anati, “Tenga mwana wako.” 37 Mayiyo analowa, nagwada pa mapazi a Elisa, naweramitsa mutu wake pansi. Kenaka ananyamula mwana wake natuluka.
Imfa mu Mʼphika
38 Elisa anabwerera ku Giligala ndipo ku dera limenelo kunali njala. Elisa akukumana ndi ana a aneneri, anati kwa mtumiki wake, “Ika mʼphika waukulu pa moto ndipo uwaphikire chakudya anthu awa.”
39 Mmodzi mwa ana aneneriwo anapita kuthengo kukafuna ndiwo ndipo anakapeza mpesa wakuthengo. Iye anathyolako zipatso zake nadzaza nsalu yake. Atabwerera, anazidula zipatsozo naziyika mu mʼphika, ngakhale kuti panalibe amene ankazidziwa. 40 Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.
41 Elisa anati, “Bweretsani ufa.” Iye anathira ufa mu mʼphikamo ndipo anati, “Perekani chakudyachi kwa anthu kuti adye.” Ndipo mu mʼphikamo munalibenso zoopsa.
Kudyetsa Anthu 100
42 Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”
43 Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?”
Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’ ” 44 Tsono iye anachipereka kwa anthuwo ndipo anadya china nʼkutsalako, molingana ndi mawu a Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.