Chronological
19 Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, 2 mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu. 3 Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”
Yehosafati Asankha Oweruza
4 Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 5 Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda. 6 Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. 7 Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”
8 Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu. 9 Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova. 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
11 “Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”
Yehosafati Agonjetsa Mowabu ndi Amoni
20 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.
2 Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). 3 Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.
5 Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 ndipo anati:
“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. 7 Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? 8 Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, 9 ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’
10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”
13 Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova.
14 Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano.
15 Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16 Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”
18 Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19 Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri.
20 Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21 Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:
“Yamikani Yehova
pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23 Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.
24 Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26 Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero.
27 Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28 Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga.
29 Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30 Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.
Kutha kwa Ufumu wa Yehosafati
31 Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32 Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33 Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.
34 Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
35 Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36 Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37 Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.
21 Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli. 3 Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.
Yehoramu Mfumu ya Yuda
4 Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli. 5 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. 6 Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 7 Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
8 Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. 9 Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku. 10 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda.
Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake. 11 Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.
12 Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti,
“Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda. 13 Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo. 14 Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu. 15 Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’ ”
16 Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi. 17 Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.
18 Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika. 19 Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.
20 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.
Ahaziya Mfumu ya Yuda
22 Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
2 Ahaziya anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Dzina la amayi ake linali Ataliya, chidzukulu cha Omuri.
3 Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika. 4 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake. 5 Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu, 6 kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu.
Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa.
7 Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu. 8 Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu anapeza atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya amene amatumikira Ahaziya, ndipo anawapha. 9 Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu.
Ataliya ndi Yowasi
10 Ataliya, amayi ake a Ahaziya, ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakapha onse a banja laufumu la Yuda. 11 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, momuba ndi kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene amati aphedwe ndipo anamuyika iye ndi mlezi wake mʼchipinda chogona. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa wansembe Yehoyada, yemwe anali mlongo wake wa Ahaziya anamubisa mwanayo kuti Ataliya asamuphe. 12 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi iwo mu Nyumba ya Mulungu kwa zaka zisanu ndi chimodzi muulamuliro wa Ataliya.
23 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. 2 Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu, 3 msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu.
Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide. 4 Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo, 5 ndi limodzi la magawo atatu likakhale ku nyumba yaufumu ndipo limodzi la magawo atatu likakhale ku chipata cha Maziko ndipo anthu ena onse akakhale mʼmabwalo a Nyumba ya Yehova. 6 Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula. 7 Alevi akhale mozungulira mfumu, munthu aliyense ali ndi chida chake mʼmanja. Aliyense amene alowe mʼNyumba ya Mulungu ayenera kuphedwa. Mukhale nayo pafupi mfumu kulikonse kumene izipita.”
8 Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite. 9 Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu. 10 Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu.
11 Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
12 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga ndi kukondwerera mfumu, anapita ku Nyumba ya Yehova komwe kunali anthuko. 13 Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
14 Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,” 15 choncho anamugwira pamene amafika pa chipata cha Kavalo pa bwalo la nyumba yaufumu, ndipo anamuphera pamenepo.
16 Tsono Yehoyada anachita pangano, iye mwini ndi anthu onse ndiponso mfumu kuti adzakhala anthu a Yehova. 17 Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo.
18 Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira. 19 Ndipo anayika alonda a pa khomo pa zipata za Nyumba ya Yehova kuti aliyense amene ndi odetsedwa asalowe.
20 Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka, 21 ndipo anthu onse a mʼderali anakondwera. Tsono mu mzinda munali bata chifukwa Ataliya anaphedwa ndi lupanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.