Chronological
Beni-Hadadi Athira Nkhondo Samariya
20 Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. 2 Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, 3 “Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ”
4 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.”
5 Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. 6 Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”
7 Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”
8 Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.”
9 Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.
10 Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”
11 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ”
12 Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.
Ahabu Agonjetsa Beni-Hadadi
13 Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
14 Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”
Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”
Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”
Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”
15 Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. 16 Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. 17 Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.
Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”
18 Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.”
19 Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. 20 Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. 21 Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa.
22 Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”
23 Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo. 24 Inu chitani izi: chotsani mafumu onse pa maudindo awo ndipo mʼmalo mwawo muyikemo atsogoleri a ankhondo. 25 Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo.
26 Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli. 27 Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo.
28 Munthu wa Mulungu anabwera, nawuza mfumu ya Israeli kuti, “Yehova akuti, ‘Popeza Aaramu akuganiza kuti Yehova ndi mulungu wa ku mapiri, osati wa ku zigwa, Ine ndidzapereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
29 Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha. 30 Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.
31 Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.”
32 Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ”
Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.”
33 Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!”
Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake.
34 Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.”
Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite.
Mneneri Adzudzula Ahabu
35 Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana.
36 Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha.
37 Mneneriyo anapeza munthu wina ndipo anamuwuza kuti, “Chonde, menye.” Choncho munthuyo anamumenya ndi kumuvulaza. 38 Pamenepo mneneriyo anapita nakayima pa msewu kudikirira mfumu. Iye anadzibisa nakulunga nsalu nkhope yake. 39 Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’ 40 Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.”
Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.”
41 Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. 42 Iye anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chakuti mwamasula munthu amene Ine ndinati ndi woyenera kuphedwa, inuyo ndi amene mudzaphedwe mʼmalo mwa iyeyo, anthu anu mʼmalo mwa anthu ake.’ ” 43 Mwachisoni ndi mokwiya, mfumu ya Israeli inapita ku nyumba yake yaufumu ku Samariya.
Munda Wamphesa wa Naboti
21 Zitatha izi, panachitika nkhani yokhudza Naboti wa ku Yezireeli amene anali ndi munda wamphesa ku Yezireeli, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu, mfumu ya ku Samariya. 2 Ahabu anawuza Naboti kuti, “Patse munda wako wa mpesa kuti ukhale munda wanga wa ndiwo zamasamba, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga yaufumu. Mosinthana ndi mundawu ndidzakupatsa wina wabwino, kapena ngati ungafune, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawu.”
3 Koma Naboti anayankha Ahabu kuti, “Pali Yehova, sindingakupatseni cholowa cha makolo anga.”
4 Pamenepo Ahabu anapita ku nyumba yake, wachisoni ndi wokwiya chifukwa Naboti wa ku Yezireeli anamuwuza kuti, “Sindidzakupatsani cholowa cha makolo anga.” Ahabu anakagona pa bedi lake atayangʼana kumbali ndipo anakana chakudya.
5 Yezebeli mkazi wake analowa ndipo anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuoneka achisoni? Chifukwa chiyani simukufuna chakudya?”
6 Ahabu anayankha mkazi wake kuti, “Chifukwa chake nʼchakuti ine ndinamuwuza Naboti wa ku Yezireeli kuti, ‘Gulitse munda wako wa mpesa kapena ngati ungakonde ine ndidzakupatsa munda wina wabwino mʼmalo mwake.’ Koma iye anandiyankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wa mpesa.’ ”
7 Ndipo Yezebeli mkazi wake anati, “Kodi umu ndi mmene mumachitira ngati mfumu ya Israeli? Dzukani, idyani! Sangalalani. Ine ndidzakutengerani munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli.”
8 Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu, nawadinda chidindo cha mfumu, nawatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake. 9 Mʼmakalatamo Yezebeli analemba kuti:
“Lengezani kuti anthu asale chakudya ndipo muyike Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. 10 Koma muyike anthu awiri oyipa mtima moyangʼanana naye ndipo iwo achitire umboni kuti watemberera Mulungu ndiponso mfumu. Ndipo mumutulutse ndi kumuponya miyala ndi kumupha.”
11 Choncho akuluakulu ndi anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake anachita monga analamulira Yezebeli mʼmakalata amene anawalembera. 12 Iwo analengeza kuti anthu asale chakudya ndipo anayika Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. 13 Ndipo anthu awiri oyipa anabwera nakhala moyangʼanana naye ndipo anamunenera zoyipa Naboti pamaso pa anthu, ponena kuti, “Naboti watemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Choncho anamutulutsira kunja kwa mzinda ndi kumuponya miyala ndi kumupha. 14 Atatero anatumiza mawu kwa Yezebeli akuti, “Naboti amuponya miyala ndipo wafa.”
15 Yezebeli atangomva kuti Naboti amuponya miyala ndipo wafa, iye anakamuwuza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli umene anawukaniza kukugulitsani. Naboti sali moyonso, koma wafa.” 16 Ahabu atamva kuti Naboti wafa, ananyamuka kukatenga munda wamphesa wa Naboti.
17 Ndipo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, 18 “Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya Israeli amene amalamulira ku Samariya. Pano ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene wapita kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake. 19 Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ”
20 Ahabu anati kwa Eliya, “Tsono wandipeza, iwe mdani wanga!”
Eliya anayankha kuti, “Inde ndakupezani chifukwa mwadzigulitsa kuti muchite zoyipa pamaso pa Yehova. 21 Iye akuti ‘Taonani, ine ndidzabweretsa mavuto pa iwe. Ndidzawononga kotheratu zidzukulu zako ndi kuchotsa mu Israeli munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu. 22 Ndidzawononga nyumba yako monga momwe ndinawonongera nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya, chifukwa wandikwiyitsa Ine ndi kuchimwitsa Israeli.’
23 “Ndipo kunena za Yezebeli, Yehova akuti, ‘Agalu adzadya Yezebeli mʼmbali mwa khoma la Yezireeli.’
24 “Agalu adzadya munthu aliyense wa nyumba ya Ahabu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya aliyense wofera ku thengo.”
25 (Kunalibe munthu ngati Ahabu, amene anadzigulitsa kuchita zoyipa pamaso pa Yehova, amene anakopedwa ndi mkazi wake Yezebeli. 26 Iye anachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga mmene ankachitira Aamori amene Yehova anawachotsa pamene Aisraeli ankafika).
27 Ahabu atamva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake, navala ziguduli ndi kusala chakudya. Anagona pa ziguduli, nayenda pangʼonopangʼono.
28 Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, 29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Chifukwa wadzichepetsa, sindidzabweretsa mavuto amenewa pa nthawi ya moyo wake, koma ndidzawabweretsa pa nyumba yake pa nthawi ya mwana wake.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.