Chronological
Aisraeli Awukira Rehobowamu
10 Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse anapita kumeneko kuti akamulonge ufumu. 2 Yeroboamu mwana wa Nebati atamva zimenezi (Iye anali ku Igupto, kumene anapita pothawa mfumu Solomoni) anabwerako kuchokera ku Igupto. 3 Kotero anthu anakayitana Yeroboamu ndipo iye ndi Aisraeli onse anapita kwa Rehobowamu ndi kumuwuza kuti, 4 “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”
5 Rehobowamu anayankha kuti, “Mukabwerenso pakapita masiku atatu.” Choncho anthuwo anachoka.
6 Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”
7 Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.”
8 Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira. 9 Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ndi otani? Kodi tiwayankhe chiyani anthu amene akunena kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anayika pa ife?’ ”
10 Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga. 11 Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’ ”
12 Tsiku lachitatu Yeroboamu ndi anthu onse anabwerera kwa Rehobowamu monga ananenera mfumu kuti, “Mukabwerenso kwa ine pakapita masiku atatu.” 13 Mfumu inawayankha mwankhanza, pokana malangizo a akuluakulu aja. 14 Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” 15 Kotero mfumu sinamvere anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Mulungu, kukwaniritsa mawu amene Yehova ananena kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
16 Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti,
“Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide,
gawo lanji mwa mwana wa Yese?
Inu Aisraeli! Pitani kwanu.
Iwe Davide! Yangʼana banja lako.”
Kotero Aisraeli onse anapita kwawo. 17 Koma Rehobowamu anakhala akulamulirabe Aisraeli amene amakhala mʼmizinda ya Yuda.
18 Mfumu Rehobowamu inatuma Hadoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli anamugenda miyala ndi kumupha. Koma mfumu Rehobowamu anakwera galeta lake ndi kuthawira ku Yerusalemu. 19 Motero Israeli wakhala akuwukira banja la Davide mpaka lero lino.
11 Rehobowamu atafika ku Yerusalemu anasonkhanitsa asilikali 180,000 a fuko la Yuda ndi Benjamini kuti akachite nkhondo ndi Israeli, kuti abwezeretse ufumu kwa Rehobowamu.
2 Koma Yehova anayankhula ndi munthu wa Mulungu Semaya kuti, 3 “Kawuze Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Aisraeli onse ali mu Yuda ndi Benjamini kuti, 4 ‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu. Pitani kwanu, aliyense wa inu, pakuti izi ndikuchita ndine.’ ” Choncho anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera osapita kukamenyana ndi Yeroboamu.
Rehobowamu Akhwimitsa Chitetezo cha Yuda
5 Rehobowamu amakhala mu Yerusalemu ndipo anamanga mizinda ya chitetezo iyi mu Yuda: 6 Betelehemu, Etamu, Tekowa, 7 Beti Zuri, Soko, Adulamu, 8 Gati, Maresa, Zifi, 9 Adoraimu, Lakisi, Azeka, 10 Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini. 11 Iye anakhwimitsa chitetezo cha mizindayi ndipo anayikamo atsogoleri a ankhondo, pamodzi ndi chakudya, mafuta a olivi ndi vinyo. 12 Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.
13 Ansembe ndi Alevi a mʼmadera onse a Israeli anakhala mbali ya Rehobowamu. 14 Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova. 15 Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga. 16 Anthu ochokera fuko lililonse la Israeli amene anatsimikiza mitima yawo kufunafuna Yehova Mulungu wa Israeli, ankapitabe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 17 Iwo analimbikitsa ufumu wa Yuda, ndipo anathandiza Rehobowamu mwana wa Solomoni kwa zaka zitatu. Pa nthawi imeneyi iye amatsatira zochita za Davide ndi Solomoni.
Banja la Rehobowamu
18 Rehobowamu anakwatira Mahalati, amene abambo ake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo amayi ake anali Abihaili, mwana wa Eliabu, mwana wa Yese. 19 Mkaziyo anamubereka ana aamuna awa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu. 20 Kenaka anakwatira Maaka, mwana wamkazi wa Abisalomu, amene anamubereka Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti. 21 Rehobowamu ankamukonda Maaka mwana wa Abisalomu kuposa aliyense mwa akazi ake ndi azikazi. Iye anali ndi akazi 18, azikazi 60, ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60.
22 Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri pa abale ake, ndi cholinga choti adzakhale mfumu. 23 Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.
Sisaki Athira Nkhondo Dziko la Yuda
12 Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova. 2 Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu. 3 Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto. 4 Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu.
5 Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’ ”
6 Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.”
7 Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki. 8 Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.”
9 Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga. 10 Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu. 11 Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda.
12 Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.
13 Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni. 14 Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.
15 Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 16 Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.