Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mlaliki 7-12

Nzeru

Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino,
    ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro
    kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero:
Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense;
    anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka,
    pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa,
    koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru
    kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati
    kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika,
    izinso ndi zopandapake.

Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru,
    ndipo chiphuphu chimawononga mtima.

Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake,
    ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako,
    pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.

10 Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?”
    pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.

11 Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino
    ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 Nzeru ndi chitetezo,
    monganso ndalama zili chitetezo,
koma phindu la chidziwitso ndi ili:
    kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.

13 Taganizirani zimene Mulungu wazichita:

ndani angathe kuwongola chinthu
    chimene Iye anachipanga chokhota?
14 Pamene zinthu zili bwino, sangalala;
    koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino:
Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo,
    ndiponso nthawi imene si yabwinoyo.
Choncho munthu sangathe kuzindikira
    chilichonse cha mʼtsogolo mwake.

15 Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi:

munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake,
    ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Usakhale wolungama kwambiri
    kapena wanzeru kwambiri,
    udziwonongerenji wekha?
17 Usakhale woyipa kwambiri,
    ndipo usakhale chitsiru,
    uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi,
    ndipo usataye njira inayo.
    Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.

19 Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru
    kupambana olamulira khumi a mu mzinda.

20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi
    amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.

21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula,
    mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako
    kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.

23 Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati,

“Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,”
    koma nzeruyo inanditalikira.
24 Nzeru zimene zilipo,
    zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri,
    ndani angathe kuzidziwa?
25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe,
    ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira
ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru
    ndiponso kupusa kwake kwa misala.

26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa,
    mkazi amene ali ngati khoka,
amene mtima wake uli ngati khwekhwe,
    ndipo manja ake ali ngati maunyolo.
Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo,
    koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.

27 Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi:

“Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28     pamene ine ndinali kufufuzabe
    koma osapeza kanthu,
ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000,
    koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi:
    Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama,
    koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”
Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?
    Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu?
Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu
    ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.

Za Kumvera Mfumu

Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu. Usafulumire kuchoka pamaso pa mfumu. Usawumirire chinthu choyipa, pakuti mfumu idzachita chilichonse chomwe imasangalatsidwa nacho. Popeza mawu a mfumu ali ndi mphamvu, ndani anganene kwa mfumuyo kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”

Aliyense amene amamvera lamulo lake sadzapeza vuto lililonse,
    ndipo munthu wanzeru amadziwa nthawi yoyenera ndi machitidwe ake.
Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse,
    ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri.

Popeza palibe munthu amene amadziwa zamʼtsogolo,
    ndani angamuwuze zomwe zidzachitika mʼtsogolo?
Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yolamulira mpweya wa moyo kuti athe kuwusunga,
    choncho palibe amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa yake.
Nkhondo sithawika; tsono anthu ochita zoyipa,
    kuyipa kwawoko sikudzawapulumutsa.

Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza. 10 Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.

11 Pamene chigamulo cha anthu opalamula mlandu chikuchedwa, mitima ya anthu imadzaza ndi malingaliro ochita zolakwa. 12 Ngakhale munthu woyipa apalamule milandu yambirimbiri, nʼkumakhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu owopa Mulungu zinthu zidzawayendera bwino, omwe amapereka ulemu pamaso pa Mulungu. 13 Koma popeza oyipa saopa Mulungu zinthu sizidzawayendera bwino, ndipo moyo wawo sudzakhalitsa monga mthunzi.

14 Palinso chinthu china chopanda phindu chomwe chimachitika pa dziko lapansi: anthu olungama amalangidwa ngati anthu osalungama. Pamene oyipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. 15 Nʼchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake amene Mulungu wamupatsa pansi pano.

16 Pamene ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe nzeru ndi kuonetsetsa ntchito za munthu pa dziko lapansi, osapeza tulo usana ndi usiku, 17 pamenepo ndinaona zonse zimene Mulungu anazichita. Palibe munthu amene angathe kuzimvetsa zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse kuzifufuza, sangathe kupeza tanthauzo lake. Ngakhale munthu wanzeru atanena kuti iye amadziwa, sangathe kuzimvetsetsa zinthuzo.

Mathero a Zinthu Zonse ndi Wofanana

Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe.

Zomwe zimachitikira munthu wabwino,
    zimachitikiranso munthu wochimwa,
zomwe zimachitikira amene amalumbira,
    zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.

Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa. Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa!

Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,
    koma akufa sadziwa kanthu;
alibe mphotho ina yowonjezera,
    ndipo palibe amene amawakumbukira.
Chikondi chawo, chidani chawo
    ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale;
sadzakhalanso ndi gawo
    pa zonse zochitika pansi pano.

Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako. Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse. Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano. 10 Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.

11 Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:

opambana pa kuthamanga si aliwiro,
    kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,
ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,
    kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,
    kapena okomeredwa mtima si ophunzira;
koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.

12 Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti:

monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde,
    kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha,
chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa,
    pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.

Nzeru Iposa Uchitsiru

13 Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri: 14 Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. 15 Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. 16 Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.

17 Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambiri
    kupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru.
18 Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo,
    koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.
10 Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira,
    choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino,
    koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu,
    zochita zake ndi zopanda nzeru
    ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
Ngati wolamulira akukwiyira,
    usachoke pa ntchito yako;
    kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.

Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano,
    kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba,
    pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
Ndaona akapolo atakwera pa akavalo,
    pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.

Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha;
    amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo;
    amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.

10 Ngati nkhwangwa ili yobuntha
    yosanoledwa,
pamafunika mphamvu zambiri potema,
    koma luso limabweretsa chipambano.

11 Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka
    ngati njokayo yakuluma kale.

12 Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa,
    koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
13 Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa;
    potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
14     ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu.

Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo,
    ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?

15 Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa;
    ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.

16 Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana,
    ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
17 Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka
    ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake,
    kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.

18 Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka;
    ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.

19 Phwando ndi lokondweretsa anthu,
    ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo,
    koma ndalama ndi yankho la chilichonse.

20 Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako,
    kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako,
pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako
    nʼkukafotokoza zomwe wanena.

Kuponya Chakudya pa Madzi

11 Ponya chakudya chako pa madzi,
    udzachipezanso patapita masiku ambiri.
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
    pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.

Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,
    imagwetsa mvula pa dziko lapansi.
Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,
    ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
Amene amayangʼana mphepo sadzadzala;
    amene amayangʼana mitambo sadzakolola.

Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,
    kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,
momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,
    Mlengi wa zinthu zonse.

Dzala mbewu zako mmawa
    ndipo madzulo usamangoti manja lobodo,
pakuti sudziwa chimene chidzapindula,
    mwina ichi kapena icho,
    kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.

Kumbukira Mlengi Wako

Kuwala nʼkwabwino,
    ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
Munthu akakhala wa zaka zambiri,
    mulekeni akondwerere zaka zonsezo,
koma iye azikumbukira masiku a mdima,
    pakuti adzakhala ochuluka.
    Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.

Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,
    ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.
Tsatira zimene mtima wako ukufuna,
    ndiponso zimene maso ako akuona,
koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo
    Mulungu adzakuweruza.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,
    upewe zokupweteka mʼthupi mwako,
    pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
12 Uzikumbukira mlengi wako
    masiku a unyamata wako,
masiku oyipa asanafike,
    nthawi isanafike pamene udzanena kuti,
    “Izi sizikundikondweretsa.”
Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,
    mwezi ndi nyenyezi zidzada.
    Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,
    miyendo yako idzafowoka,
pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,
    ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
Makutu ako adzatsekeka,
    ndipo sudzamva phokoso lakunja;
sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo
    kapena kulira kwa mbalame mmawa.
Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,
    amaopa kuyenda mʼmisewu;
Mutu umatuwa kuti mbuu,
    amayenda modzikoka ngati ziwala
    ndipo chilakolako chimatheratu.
Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya
    ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.

Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,
    kapena mbale yagolide isanasweke;
mtsuko usanasweke ku kasupe,
    kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,
    mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.

“Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.
    “Zonse ndi zopandapake!”

Mawu Otsiriza

Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri. 10 Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.

11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12 Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi.

Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.

13 Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:
    uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,
pakuti umenewu ndiwo udindo
    wa anthu onse.
14 Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,
    kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,
    kaya zabwino kapena zoyipa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.