Chronological
22 Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri;
kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.
2 Wolemera ndi wosauka ndi ofanana;
onsewa anawalenga ndi Yehova.
3 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.
4 Mphotho ya munthu wodzichepetsa
ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.
5 Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha,
koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.
6 Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.
7 Wolemera amalamulira wosauka,
ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.
8 Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto,
ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.
9 Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika,
pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.
10 Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha;
mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.
11 Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino,
adzakhala bwenzi la mfumu.
12 Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu,
koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.
13 Munthu waulesi amati,
“Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”
14 Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama;
amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.
15 Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,
koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.
16 Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake,
ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.
Malangizo a Anthu Anzeru
17 Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru;
uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.
18 Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako
ndi wokonzeka kuziyankhula.
19 Ndakuphunzitsa zimenezi lero
koma makamaka uziopa Yehova.
20 Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu
okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21 malangizo okudziwitsa zolungama
ndi zoona
ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?
22 Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka,
ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,
23 pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo
ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.
24 Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima
ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya
25 kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake
ndi kukodwa mu msampha.
26 Usakhale munthu wopereka chikole
kapena kukhala mboni pa ngongole;
27 ngati ulephera kupeza njira yolipirira
adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.
28 Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale
amene anayikidwa ndi makolo ako.
29 Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake?
Iye adzatumikira mafumu;
sadzatumikira anthu wamba.
23 Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira,
uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,
2 ngati ndiwe munthu wadyera
udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.
3 Usasirire zakudya zake,
pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.
4 Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma,
ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.
5 Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo.
Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi
ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.
6 Usadye chakudya cha munthu waumbombo,
usalakalake zakudya zake zokoma;
7 paja iye ndi munthu amene
nthawi zonse amaganizira za mtengo wake
ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,”
koma sakondweretsedwa nawe.
8 Udzasanza zimene wadyazo
ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.
9 Usayankhule munthu wopusa akumva,
pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.
10 Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale
kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,
11 paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;
iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.
12 Mtima wako uzikhala pa malangizo
ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.
13 Usaleke kumulangiza mwana;
ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.
14 Ukamukwapula ndi tsatsa
udzapulumutsa moyo wake.
15 Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru,
inenso mtima wanga udzakondwera.
16 Mtima wanga udzakondwera
pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.
17 Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa,
koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.
18 Ndithu za mʼtsogolo zilipo
ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.
19 Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru,
mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.
20 Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera
kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.
21 Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi
ndipo aulesi adzavala sanza.
22 Mvera abambo ako amene anakubala,
usanyoze amayi ako pamene akalamba.
23 Gula choonadi ndipo usachigulitse;
ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.
24 Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;
Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.
25 Abambo ndi amayi ako asangalale;
amene anakubereka akondwere!
26 Mwana wanga, undikhulupirire
ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.
27 Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama;
ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.
28 Amabisala ngati mbala yachifwamba,
ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.
29 Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni?
Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo?
Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?
30 Ndi amene amakhalitsa pa mowa,
amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.
31 Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo,
pamene akuwira mʼchikho
pamene akumweka bwino!
32 Potsiriza pake amaluma ngati njoka,
ndipo amajompha ngati mphiri.
33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo
ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.
34 Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja,
kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.
35 Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe!
Andimenya koma sindinamve kanthu!
Kodi ndidzuka nthawi yanji?
Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”
24 Usachitire nsanje anthu oyipa,
usalakalake kuti uzikhala nawo,
2 pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa,
ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.
3 Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,
ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
4 Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake
ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.
5 Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri,
ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
6 Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo.
Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.
7 Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru;
chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.
8 Amene amakonzekera kuchita zoyipa
adzatchedwa mvundulamadzi.
9 Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo,
ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.
10 Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti
mphamvu yako ndi yochepadi!
11 Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe;
uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12 Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,”
kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi?
Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi?
Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
13 Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino;
uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14 Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;
ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,
ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
15 Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa.
Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16 paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso.
Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.
17 Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako.
Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18 Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo,
angaleke kukwiyira mdaniyo.
19 Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa
kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20 paja munthu woyipa alibe tsogolo.
Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.
21 Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu,
ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22 awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi.
Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?
Malangizo Enanso a Anthu Anzeru
23 Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:
Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24 Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,”
anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25 Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino
ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
26 Woyankhula mawu owona
ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
27 Ugwiriretu ntchito zako zonse,
makamaka za ku munda
ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
28 Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,
kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29 Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine;
ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
30 Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi
ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31 Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga,
mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa,
ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32 Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga
ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33 Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,”
kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34 umphawi udzafika pa iwe ngati mbala
ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.