Chronological
Solomoni Apempha Nzeru
3 Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu. 2 Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba. 3 Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.
4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe. 5 Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
6 Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.
7 “Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. 8 Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. 9 Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. 13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. 14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.” 15 Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.
Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse.
Kuweruza Kolungama
16 Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake. 17 Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu. 18 Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.
19 “Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera. 20 Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga. 21 Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”
22 Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.”
Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
23 Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ”
24 Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu. 25 Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”
26 Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!”
Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”
27 Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”
28 Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.
Nduna za Solomoni ndi Abwanamkubwa
4 Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse. 2 Nduna zake zikuluzikulu zinali izi:
Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;
3 Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi;
Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;
4 Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo;
Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;
5 Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo;
Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;
6 Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu;
Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.
7 Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka. 8 Mayina awo ndi awa:
Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;
9 Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;
10 Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);
11 Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);
12 Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;
13 Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).
14 Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;
15 Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);
16 Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;
17 Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;
18 Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;
19 Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.
Chakudya cha Tsiku ndi Tsiku cha Solomoni
20 Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala. 21 Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.
22 Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa, 23 ngʼombe khumi zonenepa zodyetsera mʼkhola, ngʼombe za ku busa makumi awiri, ndiponso nkhosa ndi mbuzi 100, pamodzinso ndi mbawala, agwape, mphoyo ndi mbalame zoweta zonona. 24 Pakuti ankalamulira dziko lonse la kumadzulo kwa mtsinje wa Yufurate kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza, mafumu onse a kumadzulo kwa Mtsinje, ndipo anali pa mtendere ndi mayiko onse ozungulira. 25 Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.
26 Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta.
27 Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse. 28 Ankabweretsanso ku malo ake ofunikira muyeso wawo wa barele ndi udzu wa akavalo okoka magaleta ndiponso akavalo ena.
Nzeru za Solomoni
29 Mulungu anamupatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka ndipo nzeru zake zinali zochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 30 Nzeru za Solomoni zinali zoposa nzeru za anthu onse a Kummawa ndiponso nzeru zonse za ku Igupto. 31 Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira. 32 Solomoni anapeka miyambi 3,000 ndi kulemba nyimbo 1,005. 33 Iye ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope khomera pa khoma. Iye ankaphunzitsanso za nyama ndi mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba. 34 Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.
Solomoni Apempha Nzeru
1 Solomoni mwana wa Davide anakhazikika molimbika mu ufumu wake, pakuti Yehova Mulungu wake anali naye ndipo anamukweza kwambiri.
2 Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja. 3 Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja. 4 Davide anabweretsa Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriyati Yearimu, ndi kulikhazika kumalo kumene analikonzera popeza analimangira tenti mu Yerusalemu. 5 Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko. 6 Solomoni anapita pamene panali guwa lansembe lamkuwa pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano ndipo anapereka nsembe zopsereza 1,000.
7 Usiku umenewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni ndipo anati kwa iye, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
8 Solomoni anayankha Mulungu kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Davide abambo anga ndipo mwayika ine kukhala mfumu mʼmalo mwake. 9 Tsopano Inu Yehova Mulungu, lolani kuti lonjezo lanu kwa abambo anga Davide likwaniritsidwe, pakuti mwandiyika kukhala mfumu ya anthu anu amene ndi ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. 10 Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
11 Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo, 12 Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”
13 Kotero Solomoni anabwerera ku Yerusalemu kuchoka kumalo opembedzerako a ku Gibiyoni, ku tenti ya msonkhano ndipo analamulira Israeli.
14 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu. 15 Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. 16 Solomoni amagula akavalo ku Igupto ndi Kuwe pakuti anthu amalonda a mfumu amakawagula ku Kuwe. 17 Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu.
Salimo la Solomoni.
72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
anthu anu ozunzika mosakondera.
3 Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
4 Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
adzaphwanya ozunza anzawo.
5 Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
6 Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
7 Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.
8 Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
9 Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
ndipo mitundu yonse idzamutumikira.
12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
15 Iye akhale ndi moyo wautali;
golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.
Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
Ameni ndi Ameni.
20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.