Chronological
Fuko la Levi
23 Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.
2 Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi. 3 Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000. 4 Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza. 5 Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”
6 Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Banja la Geresoni
7 Ana a Geresoni:
Ladani ndi Simei.
8 Ana a Ladani:
Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.
9 Ana a Simei:
Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.
Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.
10 Ndipo ana a Simei anali:
Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.
Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.
11 Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
Banja la Kohati
12 Ana a Kohati:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.
13 Ana a Amramu:
Aaroni ndi Mose.
Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya. 14 Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.
15 Ana a Mose:
Geresomu ndi Eliezara.
16 Zidzukulu za Geresomu:
Mtsogoleri anali Subaeli.
17 Zidzukulu za Eliezara:
Mtsogoleri anali Rehabiya.
Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.
18 Ana a Izihari:
Mtsogoleri anali Selomiti.
19 Ana a Hebroni:
Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.
20 Ana a Uzieli:
Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.
Banja la Merari
21 Ana a Merari:
Mahili ndi Musi.
Ana a Mahili:
Eliezara ndi Kisi.
22 Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.
23 Ana a Musi:
Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.
24 Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova. 25 Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya, 26 sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.” 27 Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.
28 Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu. 29 Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake. 30 Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo, 31 ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
32 Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.
Magulu a Ansembe
24 Magulu a ana a Aaroni anali awa:
Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 2 Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. 3 Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. 4 Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. 5 Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.
6 Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
7 Maere woyamba anagwera Yehoyaribu,
achiwiri anagwera Yedaya,
8 achitatu anagwera Harimu,
achinayi anagwera Seorimu,
9 achisanu anagwera Malikiya,
achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,
10 achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi,
achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,
11 achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa,
a khumi anagwera Sekaniya,
12 a 11 anagwera Eliyasibu,
a 12 anagwera Yakimu,
13 a 13 anagwera Hupa,
a 14 anagwera Yesebeabu,
14 a 15 anagwera Biliga,
a 16 anagwera Imeri,
15 a 17 anagwera Heziri,
a 18 anagwera Hapizezi,
16 a 19 anagwera Petahiya,
a 20 anagwera Ezekieli,
17 a 21 anagwera Yakini,
a 22 anagwera Gamuli,
18 a 23 anagwera Delaya,
ndipo a 24 anagwera Maaziya.
19 Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
Alevi Ena Onse
20 Za zidzukulu zina zonse za Levi:
Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli;
kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.
21 Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake:
Mtsogoleri anali Isiya.
22 Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti;
kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.
23 Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.
24 Mwana wa Uzieli: Mika;
kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.
25 Mʼbale wa Mika: Isiya;
kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.
26 Ana a Merari: Mahili ndi Musi.
Mwana wa Yaaziya: Beno.
27 Ana a Merari:
Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
28 Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.
29 Kuchokera kwa Kisi:
Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.
30 Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti.
Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. 31 Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.
Anthu Oyimba Nyimbo
25 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
2 Kuchokera kwa ana a Asafu:
Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.
3 Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake:
Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.
4 Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake:
Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti. 5 Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
6 Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu. 7 Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288. 8 Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.
9 Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, | |
ana ndi abale ake. | 12 |
Maere achiwiri anagwera Gedaliya, | |
ndi abale ake ndi ana ake. | 12 |
10 Maere achitatu anagwera Zakuri, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
11 Maere achinayi anagwera Iziri, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
12 Maere achisanu anagwera Netaniya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
17 Maere a khumi anagwera Simei, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
18 Maere a 11 anagwera Azareli, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
19 Maere a 12 anagwera Hasabiya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
20 Maere a 13 anagwera Subaeli, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
21 Maere a 14 anagwera Matitiya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
22 Maere a 15 anagwera Yeremoti, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
23 Maere a 16 anagwera Hananiya, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
25 Maere a 18 anagwera Hanani, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
26 Maere a 19 anagwera Maloti, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
27 Maere a 20 anagwera Eliyata, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
28 Maere a 21 anagwera Hotiri, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
29 Maere a 22 anagwera Gidaliti, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
30 Maere a 23 anagwera Mahazioti, | |
ana ake ndi abale ake. | 12 |
31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, | |
ana ake ndi abale ake | 12. |
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.