Chronological
Salimo la Davide.
26 Weruzeni Inu Yehova
pakuti ndakhala moyo wosalakwa.
Ndadalira Yehova
popanda kugwedezeka.
2 Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
3 pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
4 Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,
kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
5 Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa
ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
6 Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga
ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
7 kulengeza mofuwula za matamando anu
ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
8 Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,
malo amene ulemerero wanu umapezekako.
9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,
moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,
dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;
mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.
12 Ndayima pa malo wopanda zovuta
ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
40 Mofatsa ndinadikira Yehova
Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
2 Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
3 Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
4 Ndi wodala munthu
amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
Inu simunazipemphe.
7 Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
Mʼbuku mwalembedwa za ine.
8 Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”
9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
sinditseka milomo yanga
monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
pa msonkhano waukulu.
11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
12 Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;
machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.
Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,
ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.
13 Pulumutseni Yehova;
Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene amakhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mwamanyazi.
15 Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!”
abwerere akuchita manyazi.
16 Koma iwo amene amafunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
17 Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa;
Ambuye andiganizire.
Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga;
Inu Mulungu wanga, musachedwe.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide.
58 Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?
Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?
2 Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,
ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.
3 Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;
kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.
4 Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,
ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.
5 Imene simva liwu la munthu wamatsenga,
ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.
6 Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,
Yehova khadzulani mano a mikango!
7 Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda
pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.
8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda;
ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.
9 Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku,
kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.
10 Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango,
pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.
11 Ndipo anthu adzanena kuti,
“Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho;
zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.
61 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;
mvetserani pemphero langa.
2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu
ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;
tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,
nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.
4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya
ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;
mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.
6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,
zaka zake kwa mibado yochuluka.
7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;
ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.
8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu
ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.
62 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;
chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.
3 Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?
Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,
ngati mpanda wogwedezeka?
4 Iwo akufunitsitsa kumugwetsa
kuti achoke pa malo ake apamwamba.
Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.
Ndi pakamwa pawo amadalitsa
koma mʼmitima yawo amatemberera.
5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
khuthulani mitima yanu kwa Iye,
pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
Sela
9 Anthu wamba ndi mpweya chabe;
anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
musayike mtima wanu pa icho.
11 Mulungu wayankhula kamodzi,
ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
molingana ndi ntchito zake.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
64 Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;
tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.
2 Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,
ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.
3 Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,
amaponya mawu awo olasa ngati mivi.
4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;
amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.
5 Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,
amayankhula zobisa misampha yawo;
ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,
“Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”
Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;
mwadzidzidzi adzakanthidwa.
8 Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa
ndi kuwasandutsa bwinja;
onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.
9 Anthu onse adzachita mantha;
adzalengeza ntchito za Mulungu
ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.
10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehova
ndi kubisala mwa Iye,
owongoka mtima onse atamande Iye!
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.