Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 7-10

Fuko la Isakara

Ana a Isakara anali awa:

Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi.

Ana a Tola ndi awa:

Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.

Mwana wa Uzi anali

Izirahiya.

Ana a Izirahiya anali:

Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja. Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri.

Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.

Fuko la Benjamini

Ana atatu a Benjamini anali awa:

Bela, Bekeri ndi Yediaeli.

Ana a Bela anali awa:

Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo.

Ana a Bekeri anali awa:

Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo.

10 Mwana wa Yediaeli anali

Bilihani.

Ana a Bilihani anali awa:

Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara. 11 Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.

12 Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri.

Fuko la Nafutali

13 Ana a Nafutali anali awa:

Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha.

Fuko la Manase

14 Ana a Manase anali awa:

Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi. 15 Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka.

Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.

16 Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu.

17 Mwana wa Ulamu anali

Bedani.

Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase. 18 Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila.

19 Ana a Semida anali:

Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu.

Fuko la Efereimu

20 Ana a Efereimu anali awa:

Sutela, Beredi,

Tahati, Eliada,

Tahati, 21 Zabadi,

Sutela.

Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo. 22 Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza. 23 Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake. 24 Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera.

25 Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu,

Tela, Tahani,

26 Ladani, Amihudi,

Elisama, 27 Nuni

ndi Yoswa.

28 Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake. 29 Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.

Fuko la Aseri

30 Ana a Aseri anali awa:

Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera.

31 Ana a Beriya anali awa:

Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti.

32 Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo.

33 Ana a Yafuleti anali awa:

Pasaki, Bimuhali ndi Asivati.

Awa anali ana a Yafuleti.

34 Ana a Someri anali awa:

Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu.

35 Ana a mʼbale wake Helemu anali awa:

Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali.

36 Ana a Zofa anali awa:

Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula, 37 Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera.

38 Ana a Yeteri anali awa:

Yefune, Pisipa ndi Ara.

39 Ana a Ula anali awa:

Ara, Hanieli ndi Riziya.

40 Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.

Adzukulu a Benjamini ndi Sauli

Benjamini anabereka Bela mwana wake woyamba,

wachiwiri Asibeli, wachitatu Ahara,

wachinayi Noha ndipo wachisanu Rafa.

Ana a Bela anali awa:

Adari, Gera, Abihudi, Abisuwa, Naamani, Ahowa, Gera, Sefufani ndi Hiramu.

Zidzukulu za Ehudi, zimene zinali atsogoleri a mabanja a amene amakhala ku Geba ndipo zinasamutsidwa kupita ku Manahati zinali izi:

Naamani, Ahiya ndi Gera, amene anawasamutsa ndipo anabereka Uza ndi Ahihudi.

Saharaimu anabereka ana ku Mowabu atalekana ndi akazi ake, Husimu ndi Baara. Mwa mkazi wake Hodesi anabereka Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu, 10 Yeusi, Sakiya ndi Mirima. Awa ndiye ana ake, atsogoleri a mabanja awo. 11 Mwa mkazi wake Husimu anabereka Abitubi ndi Elipaala.

12 Ana a Elipaala anali awa:

Eberi, Misamu, Semedi (amene anamanga mizinda ya Ono ndi Lodi ndi midzi yake yozungulira) 13 ndiponso Beriya ndi Sema, amene anali atsogoleri a mabanja a amene ankakhala ku Ayaloni ndipo anathamangitsa nzika za ku Gati.

14 Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, 15 Zebadiya, Aradi, Ederi, 16 Mikayeli, Isipa ndi Yoha anali ana a Beriya.

17 Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Heberi, 18 Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali ana a Elipaala.

19 Yakimu, Zikiri, Zabidi, 20 Elienai, Ziletai, Elieli, 21 Adaya, Beraya ndi Simirati anali ana a Simei.

22 Isipani, Eberi, Elieli, 23 Abidoni, Zikiri, Hanani, 24 Hananiya, Elamu, Anitotiya, 25 Ifideya ndi Penueli anali ana a Sasaki.

26 Samuserai, Sehariya, Ataliya, 27 Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali ana a Yerohamu.

28 Onsewa anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.

29 Yeiyeli amene amabereka Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni.

Dzina la mkazi wake linali Maaka, 30 ndipo mwana wake woyamba anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, 31 Gedori, Ahiyo, Zekeri 32 ndi Mikiloti, amene anabereka Simea. Iwowa ankakhalanso ku Yerusalemu ndi abale awo.

33 Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.

34 Mwana wa Yonatani anali

Meri-Baala, amene anabereka Mika.

35 Ana a Mika anali awa:

Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi.

36 Ahazi anabereka Yehoyada, Yehoyada anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimuri anabereka Moza. 37 Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Rafa, Eleasa ndi Azeli.

38 Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo mayina awo anali awa:

Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli.

39 Ana a Eseki mʼbale wake anali awa:

Mwana wake woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi ndipo wachitatu Elifeleti. 40 Ana a Ulamu anali asilikali olimba mtima amene amadziwa kugwiritsa ntchito uta. Iwo anali ndi ana ndi adzukulu ambiri ndipo onse analipo 150.

Onsewa anali adzukulu a Benjamini.

Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli.

Anthu a ku Yerusalemu

Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.

Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa:

Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda.

A banja la Siloni:

Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake.

A banja la Zera:

Yeueli.

Anthu ochokera ku Yuda analipo 690.

A fuko la Benjamini:

Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya;

Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya.

Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.

10 Ansembe:

Yedaya, Yehoyaribu; Yakini;

11 Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu;

12 Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri.

13 Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.

14 Alevi:

Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari; 15 Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu; 16 Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati.

17 Alonda a pa makomo:

Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu. 18 Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa: 19 Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova. 20 Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye. 21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano.

22 Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 23 Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti. 24 Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. 25 Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri. 26 Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu. 27 Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse.

28 Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa. 29 Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira. 30 Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo. 31 Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya. 32 Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo.

33 Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.

34 Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.

Mibado ya Sauli

35 Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni.

Dzina la akazi awo linali Maaka, 36 ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, 37 Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti. 38 Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu.

39 Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.

40 Mwana wa Yonatani anali

Meri-Baala, amene anabereka Mika.

41 Ana a Mika anali:

Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi.

42 Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza. 43 Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli.

44 Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa:

Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli.

Sauli Adzipha Yekha

10 Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza.

Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe, kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere ndi kudzandizunza ine.”

Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa. Motero Sauli ndi ana ake atatu anafa, pamodzi ndi banja lake lonse anafera limodzi.

Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.

Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa. Iwo anamuvula zovala zake, natenga mutu wake ndi zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. 10 Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba zopembedzera milungu yawo ndipo anapachika mutu wake mʼnyumba ya Dagoni.

11 Pamene anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, 12 anthu awo onse olimba mtima anapita kukatenga mitembo ya Sauli ndi ana ake ndipo anabwera nayo ku Yabesi. Anakwirira mafupa awo pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.

13 Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, 14 sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.