Chronological
43 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;
ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;
mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.
Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
woponderezedwa ndi mdani?
3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu
kuti zinditsogolere;
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,
kumalo kumene inu mumakhala.
4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.
Ndidzakutamandani ndi zeze,
Inu Mulungu wanga.
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?
Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu,
pakuti ndidzamutamandabe Iye,
Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.
44 Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu;
makolo athu atiwuza
zimene munachita mʼmasiku awo,
masiku akalekalewo.
2 Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena
ndi kudzala makolo athu;
Inu munakantha mitundu ya anthu,
koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
3 Sanalande dziko ndi lupanga lawo,
si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,
koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
pakuti munawakonda.
4 Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga
amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
5 Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu;
kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
6 Sindidalira uta wanga,
lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
7 koma Inu mumatigonjetsera adani athu,
mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
8 Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,
ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
9 Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa;
Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10 Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani
ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa
ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,
osapindulapo kanthu pa malondawo.
13 Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina,
chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14 Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina;
anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15 Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse
ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16 chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe,
chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
17 Zonsezi zinatichitikira
ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu
kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo;
mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19 Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe
ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
20 Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu
kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21 kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi,
pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22 Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse,
tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
23 Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona!
Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,
ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
25 Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi;
matupi athu amatirira pa dothi.
26 Imirirani ndi kutithandiza,
tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.
45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2 Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
3 Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu;
mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
4 Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso
mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo;
dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
5 Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu,
mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
49 Imvani izi anthu a mitundu yonse;
mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
2 anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,
olemera pamodzinso ndi osauka:
3 Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;
mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
4 Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,
ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.
5 Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,
pamene achinyengo oyipa andizungulira.
6 Iwo amene adalira kulemera kwawo
ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
7 Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake
kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
8 Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,
palibe malipiro amene angakwanire,
9 kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya
ndi kusapita ku manda.
10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;
opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka
ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,
malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,
ngakhale anatchula malo mayina awo.
12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,
adzafa ngati nyama.
13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,
ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula.
Sela
14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,
ndipo imfa idzawadya.
Olungama adzawalamulira mmawa;
matupi awo adzavunda mʼmanda,
kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;
ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.
16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,
pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,
ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,
ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,
amene sadzaonanso kuwala.
20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru
adzafa ngati nyama yakuthengo.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.
84 Malo anu okhalamo ndi okomadi,
Inu Yehova Wamphamvuzonse!
2 Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira
Mulungu wamoyo.
3 Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,
ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,
kumene amagonekako ana ake
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,
Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
4 Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;
nthawi zonse amakutamandani.
Sela
5 Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,
mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
6 Pamene akudutsa chigwa cha Baka,
amachisandutsa malo a akasupe;
mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
7 Iwo amanka nakulirakulira mphamvu
mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.
8 Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;
mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.
Sela
9 Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;
yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.
10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
iwo amene amayenda mwangwiro.
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,
wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
85 Yehova munakomera mtima dziko lanu;
munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
2 Munakhululukira mphulupulu za anthu anu
ndi kuphimba machimo awo onse.
Sela
3 Munayika pambali ukali wanu wonse
ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.
4 Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
5 Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
6 Kodi simudzatitsitsimutsanso,
kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
7 Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova,
ndipo tipatseni chipulumutso chanu.
8 Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;
Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,
koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
9 Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,
kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;
chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,
ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,
ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
13 Wolungama amapita patsogolo pake
ndi kukonza njira za mapazi ake.
Salimo la Ana a Kora.
87 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni
kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
3 Za ulemerero wako zimakambidwa,
Iwe mzinda wa Mulungu:
Sela
4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni
pakati pa iwo amene amandidziwa.
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,
ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”
5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,
“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,
ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:
“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”
Sela
7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.