Chronological
Mawu a Yobu
6 Tsono Yobu anayankha kuti,
2 “Achikhala mavuto anga anayezedwa,
ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo!
3 Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja;
nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula.
4 Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya,
thupi langa likumva ululu wa miviyo;
zoopsa za Mulungu zandizinga.
5 Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu,
nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
6 Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere,
nanga choyera cha dzira chimakoma?
7 Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe;
zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi.
8 “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha,
chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,
9 achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye,
kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!
10 Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi,
ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu
podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo.
11 “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo?
Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe?
12 Kodi ine ndili ndi mphamvu?
Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13 Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha,
nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine?
14 “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,
ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
15 Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga,
ngati mitsinje imene imathamanga.
16 Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja,
imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
17 koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe,
ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
18 Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi;
iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
19 Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi,
anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
20 Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi;
koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
21 Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza,
mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
22 Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake,
ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
23 ndilanditseni mʼdzanja la mdani,
ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
24 “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete;
ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
25 Ndithu, mawu owona ndi opweteka!
Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
26 Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena,
ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
27 Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye
ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
28 “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana.
Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
29 Fewani mtima, musachite zosalungama;
ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
30 Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga?
Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?
7 “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi?
Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
2 Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo,
kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
3 choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe,
ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
4 Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’
Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
5 Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera,
khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.
6 “Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu,
ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
7 Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya;
sindidzaonanso masiku achisangalalo.
8 Amene akundiona tsopano akundiona;
mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,
momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.
10 Iye sadzabweranso ku nyumba kwake
ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.
11 “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete;
ndidzayankhula mopsinjika mtima,
ndidzadandaula mowawidwa mtima.
12 Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja
kuti inu mundiyikire alonda?
13 Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga
ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
14 ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto
ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
15 kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa,
kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
16 Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse.
Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.
17 “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,
kuti muzisamala zochita zake,
18 kuti muzimusanthula mmawa uliwonse
ndi kumamuyesa nthawi yonse?
19 Kodi simudzaleka kumandizonda
kuti ndipezeko mpata wopumula?
20 Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu,
Inu wopenyetsetsa anthu?
Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu?
Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
21 Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga
ndi kundichotsera machimo anga?
Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda;
mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”
Mawu a Bilidadi
8 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2 “Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti?
Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.
3 Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama?
Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?
4 Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu,
Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.
5 Koma utayangʼana kwa Mulungu,
ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,
6 ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima
ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako
ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.
7 Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa
koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.
8 “Funsa kwa anthu amvulazakale
ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira
9 pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse,
ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.
10 Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera?
Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?
11 Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho?
Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?
12 Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula;
zimawuma msangamsanga kuposa bango.
13 Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu;
ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.
14 Kulimba mtima kwake kumafowoka;
zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.
15 Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka;
amawugwiritsitsa koma sulimba.
16 Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa,
nthambi zake zimatambalala pa munda wake;
17 mizu yake imayanga pa mulu wa miyala
ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.
18 Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo,
pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’
19 Ndithudi chomeracho chimafota,
ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.
20 “Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa
kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.
21 Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete
ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.
22 Adani ako adzachita manyazi,
ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”
Mawu a Yobu
9 Ndipo Yobu anayankha kuti,
2 “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona.
Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
3 Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye,
Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe.
4 Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka.
Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka?
5 Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa,
ndipo amawagubuduza ali wokwiya.
6 Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake
ndipo amanjenjemeretsa mizati yake.
7 Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala;
Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.
8 Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba
ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja.
9 Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana,
nsangwe ndi kumpotosimpita.
10 Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,
zodabwitsa zimene sizingawerengeke.
11 Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona;
akadutsa, sindingathe kumuzindikira.
12 Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa?
Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’
13 Mulungu sabweza mkwiyo wake;
ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake.
14 “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji?
Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye?
15 Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe;
ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga.
16 Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera,
sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo.
17 Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho,
ndipo akanandipweteka popanda chifukwa.
18 Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso
koma akanandichulukitsira zowawa.
19 Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi!
Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu?
20 Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa;
ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa.
21 “Ngakhale ine ndili wosalakwa,
sindidziyenereza ndekha;
moyo wanga ndimawupeputsa.
22 Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti,
‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’
23 Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi,
Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo.
24 Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa
Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo.
Ngati si Iyeyo, nanga ndani?
25 “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro;
masikuwo amapita ine osaonapo zabwino.
26 Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja,
ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye.
27 Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga,
ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’
28 ndikuopabe mavuto anga onse,
popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa.
29 Popeza ndapezeka kale wolakwa
ndivutikirenji popanda phindu?
30 Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri
ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo,
31 mutha kundiponyabe pa dzala,
kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa.
32 “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha,
sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu.
33 Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu,
kuti atibweretse ife tonse pamodzi,
34 munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine
kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha!
35 Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo,
koma monga zililimu, sindingathe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.