Chronological
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.
Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
Chisomo ndi mtendere kwa inu.
Kuyamikira Chikhulupiriro cha Atesalonika
2 Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. 3 Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.
4 Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani, 5 chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. 6 Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. 7 Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya. 8 Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu, 9 pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10 Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.
Utumiki wa Paulo ku Atesalonika
2 Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa. 2 Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. 3 Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. 4 Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. 5 Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. 6 Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. 7 Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu.
Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, 8 moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu. 9 Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.
10 Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira. 11 Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake, 12 kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.
13 Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. 14 Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda, 15 amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse 16 ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.
Paulo Afunitsitsa Kuonanso Atesalonika
17 Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni. 18 Pakuti ife tinafuna kubweranso kwa inu, makamaka ine Paulo, ndinayesa kangapo koma Satana anatiletsa. 19 Nanga chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu kapena chaufumu chimene ife tidzanyadira pamaso pa Ambuye athu Yesu Khristu pamene abwere ndi chiyani? Kodi si inu? 20 Indedi, inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe.
3 Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. 2 Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, 3 ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. 4 Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. 5 Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo
6 Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. 7 Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. 8 Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. 9 Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.
11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.
Moyo Wokondweretsa Mulungu
4 Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. 2 Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.
3 Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; 4 aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, 5 osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. 6 Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. 7 Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. 8 Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.
9 Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. 10 Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.
11 Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. 12 Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.
Kubweranso kwa Ambuye
13 Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. 14 Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. 15 Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. 16 Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17 Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. 18 Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.
Tsiku la Ambuye
5 Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, 2 chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. 3 Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
4 Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. 5 Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. 6 Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. 7 Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. 8 Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. 9 Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 10 Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. 11 Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
Malangizo Otsiriza
12 Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. 13 Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. 14 Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20 Musanyoze mawu a uneneri. 21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.
23 Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. 24 Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.
25 Abale, mutipempherere. 26 Perekani moni wachikondi kwa onse. 27 Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.
28 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.
Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
2 Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
Kuyamika ndi Pemphero
3 Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe. 4 Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo.
5 Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira. 6 Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo 7 ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. 8 Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. 9 Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake 10 pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.
11 Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro. 12 Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Kubwera kwa Munthu Woyipitsitsa
2 Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani 2 kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale. 3 Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo. 4 Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi? 6 Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera. 7 Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe. 8 Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake. 9 Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo. 10 Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe. 11 Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza. 12 Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.
Imani Mwamphamvu
13 Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi. 14 Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. 15 Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.
16 Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, 17 akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.
Tipempherereni
3 Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. 2 Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. 4 Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. 5 Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.
Awachenjeza za Kusagwira Ntchito
6 Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7 Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8 ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9 Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”
11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
14 Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15 Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.
Malonje Otsiriza
16 Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.
18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.