Chronological
23 Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato. 2 Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3 Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4 Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5 Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6 Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya. 7 Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8 Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa. 9 Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe. 10 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri. 11 Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato. 12 Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13 Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu, 14 ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu. 15 Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe. 16 Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.” 17 (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18 Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!” 19 (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20 Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo. 21 Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22 Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23 Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira. 24 Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo. 25 Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
Kupachikidwa kwa Yesu
26 Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu. 27 Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira. 28 Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu. 29 Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’ 30 Kenaka,
“adzawuza mapiri kuti tigwereni ife;
zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32 Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa. 33 Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. 34 Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36 Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, 37 ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38 Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40 Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? 41 Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42 Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
Imfa ya Yesu
44 Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi, 45 pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati. 46 Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47 Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.” 48 Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka. 49 Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
50 Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama. 51 Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu. 52 Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu. 53 Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo. 54 Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55 Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira. 56 Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.
Amugwira Yesu
18 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.
2 Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. 3 Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
4 Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”
5 Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.”
Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo). 6 Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.
7 Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?”
Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”
8 Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.” 9 Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”
10 Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
11 Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”
Amutengera Yesu kwa Anasi
12 Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. 13 Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho. 14 Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu.
Petro Akana Yesu Koyamba
15 Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe 16 koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro.
17 Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?”
Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
18 Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.
Mkulu wa Ansembe Amufunsa Yesu
19 Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake.
20 Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri. 21 Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.”
22 Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?”
23 Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?” 24 Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.
Petro Akana Yesu Kachiwiri ndi Kachitatu
25 Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?”
Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
26 Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?” 27 Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira.
Yesu ku Bwalo la Pilato
28 Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska. 29 Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?”
30 Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.”
31 Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.”
Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.” 32 Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe.
33 Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?”
34 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?”
35 Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”
36 Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”
37 Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!”
Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”
38 Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye. 39 Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’ ”
40 Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.
Yesu Aweruzidwa kuti Aphedwe
19 Kenaka Pilato anatenga Yesu namukwapula mwankhanza. 2 Asilikali analuka nkhata yaminga ndi kumuveka pamutu pake. Kenaka anamuveka mkanjo wapepo 3 ndipo ankapita kwa Iye mobwerezabwereza ndi kumanena kuti, “Moni mfumu ya Ayuda?” Ndipo amamumenya makofi.
4 Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, “Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.” 5 Pamenepo Yesu anatuluka atavala nkhata yaminga ndi mkanjo wapepo ndipo Pilato anawawuza kuti, “Nayu munthu uja!”
6 Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
7 Ayuda anayimirira nati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo molingana ndi lamulolo, Iyeyu ayenera kuphedwa chifukwa akudzitcha kuti ndi Mwana wa Mulungu.”
8 Pilato atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri, 9 ndipo anabwereranso mʼnyumba yaufumu. Iye anafunsa Yesu kuti, “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanayankhe. 10 Pilato anati, “Kodi ukukana kundiyankhula ine? Kodi sukuzindikira kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula ndiponso mphamvu yokupachika?”
11 Yesu anayankha kuti, “Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri.”
12 Kuyambira pamenepo Pilato anayesa kuti amumasule Yesu, koma Ayuda anapitirira kufuwula kuti, “Ngati mumumasula munthuyu kuti apite, inu si bwenzi la Kaisara.”
13 Pilato atamva zimenezi, iye anamutulutsa Yesu kunja ndi kukhala pansi pa mpando wa woweruza pamalo otchedwa Mwala Wowaka (umene pa Chiaramaiki ndi Gabata). 14 Linali tsiku lokonzekera Sabata la Paska ndipo nthawi inali ora lachisanu ndi chimodzi masana.
Pilato anati kwa Ayuda, “Nayi mfumu yanu.”
15 Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!”
Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?”
Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.”
16 Pomaliza Pilato anamupereka kwa iwo kuti akapachikidwe. Choncho asilikali anamutenga Yesu.
Kupachikidwa kwa Yesu
17 Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa “Malo a Bade” (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota). 18 Pamenepo iwo anamupachika Iye pamodzi ndi anthu ena awiri, mmodzi mbali ina ndi wina mbali inanso ndipo Yesu pakati.
19 Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda. 20 Ayuda ambiri anawerenga chikwangwanichi, pakuti pamalo pamene Yesu anapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda ndipo chikwangwanicho chinalembedwa mu Chiaramaiki, Chilatini ndi Chigriki. 21 Kenaka mkulu wa ansembe wa Ayuda anakadandaula kwa Pilato nati, “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti munthuyu amadzitcha kuti ndi mfumu ya Ayuda.”
22 Pilato anayankha kuti, “Chimene ine ndalemba, ndalemba.”
23 Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.
24 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.”
Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,
“Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo
ndi kuchita maere pa zovala zangazo.”
Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.
25 Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. 26 Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, “Amayi nayu mwana wanu.” 27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, “Nawa amayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.
Imfa ya Yesu
28 Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.” 29 Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. 30 Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.
31 Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. 32 Chifukwa chake asilikali anabwera ndi kuthyola miyendo ya munthu oyamba amene anapachikidwa ndi Yesu ndipo kenaka ya winayo. 33 Koma atafika pa Yesu ndi kupeza kuti anali atamwalira kale, iwo sanathyole miyendo yake. 34 Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi mkondo mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi. 35 Munthu amene anaona izi wapereka umboni ndipo umboni wake ndi woona. Iye akudziwa kuti akunena choonadi kuti inunso mukhulupirire. 36 Zinthu izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe: “Palibe limodzi la mafupa limene lidzathyoledwa,” 37 ndi monga lemba linanso linena, “Iwo adzayangʼana Iye amene iwo anamubaya.”
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
38 Kenaka, Yosefe wa ku Arimateyu anakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Tsono Yosefe anali wophunzira wa Yesu koma mobisa chifukwa iye ankaopa Ayuda. Atalandira chilolezo kwa Pilato, anakatsitsa mtembo wa Yesu. 39 Nekodimo, munthu amene poyamba pake anabwera kwa Yesu usiku, anatenga mafuta osakaniza ndi mure ndi aloe wolemera pafupifupi makilogalamu 32. 40 Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu nawukulunga pamodzi ndi zonunkhiritsa mu nsalu za mtundu woyera monga mwa mwambo wa maliro wa Ayuda. 41 Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense. 42 Chifukwa linali Tsiku la Ayuda Lokonzekera ndi kuti mandawo anali pafupipo, iwo anayika Yesu mʼmenemo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.