Chronological
Adani Apitiriza Kutsutsa ndi Kuopseza Nehemiya
6 Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata. 2 Sanibalati ndi Gesemu, ananditumizira uthenga uwu: “Bwerani tidzakumane pa mudzi wina ku chigwa cha Ono.”
Koma iwo anakonzekera kuti akandichite chiwembu kumeneko. 3 Choncho ine ndinatuma amithenga ndi yankho ili: “Ine ndikugwira ntchito yayikulu kuno ndipo sindingathe kubwera kumeneko. Kodi ntchito iyime pofuna kuti ndibwere kumeneko?” 4 Ananditumizira uthenga umodzimodzi omwewu kanayi ndipo ndinawayankha chimodzimodzi.
5 Tsono kachisanu, Sanibalati anatumiza wantchito wake ndi kalata yosamata. 6 Mu kalatamo munali mawu akuti,
“Pali mphekesera pakati pa mitundu ya anthu, ndiponso Gesemu akunena zomwezo kuti inu ndi Ayuda onse mufuna kuwukira boma. Nʼchifukwa chake mukumanga khoma. Mphekeserazo zikutinso inu mukufuna kudzakhala mfumu yawo. 7 Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.”
8 Ine ndinatumiza yankho ili: “Pa zimene mukunenazo, palibe chimene chinachitikapo. Inu mukungozipeka mʼmutu mwanu.”
9 Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.”
Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.”
10 Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.”
11 Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!” 12 Ndinazindikira kuti Mulungu sanamutume koma kuti anayankhula mawu oloserawa motsutsana nane chifukwa Tobiya ndi Sanibalati anamulemba ntchitoyi. 13 Iye analembedwa ntchitoyi ndi cholinga choti ine ndichite mantha, ndithawe. Ndikanatero ndiye kuti ndikanachimwira Yehova ndiponso iwowo akanandiyipitsira mbiri yanga ndi kumandinyoza.
14 Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobiya ndi Sanibalati chifukwa cha zimene achita. Kumbukiraninso mneneri wamkazi Nowadiya ndi aneneri amene akhala akufuna kundiopseza.”
Kutsiriza kwa Khoma
15 Ndipo khoma linatsirizidwa kumanga pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli. Linamangidwa pa masiku okwana 52. 16 Adani athu onse atamva izi, mitundu yonse ya anthu yozungulira inachita mantha ndi kuchita manyazi. Iwo anazindikira kuti ntchitoyo inachitika ndi thandizo la Mulungu wathu.
17 Komanso masiku amenewo anthu olemekezeka a ku Yuda ankalemberana naye makalata ambiri ndi Tobiyayo, 18 pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya. 19 Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza.
7 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3 Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo
4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:
6 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 7 Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.
Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:
8 Zidzukulu za Parosi | 2,172 |
9 Zidzukulu za Sefatiya | 372 |
10 Zidzukulu za Ara | 652 |
11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) | 2,818 |
12 Zidzukulu za Elamu | 1,254 |
13 Zidzukulu za Zatu | 845 |
14 Zidzukulu za Zakai | 760 |
15 Zidzukulu za Binuyi | 648 |
16 Zidzukulu za Bebai | 628 |
17 Zidzukulu za Azigadi | 2,322 |
18 Zidzukulu za Adonikamu | 667 |
19 Zidzukulu za Abigivai | 2,067 |
20 Zidzukulu za Adini | 655 |
21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) | 98 |
22 Zidzukulu za Hasumu | 328 |
23 Zidzukulu za Bezayi | 324 |
24 Zidzukulu za Harifu | 112 |
25 Zidzukulu za Gibiyoni | 95. |
26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa | 188 |
27 Anthu a ku Anatoti | 128 |
28 Anthu a ku Beti-Azimaveti | 42 |
29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti | 743 |
30 Anthu a ku Rama ndi Geba | 621 |
31 Anthu a ku Mikimasi | 122 |
32 Anthu a ku Beteli ndi Ai | 123 |
33 Anthu a ku Nebo winayo | 52 |
34 Ana a Elamu wina | 1,254 |
35 Zidzukulu za Harimu | 320 |
36 Zidzukulu za Yeriko | 345 |
37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono | 721 |
38 Zidzukulu za Senaya | 3,930. |
39 Ansembe anali awa:
A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) | 973 |
40 Zidzukulu za Imeri | 1,052 |
41 Zidzukulu za Pasi-Huri | 1,247 |
42 Zidzukulu za Harimu | 1,017. |
43 Alevi anali awa:
A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya | 74. |
44 Anthu oyimba:
Zidzukulu za Asafu | 148. |
45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za | |
Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai | 138. |
46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za |
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, |
47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni |
48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi, |
49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, |
50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda, |
51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya, |
52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu, |
53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, |
54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, |
55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema |
56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa. |
57 Zidzukulu za antchito a Solomoni:
Zidzukulu za | |
Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida | |
58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, | |
59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu | |
zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni. | |
60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo | 392. |
61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
62 Zidzukulu za | |
Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda | 642. |
63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:
zidzukulu za
Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.
66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.
70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.
Ezara Awerenga Malamulo
Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.