Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 44-48

Israeli Wosankhidwa wa Yehova

44 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Israeli, amene ndinakusankha.
Yehova
    amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
    ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Yesuruni, amene ndinakusankha.
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
    ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
    ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
    ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’
    wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;
winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’
    ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.

Yehova, Osati Mafano

“Yehova Mfumu
    ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:
Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;
    palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.
    Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe
zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,
    ndi ziti zimene zidzachitike;
    inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
Musanjenjemere, musachite mantha.
    Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?
Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
    Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”

Onse amene amapanga mafano ngachabe,
    ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.
Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;
    ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
10 Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,
    limene silingamupindulire?
11 Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;
    amisiri a mafano ndi anthu chabe.
Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;
    onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.

12 Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo
    ndipo amachiyika pa makala amoto;
ndi dzanja lake lamphamvu
    amachisula pochimenya ndi nyundo.
Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;
    iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
13 Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe
    ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera;
amasema bwinobwino ndi chipangizo chake
    ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake.
Amachipanga ngati munthu,
    munthu wake wokongola
    kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
14 Amagwetsa mitengo ya mkungudza,
    mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu
nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,
    ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
15 Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;
    nthambi zina amasonkhera moto wowotha,
    amakolezera moto wophikira buledi
ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;
    iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
16 Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto
    wowotcherapo nyama imene
    amadya, nakhuta.
Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,
    “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
17 Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;
    amaligwadira ndi kulipembedza.
Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,
    “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
18 Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;
    maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,
    ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
19 Palibe amene amayima nʼkulingalira.
    Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,
chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;
    pa makala ake ndinaphikira buledi,
    ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.
Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.
    Kodi ndidzagwadira mtengo?
20 Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;
    motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,
    “Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”

21 Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi
    popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.
Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;
    iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
22 Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,
    ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.
Bwerera kwa Ine,
    popeza ndakupulumutsa.”

23 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;
    fuwula, iwe dziko lapansi.
Imbani nyimbo, inu mapiri,
    inu nkhalango ndi mitengo yonse,
chifukwa Yehova wawombola Yakobo,
    waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.

Anthu Adzakhalanso mu Yerusalemu

24 Yehova Mpulumutsi wanu, amene
    anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti:

“Ine ndine Yehova,
amene anapanga zinthu zonse,
ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,
ndinayala ndekha dziko lapansi.
25 Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,
    ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.
Ndimasokoneza anthu a nzeru,
    ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
26 Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake
    ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake.

“Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.
    Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.
    Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
27 Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’
    ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
28 Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’
    ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;
    iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’
    ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”
45 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake
    Koresi amene anamugwira dzanja lamanja
kuti agonjetse mitundu ya anthu
    ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,
ndi kutsekula zitseko
    kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
Ine ndidzayenda patsogolo pako,
    ndi kusalaza mapiri;
ndidzaphwanya zitseko za mkuwa
    ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,
    katundu wa pamalo obisika,
kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova
    Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,
    chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,
Ine ndakuyitana pokutchula dzina
    ndipo ndakupatsa dzina laulemu
    ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;
    kupatula Ine palibenso Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu,
    ngakhale sukundidziwa Ine,
kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo
    anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Ine ndine Yehova,
    ndipo palibenso wina.
Ndimalenga kuwala ndi mdima,
    ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;
    ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.

“Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;
    mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.
Dziko lapansi litsekuke,
    ndipo chipulumutso chiphuke kuti
chilungamo chimereponso;
    Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.

“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
    ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
    ‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
    ‘Ulibe luso?’
10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,
    ‘Kodi munabereka chiyani?’
Kapena amayi ake kuti,
    ‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’

11 “Yehova
    Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,
zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:
    Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,
    kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansi
    ndikulenga munthu kuti akhalemo.
Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;
    ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:
    ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.
Iye adzamanganso mzinda wanga
    ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,
    akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

14 Yehova akuti,

“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.
    Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba
adzabwera kwa inu
    ndipo adzakhala anthu anu;
iwo adzidzakutsatani pambuyo panu
    ali mʼmaunyolo.
Adzakugwadirani
    ndi kukupemphani, ponena kuti,
‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;
    palibenso mulungu wina.’ ”

15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika
    amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.
    Adzakhala osokonezeka maganizo.
17 Koma Yehova adzapulumutsa Israeli
    ndi chipulumutso chamuyaya;
simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka
    mpaka kalekale.

18 Yehova
analenga zinthu zakumwamba,
    Iye ndiye Mulungu;
amene akulenga dziko lapansi,
    ndi kulikhazikitsa,
sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,
    koma analipanga kuti anthu akhalemo.
Iyeyu akunena kuti:
Ine ndine Yehova,
    ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi,
    pamalo ena a mdima;
Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,
    “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”
Ine Yehova, ndimayankhula zoona;
    ndikunena zolungama.

20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;
    yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.
Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,
    amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21 Fotokozani mlandu wanu,
    mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?
    Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?
Kodi si Ineyo Yehova?
    Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,
Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,
    palibenso wina kupatula Ine.

22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,
    inu anthu onse a pa dziko lapansi,
    pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
23 Ndalumbira ndekha,
    pakamwa panga patulutsa mawu owona,
    mawu amene sadzasinthika konse akuti,
bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;
    anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
24 Iwo adzanene kwa Ine kuti,
    ‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”
Onse amene anamuwukira Iye
    adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli
    zidzapambana ndi kupeza ulemerero.

Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake

46 Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;
    nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.
Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.
    Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;
    sizikutha kupulumutsa katunduyo,
    izo zomwe zikupita ku ukapolo.
Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,
    inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,
Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,
    ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
    ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
    ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.

“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?
    Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo
    ndipo amayeza siliva pa masikelo;
amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,
    kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;
    amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.
    Singathe kusuntha pamalo pakepo.
Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;
    kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.

“Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,
    Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;
    chifukwa Ine ndine Mulungu
    ndipo palibe wina ofanana nane.
10 Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.
    Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.
Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.
    Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
11 Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.
    Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.
Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;
    zimene ndafuna ndidzazichitadi.
12 Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,
    inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13 Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;
    sichili kutali.
    Tsikulo layandikira
ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani
    ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.

Kugwa kwa Babuloni

47 “Tsika, ndi kukhala pa fumbi,
    iwe namwali, Babuloni;
khala pansi wopanda mpando waufumu,
    iwe namwali, Kaldeya
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera
    kumugwira mosamala.
Tenga mphero ndipo upere ufa;
    chotsa nsalu yako yophimba nkhope
kwinya chovala chako mpaka ntchafu
    ndipo woloka mitsinje.
Maliseche ako adzakhala poyera
    ndipo udzachita manyazi.
Ndidzabwezera chilango
    ndipo palibe amene adzandiletse.”

Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,
    dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

“Khala chete, ndipo lowa mu mdima,
    iwe namwali, Kaldeya;
chifukwa sadzakutchulanso
    mfumukazi ya maufumu.
Ndinawakwiyira anthu anga,
    osawasamalanso.
Ndinawapereka manja mwako,
    ndipo iwe sunawachitire chifundo.
Iwe unachitira nkhanza
    ngakhale nkhalamba.
Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse
    ngati mfumukazi.’
Koma sunaganizire zinthu izi
    kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.

“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,
    amene ukukhala mosatekesekawe,
umaganiza mu mtima mwako kuti,
    ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,
    ndipo ana anga sadzamwalira.’
Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,
    zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:
    ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu
    ngakhale ali ndi amatsenga ambiri
    ndi mawula amphamvu.
10 Iwe unkadalira kuyipa kwako
    ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,
    choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,
    ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11 Ngozi yayikulu idzakugwera
    ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.
Mavuto adzakugwera
    ndipo sudzatha kuwachotsa;
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa
    chidzakugwera mwadzidzidzi.

12 “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,
    pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,
    wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.
Mwina udzatha kupambana
    kapena kuopsezera nazo adani ako.
13 Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!
    Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi
    zimene ziti zidzakuchitikire.
14 Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;
    adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa okha
    ku mphamvu ya malawi a moto.
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;
    kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15 Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,
    anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito
    ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onse adzamwazika ndi mantha,
    sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”

Israeli ndi Nkhutukumve

48 “Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,
    inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,
    ndinu a fuko la Yuda,
inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,
    ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,
    ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika
    ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli,
    amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale,
    zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza;
    tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve
    wa nkhongo gwaa,
    wa mutu wowuma.
Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe;
    zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe
kuti unganene kuti,
    ‘Fano langa ndilo lachita zimenezi,
    kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
Inu munamva zinthu zimenezi.
    Kodi inu simungazivomereze?

“Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano
    zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale;
    munali musanazimve mpaka lero lino.
Choncho inu simunganene kuti,
    ‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa;
    makutu anu sanali otsekuka.
Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti
    chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.
    Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze.
    Sindidzakuwonongani kotheratu.
10 Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva;
    ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
11 Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.
    Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?
    Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.

Kumasulidwa kwa Israeli

12 “Tamvera Ine, iwe Yakobo,
    Israeli, amene ndinakuyitana:
Mulungu uja Woyamba
    ndi Wotsiriza ndine.
13 Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi,
    dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga.
Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba
    ndi dziko lapansi.

14 “Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:
    Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?
Wokondedwa wa Yehova uja adzachita
    zomwe Iye anakonzera Babuloni;
    dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
15 Ine, Inetu, ndayankhula;
    ndi kumuyitana
ndidzamubweretsa ndine
    ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.

16 “Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi:

“Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa;
    pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.”

Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake
    ndi kundituma.

17 Yehova, Mpulumutsi wanu,
    Woyerayo wa Israeli akuti,
“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,
    ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
18 Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,
    bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,
    ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
19 Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,
    ana ako akanachuluka ngati fumbi;
dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga
    ndipo silikanafafanizidwa konse.”

20 Tulukani mʼdziko la Babuloni!
    Thawani dziko la Kaldeya!
Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo
    ndipo muzilalikire
mpaka kumathero a dziko lapansi;
    muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
21 Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;
    anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;
anangʼamba thanthwelo ndipo
    munatuluka madzi.

22 “Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.