Chronological
Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu
40 Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,
akutero Mulungu wanu.
2 Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu
ndipo muwawuzitse
kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,
tchimo lawo lakhululukidwa.
Ndawalanga mokwanira
chifukwa cha machimo awo onse.
3 Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,
“Konzani njira ya Yehova
mʼchipululu;
wongolani njira zake;
msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
4 Chigwa chilichonse achidzaze.
Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;
Dziko lokumbikakumbika alisalaze,
malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
5 Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,
ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,
pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
6 Wina ananena kuti, “Lengeza.”
Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?
“Pakuti anthu onse ali ngati udzu
ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
7 Udzu umanyala ndipo maluwa amafota
chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”
Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
8 Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,
koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
9 Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,
kwera pa phiri lalitali.
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,
fuwula kwambiri,
kweza mawu, usachite mantha;
uza mizinda ya ku Yuda kuti,
“Mulungu wanu akubwera!”
10 Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,
ndipo dzanja lake likulamulira,
taonani akubwera ndi mphotho yake
watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
11 Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:
Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake
ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake
ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
12 Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,
kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?
Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,
kapena kuyeza kulemera kwa
mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
13 Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova
kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
14 Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,
kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?
Iye anapempha nzeru kwa yani
ndi njira ya kumvetsa zinthu?
15 Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.
Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;
mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
16 Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,
ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
17 Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;
Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu
ndi cha chabechabe.
18 Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?
Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19 Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga
ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide
naliveka mkanda wasiliva.
20 Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere
amasankha mtengo umene sudzawola,
nafunafuna mʼmisiri waluso woti
amupangire fano limene silingasunthike.
21 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?
Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
22 Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,
Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.
Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,
nayikunga ngati tenti yokhalamo.
23 Amatsitsa pansi mafumu amphamvu
nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
24 Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene
kapena kufesedwa chapompano,
ndi kungoyamba kuzika mizu kumene
ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa
ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
25 Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?
Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26 Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.
Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?
Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,
nayitana iliyonse ndi dzina lake.
Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,
palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
27 Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena
ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,
“Yehova sakudziwa mavuto anga,
Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
28 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,
ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.
Iye sadzatopa kapena kufowoka
ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
29 Iye amalimbitsa ofowoka
ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
30 Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,
ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
31 koma iwo amene amakhulupirira Yehova
adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
adzathamanga koma sadzalefuka,
adzayenda koma sadzatopa konse.
Mulungu Thandizo la Israeli
41 “Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja!
Alekeni ayandikire ndi kuyankhula;
tiyeni tikhale pamodzi
kuti atiweruze.
2 “Ndani anadzutsa wochokera kummawa
uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita?
Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake
ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa
ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi
nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
3 Amawalondola namayenda mosavutika,
mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
4 Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,
si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?
Ine Yehova, ndine chiyambi
ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
5 Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;
anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.
Akuyandikira pafupi, akubwera;
6 aliyense akuthandiza mnzake
ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
7 Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,
ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo
amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.
Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”
Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
8 “Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,
Yakobo amene ndakusankha,
Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
9 Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,
ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.
Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’
Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
10 Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;
usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.
Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,
ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
11 “Onse amene akupsera mtima
adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa;
onse amene akukangana nawe
sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
12 Udzafunafuna adani ako,
koma sadzapezeka.
Iwo amene akuchita nawe nkhondo
sadzakhalanso kanthu.
13 Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
ndidzakuthandiza.
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15 “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu
chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.
Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,
ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16 Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso
adzamwazika ndi kamvuluvulu.
Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,
ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
17 “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,
koma sakuwapeza;
ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.
Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;
Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18 Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,
ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.
Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi
ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19 Mʼchipululu ndidzameretsa
mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.
Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo
ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20 kuti anthu aone ndi kudziwa;
inde, alingalire ndi kumvetsa,
kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;
kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
21 “Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’
Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
22 Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze
zomwe zidzachitike mʼtsogolo.
Tifotokozereni zinthu zamakedzana
tiziganizire
ndi kudziwa zotsatira zake.
Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
23 tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani,
ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu.
Chitani chinthu chabwino kapena choyipa,
ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
24 Koma inu sindinu kanthu
ndipo zochita zanu nʼzopandapake;
amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
25 “Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera,
munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana.
Amapondaponda olamulira ngati matope,
ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
26 Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe,
kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’
Palibe amene ananena,
palibe analengeza zimenezi,
palibe anamva mawu anu.
27 Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’
Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
28 Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe,
palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu,
palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
29 Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo!
Zochita zawo si kanthu konse;
mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.
Mtumiki wa Yehova
42 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,
amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.
Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,
kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
3 Bango lophwanyika sadzalithyola,
ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.
Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
4 sadzafowoka kapena kukhumudwa
mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,
ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
5 Yehova Mulungu
amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,
amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,
amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,
ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;
ndikugwira dzanja ndipo
ndidzakuteteza.
Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu
ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
7 Udzatsekula maso a anthu osaona,
udzamasula anthu a mʼndende
ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!
Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense
kapena matamando anga kwa mafano.
9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,
ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;
zinthuzo zisanaonekere
Ine ndakudziwitsani.”
Nyimbo Yotamanda Yehova
10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi,
inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo.
Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.
11 Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo;
midzi ya Akedara ikondwere.
Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe;
afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.
12 Atamande Yehova
ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.
13 Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu,
adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo;
akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo
ndipo adzagonjetsa adani ake.
14 Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali,
ndakhala ndili phee osachita kanthu.
Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira,
ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
15 Ndidzawononga mapiri ndi zitunda
ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse;
ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba
ndipo ndidzawumitsa maiwe.
16 Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe,
ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo;
ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala
ndipo ndidzasalaza malo osalala.
Zimenezi ndizo ndidzachite;
sindidzawataya.
17 Koma onse amene amadalira mafano
amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’
ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
Aisraeli Alephera Kuphunzira
18 “Imvani, agonthi inu;
yangʼanani osaona inu, kuti muone! 19 Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?
Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?
Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,
kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;
makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
21 Chinamukomera Yehova
chifukwa cha chilungamo chake,
kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.
22 Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo,
onsewa anawakola mʼmaenje
kapena akuwabisa mʼndende.
Tsono asanduka chofunkha
popanda wina wowapulumutsa
kapena kunena kuti,
“Abwezeni kwawo.”
23 Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi
kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?
24 Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha,
ndi Israeli kwa anthu akuba?
Kodi si Yehova,
amene ife tamuchimwirayu?
Pakuti sanathe kutsatira njira zake;
ndipo sanamvere malangizo ake.
25 Motero anawakwiyira kwambiri,
nawavutitsa ndi nkhondo.
Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse;
motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.
Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli
43 Koma tsopano, Yehova
amene anakulenga, iwe Yakobo,
amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,
“Usaope, pakuti ndakuwombola;
Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
2 Pamene ukuwoloka nyanja,
ndidzakhala nawe;
ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,
sidzakukokolola.
Pamene ukudutsa pa moto,
sudzapsa;
lawi la moto silidzakutentha.
3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,
Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.
Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,
ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,
ndipo chifukwa ndimakukonda,
ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,
ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;
ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,
ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’
ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’
Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,
ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
7 onsewo amadziwika ndi dzina langa;
ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,
ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
8 Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,
anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
9 Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,
anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.
Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?
Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?
Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,
kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
10 Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,
ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,
kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.
Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,
ngakhale pambuyo panga
sipadzakhalaponso wina.”
11 Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,
ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
12 Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;
ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.
Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
13 “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.
Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,
ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
Chifundo cha Mulungu ndi Kusakhulupirika kwa Israeli
14 Yehova akuti,
Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,
“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni
ndi kukupulumutsani.
Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,
Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
16 Yehova
anapanga njira pa nyanja,
anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
17 Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,
gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,
ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso
anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
18 “Iwalani zinthu zakale;
ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
19 Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!
Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?
Ine ndikulambula msewu mʼchipululu
ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
20 Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi
zinandilemekeza.
Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma
kuti ndiwapatse madzi anthu anga
osankhidwa.
21 Anthu amene ndinadziwumbira ndekha
kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
22 “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,
munatopa nane, Inu Aisraeli.
23 Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,
kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.
Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya
kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
24 Simunandigulire bango lonunkhira
kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.
Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu
ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
25 “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza
zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
26 Mundikumbutse zakale,
ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;
fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
27 Kholo lanu loyamba linachimwa;
ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
28 Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,
ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe
ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.